1 Mbiri 16 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 16:1-43

1Iwo anabwera nalo Bokosi la Mulungu ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Mulungu. 2Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova. 3Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma.

4Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli. 5Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga, 6ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu.

Nyimbo Yotamanda ya Davide

7Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova:

8Yamikani Yehova, itanani dzina lake;

lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.

9Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando;

nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa.

10Nyadirani dzina lake loyera;

ikondwere mitima ya iwo akufunafuna Yehova.

11Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;

funafunani nkhope yake nthawi zonse.

12Kumbukirani ntchito zodabwitsa wazichita,

zozizwitsa zake, ndi kuweruza kwa mʼkamwa mwake,

13inu zidzukulu za Israeli mtumiki wake,

inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.

14Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;

chiweruzo chake chili pa dziko lonse lapansi.

15Iye amakumbukira pangano lake nthawi zonse,

mawu amene Iye analamula, kwa mibado miyandamiyanda,

16pangano limene anachita ndi Abrahamu,

lonjezo limene analumbira kwa Isake.

17Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga lamulo,

kwa Israeli monga pangano lamuyaya.

18“Kwa iwe, ine ndidzapereka dziko la Kanaani

monga cholowa chimene udzachilandira.”

19Ali anthu owerengeka,

ochepa ndithu, komanso alendo mʼdzikomo,

20iwo anayendayenda kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,

ku ufumu wina kupita ku ufumu wina.

21Iye sanalole munthu aliyense kuti awapondereze;

chifukwa cha iwo, Iye anadzudzula mafumu:

22“Musakhudze odzozedwa anga;

musawachitire choyipa aneneri anga.”

23Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi;

lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

24Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse,

ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse.

25Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda;

Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse.

26Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake,

koma Yehova analenga kumwamba.

27Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake;

mphamvu ndi chimwemwe zili pa malo pokhala Iye.

28Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina,

perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu,

29perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake.

Bweretsani chopereka ndipo mufike pamaso pake;

pembedzani Yehova mu ulemerero wachiyero chake.

30Njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi!

Dziko linakhazikika kolimba; silingasunthidwe.

31Zakumwamba zisangalale, dziko lapansi likondwere;

anene anthu a mitundu ina, “Yehova ndi mfumu!”

32Nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;

minda ikondwere, ndi zonse zili mʼmenemo!

33Ndipo mitengo ya mʼnkhalango idzayimba,

idzayimba chifukwa cha chimwemwe pamaso pa Yehova,

pakuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi.

34Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino;

chikondi chake chikhala mpaka muyaya.

35Fuwulani kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu,

mutisonkhanitse ndipo mutipulumutse kwa anthu a mitundu ina,

kuti tiyamike dzina lanu loyera,

kuti tikutamandeni.”

36Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli,

kuyambira muyaya mpaka muyaya.

Ndipo anthu onse anati, “Ameni” ndipo “Tikutamandani Yehova.”

37Ndipo Davide anasiya Asafu pamodzi ndi anzake kumene kunali Bokosi la Chipangano la Yehova kuti azitumikira kumeneko nthawi zonse, monga mwa zoyenera kuchita pa tsiku lililonse. 38Iye anasiyanso Obedi-Edomu pamodzi ndi anzake 68 kuti azitumikira nawo pamodzi. Obedi-Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa anali alonda a pa chipata.

39Davide anasiya wansembe Zadoki ndi ansembe anzake ku chihema cha Yehova ku malo achipembedzo ku Gibiyoni 40kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa lansembe nthawi zonse mmawa ndi madzulo, potsata zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Yehova, amene anawapereka kwa Aisraeli. 41Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni ndi onse amene anawasankha mowatchula dzina kuti apereke mayamiko kwa Yehova, “pakuti chikondi chake ndi chosatha.” 42Hemani ndi Yedutuni anali oyangʼanira malipenga ndi ziwaya ndiponso zipangizo zina zoyimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni anawayika kuti aziyangʼanira pa chipata.

43Kenaka anthu onse anachoka, aliyense kupita kwawo. Ndipo Davide anabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake.