1 Mbiri 13 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 13:1-14

Abweretsanso Bokosi la Chipangano

1Davide anakambirana ndi akuluakulu ake, atsogoleri a anthu 1,000 ndi atsogoleri a anthu 100. 2Ndipo anati kwa gulu lonse la Israeli, “Ngati kukukomerani komanso ngati chili chifuniro cha Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kulikonse kumene kuli abale athu ena onse ku dziko lonse la Israeli ndiponso kwa ansembe ndi Alevi amene ali nawo mʼmidzi yawo ndi madera odyetsera ziweto, kuti abwere adzakhale nafe. 3Tiyeni tibweretsenso Bokosi la Mulungu wathu kuno kwathu, pakuti nthawi ya Sauli sitinafunse za bokosili.” 4Gulu lonse linavomereza izi, pakuti anthu onse anaona kuti kunali kofunika kutero.

5Kotero Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse, kuchokera ku mtsinje wa Sihori ku Igupto mpaka ku Lebo Hamati, kuti abweretse Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriati-Yearimu. 6Davide pamodzi ndi Aisraeli onse anapita ku Baalahi (Kiriati-Yearimu) ku Yuda kukatenga Bokosi la Yehova Mulungu, amene amakhala pakati pa akerubi. Limeneli ndiye Bokosi la Chipangano lomwe limadziwika ndi Dzina lake.

7Iwo anachotsa Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Abinadabu pa ngolo yatsopano. Uza ndi Ahiyo ndiwo ankayendetsa ngoloyo. 8Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Mulungu, poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.

9Atafika pa malo opunthira tirigu ku Kidoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire bokosilo, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa. 10Yehova anapsera mtima Uza ndipo anamukantha chifukwa chogwira bokosilo. Choncho iyeyo anafera pomwepo pamaso pa Mulungu.

11Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.

12Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Mulungu ndipo anafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu lingafike bwanji kwathu?” 13Iye sanapitenso nalo Bokosi la Mulungu ku Mzinda wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti. 14Ndipo Bokosi la Mulungu linakhala mʼbanja la Obedi-Edomu mʼnyumba mwake kwa miyezi itatu ndipo Yehova anadalitsa nyumba yake ndi chilichonse chimene anali nacho.