1 Mbiri 12 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 12:1-40

Ankhondo Amene Anali ndi Davide, Sauli Asanafe

1Nawa anthu amene anabwera kwa Davide ali ku Zikilagi pamene iye anathamangitsidwa ndi Sauli mwana wa Kisi (iwowo anali mʼgulu la asilikali amene ankamuthandiza pa nkhondo. 2Iwo anali ndi mauta ndipo amadziwa kuponya mivi komanso miyala, ndipo amatha kuponyera dzanja lamanja kapena lamanzere. Iwo anali abale ake a Sauli ochokera ku fuko la Benjamini.

3Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri ndi Yowasi ana a Semaya wa ku Gibeya; Yezieli ndi Peleti ana a Azimaveti; Beraka, Yehu wa ku Anatoti, 4ndi Isimaiya wa ku Gibiyoni, munthu wamphamvu mʼgulu la anthu makumi atatu aja, yemwenso anali mtsogoleri wawo; Yeremiya, Yahazieli, Yohanani, Yozabadi wa ku Gederi, 5Eluzai, Yerimoti, Bealiya, Semariya ndi Sefatiya Mharufi; 6Elikana, Isiya, Azareli, Yowezeri ndi Yasobeamu a ku banja la Kora; 7ndi Yowela ndi Zebadiya ana a Yerohamu wa ku Gedori.

8Asilikali ena a fuko la Gadi anathawira kwa Davide ku linga lake ku chipululu. Iwo anali asilikali olimba mtima, okonzekera nkhondo ndipo amadziwa kugwiritsa ntchito chishango ndi mkondo. Iwowo anali woopsa ngati mikango ndipo anali aliwiro ngati ngoma zamʼmapiri.

9Mtsogoleri wawo anali Ezeri,

wotsatana naye anali Obadiya, wachitatu anali Eliabu,

10wachinayi anali Misimana, Yeremiya anali wachisanu,

11wachisanu ndi chimodzi anali Atai, Elieli anali wachisanu ndi chiwiri,

12wachisanu ndi chitatu anali Yohanani, Elizabadi anali wachisanu ndi chinayi,

13wakhumi anali Yeremiya ndipo Makibanai anali wa 11.

14Anthu a fuko la Gadi amenewa anali atsogoleri; angʼonoangʼono amalamulira anthu 100 pamene akuluakulu amalamulira anthu 1,000. 15Awa ndi amene anawoloka Yorodani mwezi woyamba pamene mtsinje unali utasefukira mbali zonse, ndipo anathamangitsa aliyense amene amakhala mʼchigwa, mbali ya kumadzulo ndi kummawa.

16Anthu ena a fuko la Benjamini ndi ena ochokera ku Yuda anabweranso kwa Davide pamene anali ku linga lake. 17Davide anapita kukakumana nawo ndipo anati, “Ngati mwabwera kwa ine mwamtendere, kuti mundithandize, ndakonzeka kugwirizana nanu. Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, ngakhale kuti sindinalakwe, Mulungu wa makolo anthu aone izi ndipo akuweruzeni.”

18Kenaka Mzimu anabwera pa Amasai, mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja ndipo anati:

“Inu Davide, ife ndife anu!

Tili nanu limodzi, inu mwana wa Yese!

Kupambana, Kupambana kwa inu,

ndiponso kupambana kukhale kwa iwo amene akukuthandizani

pakuti Mulungu wanu adzakuthandizani.”

Kotero Davide anawalandira ndipo anawayika kukhala atsogoleri a magulu ake a ankhondo.

19Anthu ena a fuko la Manase anathawira kwa Davide pamene anapita ndi Afilisti kukamenyana ndi Sauli. (Iye ndi anthu ake sanathandize Afilisti chifukwa, atsogoleri awo atakambirana, anamubweza Davide. Iwo anati, “Ife tidzawonongedwa ngati uyu adzabwerera kwa mbuye wake Sauli).” 20Davide atapita ku Zikilagi, anthu a fuko la Manase amene anathawira kwa iye anali awa: Adina, Yozabadi, Yediaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai; atsogoleri a magulu a anthu 1,000 a ku Manase. 21Iwowa anathandiza Davide kulimbana ndi magulu achifwamba, pakuti onsewa anali asilikali olimba mtima ndipo anali atsogoleri mʼgulu lake la ankhondo. 22Tsiku ndi tsiku anthu amabwera kudzathandiza Davide, mpaka anakhala ndi gulu lalikulu la ankhondo, ngati gulu la ankhondo a Mulungu.

Enanso Abwera kwa Davide ku Hebroni

23Nachi chiwerengero cha magulu a anthu ankhondo amene anabwera kwa Davide ku Hebroni kudzapereka ufumu wa Sauli kwa iye, monga momwe ananenera Yehova:

24Anthu a fuko la Yuda onyamula chishango ndi mkondo analipo 6,800;

25Anthu a fuko la Simeoni, asilikali okonzekera nkhondo analipo 7,100;

26Anthu a fuko la Levi analipo 4,600, 27mtsogoleri Yehoyada wa banja la Aaroni anabweranso ndi anthu 3,700, 28ndi Zadoki, mnyamata wankhondo wolimba mtima, anabwera ndi akuluakulu 22 ochokera mʼbanja lake;

29Anthu a fuko la Benjamini, abale ake a Sauli analipo 3,000 ndipo ambiri anali ndi Sauli ku nyumba yake pa nthawiyi;

30Anthu a fuko la Efereimu, asilikali olimba mtima, otchuka pa mabanja awo analipo 20,800;

31Anthu a fuko latheka la Manase amene anawayitana kuti adzakhazikitse nawo ufumu wa Davide analipo 18,000;

32Anthu a fuko la Isakara amene ankazindikira nthawi ndipo amadziwa zimene Israeli ankayenera kuchita, analipo atsogoleri 200 pamodzi ndi abale awo onse amene amawatsogolera.

33Anthu a fuko la Zebuloni, analipo 5,000. Iwowa anali asilikali odziwa bwino nkhondo, okhala ndi zida za mtundu uliwonse, okonzekera kudzathandiza Davide ndi mtima umodzi.

34Anthu a fuko la Nafutali, analipo atsogoleri 1,000 pamodzi ndi anthu 37,000 onyamula zishango ndi mikondo;

35Anthu a fuko la Dani, okonzekera nkhondo analipo 28,600.

36Anthu a fuko la Aseri, asilikali odziwa bwino nkhondo, okonzekeradi nkhondo analipo 40,000;

37Ndipo kuchokera kummawa kwa Yorodani, anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase, amene anali ndi zida za mtundu uliwonse analipo 120,000.

38Onsewa anali anthu odziwa kumenya nkhondo amene anadzipereka ku magulu awo. Iwo anabwera ku Hebroni ali otsimikiza kudzamuyika Davide kukhala mfumu ya Aisraeli. Aisraeli ena onse anali ndi mtima umodzinso womuyika Davide kukhala mfumu. 39Anthuwa anakhala ndi Davide masiku atatu akudya ndi kumwa pakuti mabanja awo anawapatsa zakudya. 40Komanso anthu oyandikana nawo ochokera ku Isakara, Zebuloni ndi Nafutali anabweretsa zakudya pa abulu, ngamira, nyulu ndi ngʼombe. Panali ufa wambiri, makeke ankhuyu, ntchintchi za mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi, popeza munali chimwemwe mu Israeli.

New Russian Translation

1 Паралипоменон 12:1-40

Первые сторонники Давида

1Вот имена тех, кто пришел к Давиду в город Циклаг, когда он укрывался от Саула, сына Киша12:1 См. 1 Цар. 27:1-6.. (Они были среди воинов, которые помогали ему в сражениях. 2У них были луки, и они могли метать камни и стрелять из лука и правой, и левой рукой. Они были родственниками Саула из рода Вениамина.)

3Их вождь Ахиезер и за ним Иоаш – сыновья Шемаи из Гивы; Иезиел и Пелет – сыновья Азмавета; Бераха и Ииуй из Анатота; 4Ишмая гаваонитянин – воин из числа тех тридцати и вождь над ними; Иеремия, Иахазиил, Иоханан и Иозавад из Гедеры; 5Элузай, Иеримот, Веалия, Шемария и харуфитянин Шефатия; 6корахиты Элкана, Ишшия, Азариил, Иоезер и Иашовеам; 7Иоела и Зевадия – сыновья Иерохама из Гедора.

Сторонники Давида из рода Гада

8Перешли к Давиду в его укрепление в пустыне и некоторые из гадитян. Это были отважные и опытные воины, умеющие обращаться со щитом и копьем. Лица их были, как у львов и быстры они были, как газели в горах.

9Вождем был Эзер,

вторым после него – Авдий,

третьим – Элиав,

10Мишманна – четвертым, Иеремия – пятым,

11Аттай – шестым, Элиэл – седьмым,

12Иоханан – восьмым, Элзавад – девятым,

13Иеремия – десятым, и Махбанай – одиннадцатым.

14Эти гадитяне были военачальниками: наименьший стоял над сотней, а наибольший над тысячей. 15Это они переправились через реку Иордан в первый месяц, когда она выходит из берегов, и обратили в бегство всех, кто жил в долинах к востоку и к западу.

Сторонники Давида из родов Вениамина и Иуды

16Другие вениамитяне и некоторые из рода Иуды также пришли в укрепление к Давиду. 17Давид вышел навстречу и сказал им:

– Если вы пришли с миром, чтобы помогать мне, я готов объединиться с вами. Но если вы пришли, чтобы предать меня моим врагам, когда мои руки чисты от насилия, то пусть Бог наших отцов увидит и рассудит.

18Тогда на Амасая, вождя тридцати, сошел Дух и он сказал:

– Мы твои, о Давид!

Мы с тобою, о сын Иессея!

Успеха, успеха тебе,

и успеха твоим помощникам,

ведь тебе помогает твой Бог.

Давид принял их и поставил их во главе своего войска.

Сторонники Давида из рода Манассии

19Когда Давид пошел с филистимлянами воевать против Саула, к нему перешли некоторые из рода Манассии. (Давид и его люди не помогали филистимлянам, потому что их правители, посоветовавшись, отослали его прочь. Они сказали: «Если он перейдет к своему господину Саулу, то это нам будет стоить головы».)

20Когда Давид возвращался в Циклаг, из рода Манассии к нему перешли:

Аднах, Иозавад, Иедиаел, Михаил, Иозавад, Элигу и Циллетай – тысяченачальники манассиян.

21Они помогали Давиду отражать набеги грабителей, потому что все они были отважными воинами и полководцами в его войске. 22День за днем люди шли на помощь Давиду, пока войско его не стало так велико, как войско Бога.

Войско Давида в Хевроне

23Вот количество воинов, вооруженных для битвы, которые пришли к Давиду в Хеврон, чтобы по слову Господа передать ему царство Саула:

24людей рода Иуды, которые носили щит и копье, – 6 800 вооруженных для битвы;

25из рода Симеона, воинов, готовых к битве, – 7 100;

26из рода Левия – 4 600, 27вместе с Иодаем, вождем из дома Аарона, который привел с собой 3 700 человек, 28и Цадоком, отважным молодым воином, с 22 военачальниками из его клана;

29из рода Вениамина – родственников Саула – 3 000 человек (большинство из них прежде хранило верность дому Саула);

30из рода Ефрема, отважных воинов, прославленных в своих кланах, – 20 800;

31из половины рода Манассии – 18 000 человек, которые были названы поименно, чтобы прийти и сделать Давида царем;

32из рода Иссахара, людей разумных, которые знали, что и когда надлежало делать Израилю, – 200 вождей со всеми своими родственниками, следующими по их слову.

33Из рода Завулона опытных воинов, вооруженных всякого вида оружием, которые единодушно пришли на помощь Давиду, – 50 000;

34из рода Неффалима – 1 000 военачальников и с ними 37 000 человек, носящих щит и копье;

35из рода Дана, готовых к битве, – 28 600;

36из рода Асира, опытных воинов, готовых к битве, – 40 000.

37А из родов Рувима, Гада и половины рода Манассии из-за Иордана – 120 000 человек, вооруженных всякого вида оружием.

38Все эти воины боевым строем пришли в Хеврон исполненные воли сделать Давида царем над всем Израилем. И все остальные израильтяне единодушно решили сделать Давида царем. 39Они пробыли там у Давида три дня, ели и пили, потому что их семьи снабдили их запасами. 40А также их соседи, даже такие, как роды Иссахара, Завулона и Неффалима, приходили с ослами, верблюдами, мулами и волами, нагруженными едой. Еды – муки, инжира, изюма, вина, масла, мяса крупного и мелкого скота – было в изобилии, потому что в Израиле царила радость.