1 Mafumu 9 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 9:1-28

Yehova Aonekera Solomoni

1Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene ankafuna, 2Yehova anamuonekera kachiwiri, monga momwe anamuonekera ku Gibiyoni. 3Yehova ananena kwa iye kuti:

“Ndamva pemphero ndi pembedzero lako pa zimene wapempha pamaso panga. Ndayipatula Nyumba iyi, imene wamanga, poyikamo Dzina langa mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga zidzakhala pamenepo nthawi zonse.

4“Kunena za iwe, ukayenda pamaso panga mokhulupirika, mwangwiro ndi moona mtima monga momwe anachitira abambo ako Davide, ndi kuchita zonse zimene ndakulamula ndi kusamalitsa malangizo ndi malamulo anga, 5Ine ndidzakhazikitsa mpando wako waufumu pa Israeli mpaka muyaya, monga ndinalonjezera abambo ako Davide pamene ndinati, ‘Sipadzasowa munthu pa mpando waufumu wa Israeli.’

6“Koma ngati iwe kapena ana ako mudzapatuka ndi kuleka kusunga malamulo ndi mawu anga amene ndakupatsani ndi kupita kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza, 7pamenepo Ine ndidzazula Aisraeli mʼdziko limene ndinawapatsa ndiponso ndidzayikana Nyumba ino imene ndayipatula chifukwa cha Dzina langa. Pamenepo Aisraeli adzasanduka mwambi ndi chinthu chonyozedwa pakati pa anthu onse. 8Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzatsonya ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’ 9Anthu adzayankha kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti asiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo mʼdziko la Igupto, ndipo akangamira milungu ina ndi kumayipembedza ndi kuyitumikira. Choncho Iye wabweretsa zovuta zonsezi.’ ”

Zina zimene Solomoni Anachita

10Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga nyumba ziwirizi: Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, 11Mfumu Solomoni anapereka mizinda makumi awiri ya ku Galileya kwa Hiramu mfumu ya ku Turo chifukwa Hiramu nʼkuti atapereka mitengo yonse ya mkungudza ndi ya payini ndiponso golide yense zimene Solomoni ankazifuna. 12Koma Hiramu atabwera kuchokera ku Turo kudzaona mizinda imene Solomoni anamupatsa, sanasangalatsidwe nayo mizindayo. 13Iye anafunsa kuti, “Mʼbale wanga, kodi iyi nʼkukhala mizinda yondipatsa?” Ndipo iye anayitcha mizindayo Dziko la Kabuli, dzina lomwe amatchedwa mpaka lero lino. 14Koma Hiramu anali atatumiza kwa mfumu golide oposa makilogalamu 4,000.

15Izi ndi zimene anachita Mfumu Solomoni: Analamula anthu kuti agwire ntchito yathangata pomanga Nyumba ya Yehova, nyumba yake, malo achitetezo a Milo, mpanda wa Yerusalemu, Hazori, Megido ndi Gezeri. 16(Farao mfumu ya ku Igupto inali itathira nkhondo ndi kulanda Gezeri. Iye anatentha mzindawo. Anapha Akanaani amene ankakhala mʼmenemo ndipo kenaka anawupereka ngati mphatso yaukwati kwa mwana wake wamkazi amene anakwatiwa ndi Solomoni. 17Ndipo Solomoni anamanganso Gezeri.) Iye anamanga Beti-Horoni Wakumunsi, 18Baalati ndi Tadimori ku chipululu, mʼdziko lake lomwelo, 19pamodzinso ndi mizinda yake yosungira chuma ndiponso mizinda yosungiramo magaleta ndi akavalo ake. Anamanganso chilichonse chimene anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.

20Panali anthu amene anatsala pakati pa mitundu ya Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi (anthu awa sanali Aisraeli). 21Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino. 22Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Mwisraeli aliyense; iwo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, atsogoleri a ankhondo, akapitawo ake, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake. 23Amenewa ndiwo anali akuluakulu oyangʼanira ntchito za Solomoni. Anthu okwana 550 ndiwo ankayangʼanira anthu amene ankagwira ntchitowo.

24Mwana wamkazi wa Farao atachoka mu Mzinda wa Davide, kupita ku nyumba ya mfumu imene Solomoni anamumangira, Solomoni anamanga malo achitetezo a Milo.

25Katatu pa chaka Solomoni ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pa guwa lansembe limene anamangira Yehova ndiponso ankafukiza lubani pamaso pa Yehova. Potero ankakwaniritsa zoyenera kuchitika mu Nyumba ya Yehova.

26Mfumu Solomoni anapanganso sitima zapamadzi ku Ezioni Geberi, malo amene ali pafupi ndi Eloti ku Edomu, mʼmbali mwa Nyanja Yofiira. 27Ndipo Hiramu anatumiza anthu ake oyendetsa sitima zapamadzi amene ankadziwa za pa nyanja kuti aziyendetsa pamodzi ndi anthu a Solomoni. 28Iwo anapita ku Ofiri ndipo anakatenga golide okwana makilogalamu 14,000, amene anamupereka kwa Mfumu Solomoni.

Священное Писание

3 Царств 9:1-28

Вечный является Сулейману

(2 Лет. 7:11-22)

1Когда Сулейман закончил строить храм Вечного, царский дворец и всё, что желал построить, 2Вечный явился ему во второй раз, как являлся ему в Гаваоне. 3Вечный сказал ему:

– Я услышал молитву и мольбу, которую ты вознёс Мне. Я освятил Себе храм, который ты построил, чтобы Мне поклонялись там вовеки. Мои глаза и сердце будут там всегда. 4А ты, если будешь ходить предо Мной в непорочности сердца и в правоте, как ходил твой отец Давуд, исполнять всё, что Я повелю, и соблюдать Мои установления и законы, 5то Я упрочу твой царский престол над Исраилом навеки, как Я обещал Давуду, твоему отцу, когда сказал: «Ты не лишишься преемника на престоле Исраила».

6Но если вы или ваши сыновья отвернётесь от Меня, не будете соблюдать повеления и установления, которые Я дал вам, и пойдёте служить другим богам и поклоняться им, 7то Я искореню Исраил из земли, которую Я дал ему, и отвергну этот храм, который Я освятил для поклонения Мне. Исраил станет у всех народов притчей и посмешищем. 8И хотя этот храм сейчас превознесён, всякий, кто пройдёт мимо, поразится и будет насмехаться, говоря: «Почему Вечный сделал такое с этой страной и с этим храмом?» 9А ему ответят: «Потому что они оставили Вечного, своего Бога, Который вывел их предков из Египта, приняли других богов, поклонялись и служили им – вот за что Вечный навёл на них все эти беды».

Другие дела Сулеймана

(2 Лет. 8:1-18)

10По истечении двадцати лет, в которые Сулейман строил два этих здания – храм Вечного и царский дворец, 11он отдал двадцать городов Галилеи царю Тира Хираму, потому что Хирам поставлял ему столько кедрового и кипарисового дерева и золота, сколько тот хотел. 12Но когда Хирам прибыл из Тира, чтобы осмотреть города, которые дал ему Сулейман, он остался недоволен.

13– Что же это за города ты мне дал, брат мой? – спросил он.

И он назвал их землёю Кавул («негодная земля»)9:13 О переводе имён и названий см. приложение VI. – название, что осталось за ними до сегодняшнего дня.

14(Хирам же послал царю четыре тысячи триста двадцать килограммов9:14 Букв.: «сто двадцать талантов». золота.)

15Вот сведения о подневольных людях, чей труд царь Сулейман использовал для строительства храма Вечного, своего дворца, Милло9:15 Милло – с языка оригинала переводится как «насыпь». Возможно, что это были какие-то городские укрепления., иерусалимской стены, а также для городов Хацора, Мегиддо и Гезера. 16(Фараон, царь Египта, напал на Гезер и захватил его. Он предал его огню, перебил всех хананеев в нём и отдал его в приданое своей дочери, жене Сулеймана.) 17И Сулейман отстроил Гезер, построил Нижний Бет-Хорон, 18Баалат и Тадмор в пустыне, в своей земле, 19а также все города для хранения запасов и города для своих колесниц и коней9:19 Или: «колесничих»; или: «всадников».. Он построил всё, что ему хотелось построить в Иерусалиме, на Ливане и во всех землях, которыми он правил.

20-21Оставшихся в стране неисраильтян – потомков аморреев, хеттов, перизеев, хивеев и иевусеев, – которых исраильтяне не смогли полностью уничтожить, Сулейман использовал как рабскую силу, как это есть и до сегодняшнего дня. 22Но исраильтян Сулейман не обращал в рабов, они были его воинами, приближёнными, сановниками, военачальниками и начальниками его колесниц и колесничих. 23Ещё они были главными начальниками его строительных работ – пятьсот пятьдесят начальников, которые распоряжались рабочими.

24После того как дочь фараона перебралась из Города Давуда во дворец, который построил для неё Сулейман, он построил Милло.

25Три раза в год Сулейман возносил всесожжения и жертвы примирения на жертвеннике, что построил для Вечного, возжигая благовония перед Вечным. Итак, он завершил строительство храма.

26Ещё царь Сулейман строил корабли в Эцион-Гевере, что рядом с Елатом в земле Эдома, на побережье Тростникового моря9:26 Тростниковое море – буквальный перевод с языка оригинала. В данном случае речь идёт об Акабском заливе Красного моря (см. карту № 2).. 27А Хирам послал с кораблями своих слуг – моряков, знавших море, вместе с людьми Сулеймана. 28Они отплыли в Офир и привезли оттуда пятнадцать тысяч сто двадцать килограммов9:28 Букв.: «четыреста двадцать талантов». золота, которое и доставили царю Сулейману.