1 Mafumu 18 – CCL & NVI-PT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 18:1-46

Eliya ndi Obadiya

1Patapita masiku ambiri, mʼchaka chachitatu cha chilala, Yehova anayankhula ndi Eliya kuti, “Pita ukadzionetse kwa Ahabu ndipo ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi.” 2Choncho Eliya anapita kukadzionetsa kwa Ahabu.

Tsono nthawi imeneyi njala inakula kwambiri mu Samariya, 3ndipo Ahabu anayitana Obadiya amene ankayangʼanira nyumba yake yaufumu. (Obadiya ankaopa Yehova kwambiri. 4Pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri 100 ndi kuwabisa mʼmapanga awiri, phanga lililonse aneneri makumi asanu, ndipo ankawapatsa chakudya ndi madzi). 5Ahabu anawuza Obadiya kuti, “Pita mʼdziko kulikonse kumene kuli zitsime za madzi ndi ku zigwa zonse. Mwina mwake tingapeze udzu oti nʼkumadyetsa akavalo ndi abulu kuti akhale ndi moyo, kuti tisaphe chiweto chilichonse.” 6Choncho anagawana dziko loti apiteko, Ahabu anapita mbali ina, Obadiya nʼkupita ina.

7Obadiya akuyenda mʼnjira anakumana ndi Eliya. Ndipo taonani, Obadiya anamuzindikira Eliyayo, naweramira pansi ndipo anati, “Kodi ndinu, mbuye wanga Eliya?”

8Eliya anayankha kuti, “Inde. Pita kawuze mbuye wako kuti, ‘Eliya wabwera.’ ”

9Obadiya anafunsa kuti, “Kodi ndalakwa chiyani kuti inu mupereke mtumiki wanu kwa Ahabu kuti akaphedwe? 10Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, kulibe mtundu wa anthu kapena ufumu uliwonse kumene mbuye wanga sanatumeko anthu okakufunafunani. Ndipo pamene mtundu wa anthu kapena ufumu unena kuti kuno kulibe, Ahabu ankawalumbiritsa kuti atsimikizedi kuti inuyo kulibe kumeneko. 11Koma tsopano mukundiwuza kuti ndipite kwa mbuye wanga ndi kukanena kuti, ‘Eliya wabwera.’ 12Ine sindikudziwa kumene Mzimu wa Yehova udzakupititsani ine ndikachoka. Ngati ndipita kukamuwuza Ahabu ndipo iye wosadzakupezani, adzandipha. Komatu ine mtumiki wanu ndakhala ndi kupembedza Yehova kuyambira ubwana wanga. 13Mbuye wanga, kodi simunamve zimene ndinachita pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova? Ine ndinabisa aneneri 100 a Yehova mʼmapanga awiri, mʼphanga lililonse aneneri makumi asanu, ndipo ndinkawapatsa chakudya ndi madzi akumwa. 14Ndiye inu tsopano mukundiwuza kuti ndipite kwa mbuye wanga ndi kukanena kuti, ‘Eliya wabwera.’ Iyeyo adzandipha ndithu!”

15Eliya anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse wamoyo, amene ndimamutumikira, ine lero ndidzaonekera ndithu pamaso pa Ahabu.”

Eliya pa Phiri la Karimeli

16Choncho Obadiya anapita kukakumana ndi Ahabu, namuwuza, ndipo Ahabu anapita kukakumana ndi Eliya. 17Pamene Ahabu anaona Eliya, anati kwa iye, “Kodi ndiwedi, munthu wovutitsa Israeli uja?”

18Eliya anayankha kuti, “Ine sindinavutitse Israeli, koma ndinuyo ndi banja lanu. Mwasiya malamulo a Yehova ndipo mwatsatira Abaala. 19Tsopano sonkhanitsani anthu a mʼdziko lonse la Israeli kuti akumane nane pa Phiri la Karimeli. Ndipo mubwere nawo aneneri a Baala 450 ndi aneneri a fano la Asera 400, amene amadya pa tebulo la Yezebeli.”

20Choncho Ahabu anatumiza mawu mʼdziko lonse la Israeli, ndipo anasonkhanitsa aneneri a Baala ku Phiri la Karimeli. 21Eliya anapita patsogolo pa anthuwo ndipo anati, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iwiri mpaka liti? Ngati Yehova ndi Mulungu, mutsateni; koma ngati Baala ndi Mulungu, mutsateni.”

Koma anthu aja sanayankhe.

22Pamenepo Eliya ananena kwa iwo kuti, “Ine ndilipo ndekha mneneri wa Yehova, koma Baala ali ndi aneneri 450. 23Tibweretsereni ngʼombe zazimuna ziwiri. Iwo asankhepo okha ngʼombe imodzi, ndipo ayidule nthulinthuli ndi kuziyika pa nkhuni nthulizo, koma osakolezapo moto. Ndipo ine ndidzadula nthulinthuli ngʼombe inayo ndi kuyika pa nkhuni koma sindikolezapo moto. 24Kenaka inu muyitane dzina la mulungu wanu, ndipo ine ndidzayitana dzina la Yehova. Mulungu amene ati ayankhe potumiza moto, iyeyo ndiye Mulungu.”

Pamenepo anthu onse anati, “Izi mwanena zamveka bwino.”

25Eliya anawuza aneneri a Baala kuti, “Yambani ndinu. Sankhani ngʼombe yayimuna imodzi, muyikonze, popeza mulipo ambiri. Muyitane dzina la mulungu wanu, koma musakoleze moto.” 26Choncho iwo anatenga ngʼombe yayimunayo imene anawapatsa, nayikonza.

Kenaka anayitana dzina la Baala kuyambira mmawa mpaka masana. Iwo anafuwula kuti, “Inu Baala, tiyankheni ife.” Koma panalibe yankho; palibe amene anayankha. Ndipo anavinavina mozungulira guwa lansembe limene anapanga.

27Nthawi yamasana Eliya anayamba kuwanyogodola ndipo anati, “Fuwulani kwambiri. Ndithudi, iye ndi mulungu! Mwinatu akulingalira kwambiri, kapena watanganidwa, kapena ali paulendo. Mwina wagona ndipo nʼkofunika kuti adzutsidwe.” 28Choncho iwo anafuwula kwambiri ndi kudzichekacheka ndi malupanga ndi mikondo, potsata miyambo yawo, mpaka kutuluka magazi. 29Nthawi yamasana inadutsa, ndipo anapitiriza kunenera mwakhama mpaka nthawi yopereka nsembe ya madzulo. Koma panalibe yankho. Palibe amene anayankha, kapena kulabadira zimenezo.

30Pamenepo Eliya anati kwa anthu onse, “Senderani pafupi ndi ine.” Ndipo anthu onsewo anasendera pafupi ndi iye, ndipo iye anakonza guwa lansembe la Yehova limene linali litawonongeka. 31Eliya anatenga miyala 12, mwala uliwonse kuyimira fuko lililonse la Yakobo, amene Yehova anamuwuza kuti, “Dzina lako lidzakhala Israeli.” 32Ndi miyala imeneyo anamanga guwa mʼdzina la Yehova, ndipo anakumba ngalande yayikulu yolowa malita 15 a madzi kuzungulira guwalo. 33Anayika nkhuni zija mʼmalo mwake nadula nthulinthuli ngʼombe yayimuna ija ndi kuyika nthulizo pa nkhunipo. Pamenepo Eliya anati, “Dzazani mitsuko inayi ndi madzi ndipo muwathire pa nyama ya nsembeyo ndi nkhunizo.”

34Eliya anati, “Thiraninso kachiwiri.” Anthu aja anathiranso madziwo kachiwiri.

Iye analamula kuti, “Thiraninso kachitatu.” Ndipo iwo anathiranso kachitatu. 35Madziwo anayenderera pansi kuzungulira guwa lansembe, nadzaza ngalande yonse.

36Pa nthawi yopereka nsembe, mneneri Eliya anasendera pafupi ndi guwa lansembe, napemphera kuti, “Inu Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, lero zidziwike kuti ndinu Mulungu mu Israeli ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, kuti ine ndachita zonsezi chifukwa mwalamula ndinu. 37Ndiyankheni, Inu Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe Inu Yehova, kuti ndinu Mulungu, ndipo kuti mutembenuziranso mitima yawo kwa Inu.”

38Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhuni, miyala ndi dothi lomwe. Unawumitsanso madzi amene anali mʼngalande.

39Anthu onse ataona zimenezi, anaweramitsa nkhope zawo pansi, nafuwula kuti, “Yehova ndiye Mulungu! Yehova ndiye Mulungu!”

40Pamenepo Eliya analamula anthuwo kuti, “Gwirani aneneri a Baala. Musalole kuti wina aliyense athawe!” Anagwira onsewo ndipo Eliya anabwera nawo ku Chigwa cha Kisoni, nawapha kumeneko.

41Ndipo Eliya anati kwa Ahabu, “Pitani, kadyeni ndi kumwa, pakuti kukumveka mkokomo wa mvula.” 42Choncho Ahabu anapita kukadya ndi kumwa, koma Eliya anakwera pamwamba pa Phiri la Karimeli, ndipo anawerama mpaka pansi, nayika mutu wake pakati pa mawondo ake.

43Eliya anawuza mtumiki wake kuti, “Pita kayangʼane ku nyanja.” Ndipo iye anapita nakayangʼana.

Mtumikiyo anati, “Kulibe kanthu.”

Kasanu nʼkawiri Eliya anati, “Pitanso.”

44Ulendo wachisanu ndi chiwiri mtumikiyo anafotokoza kuti, “Taonani, kamtambo kakangʼono kokhala ngati dzanja la munthu kakutuluka ku nyanja.”

Pamenepo Eliya anati, “Pita, kamuwuze Ahabu kuti, ‘Konzani galeta lanu ndipo mutsike mvula isanakutsekerezeni.’ ”

45Nthawi imeneyi nʼkuti kuthambo kutayamba kusonkhana mitambo yakuda, mphepo inawomba, mvula yamphamvu inagwa ndipo Ahabu anakwera galeta napita ku Yezireeli. 46Dzanja la Yehova linali pa Eliya ndipo atamangira lamba chovala chake, anathamanga ndi kumupitirira Ahabu mpaka kukhala woyamba kukafika ku Yezireeli.

Nova Versão Internacional

1 Reis 18:1-46

Elias e Obadias

1Depois de um longo tempo, no terceiro ano da seca, a palavra do Senhor veio a Elias: “Vá apresentar-se a Acabe, pois enviarei chuva sobre a terra”. 2E Elias foi.

Como a fome era grande em Samaria, 3Acabe convocou Obadias, o responsável por seu palácio, homem que temia muito o Senhor. 4Jezabel estava exterminando os profetas do Senhor. Por isso Obadias reuniu cem profetas e os escondeu em duas cavernas, cinquenta em cada uma, e lhes forneceu comida e água. 5Certa vez Acabe disse a Obadias: “Vamos a todas as fontes e vales do país. Talvez consigamos achar um pouco de capim para manter vivos os cavalos e as mulas e assim não será preciso matar nenhum animal”. 6Para isso dividiram o território que iam percorrer; Acabe foi numa direção e Obadias noutra.

7Quando Obadias estava a caminho, Elias o encontrou. Obadias o reconheceu, inclinou-se até o chão e perguntou: “És tu mesmo, meu senhor Elias?”

8“Sou”, respondeu Elias. “Vá dizer ao seu senhor: ‘Elias está aqui’.”

9“O que eu fiz de errado”, perguntou Obadias, “para que entregues o teu servo a Acabe para ser morto? 10Juro pelo nome do Senhor, o teu Deus, que não há uma só nação ou reino aonde o rei, meu senhor, não enviou alguém para procurar por ti. E, sempre que uma nação ou reino afirmava que tu não estavas lá, ele os fazia jurar que não conseguiram encontrar-te. 11Mas agora me dizes para ir dizer ao meu senhor: ‘Elias está aqui’. 12Não sei para onde o Espírito do Senhor poderá levar-te quando eu te deixar. Se eu for dizer isso a Acabe e ele não te encontrar, ele me matará. E eu, que sou teu servo, tenho adorado o Senhor desde a minha juventude. 13Por acaso não ouviste, meu senhor, o que eu fiz enquanto Jezabel estava matando os profetas do Senhor? Escondi cem dos profetas do Senhor em duas cavernas, cinquenta em cada uma, e os abasteci de comida e água. 14E agora me dizes que vá dizer ao meu senhor: ‘Elias está aqui’. Ele vai me matar!”

15E disse Elias: “Juro pelo nome do Senhor dos Exércitos, a quem eu sirvo, que hoje eu me apresentarei a Acabe”.

Elias no Monte Carmelo

16Então Obadias dirigiu-se a Acabe, passou-lhe a informação, e Acabe foi ao encontro de Elias. 17Quando viu Elias, disse-lhe: “É você mesmo, perturbador de Israel?”

18“Não tenho perturbado Israel”, Elias respondeu. “Mas você e a família do seu pai têm. Vocês abandonaram os mandamentos do Senhor e seguiram os baalins. 19Agora convoque todo o povo de Israel para encontrar-se comigo no monte Carmelo. E traga os quatrocentos e cinquenta profetas de Baal e os quatrocentos profetas de Aserá, que comem à mesa de Jezabel.”

20Acabe convocou então todo o Israel e reuniu os profetas no monte Carmelo. 21Elias dirigiu-se ao povo e disse: “Até quando vocês vão oscilar para um lado e para o outro? Se o Senhor é Deus, sigam-no; mas, se Baal é Deus, sigam-no”.

O povo, porém, nada respondeu.

22Disse então Elias: “Eu sou o único que restou dos profetas do Senhor, mas Baal tem quatrocentos e cinquenta profetas. 23Tragam dois novilhos. Escolham eles um, cortem-no em pedaços e o ponham sobre a lenha, mas não acendam fogo. Eu prepararei o outro novilho e o colocarei sobre a lenha, e também não acenderei fogo nela. 24Então vocês invocarão o nome do seu deus, e eu invocarei o nome do Senhor. O deus que responder por meio do fogo, esse é Deus”.

Então todo o povo disse: “O que você disse é bom”.

25Elias disse aos profetas de Baal: “Escolham um dos novilhos e preparem-no primeiro, visto que vocês são tantos. Clamem pelo nome do seu deus, mas não acendam o fogo”. 26Então pegaram o novilho que lhes foi dado e o prepararam.

E clamaram pelo nome de Baal desde a manhã até o meio-dia. “Ó Baal, responde-nos!”, gritavam. E dançavam em volta do altar que haviam feito. Mas não houve nenhuma resposta; ninguém respondeu.

27Ao meio-dia Elias começou a zombar deles. “Gritem mais alto!”, dizia, “já que ele é um deus. Quem sabe está meditando, ou ocupado, ou viajando. Talvez esteja dormindo e precise ser despertado.” 28Então passaram a gritar ainda mais alto e a ferir-se com espadas e lanças, de acordo com o costume deles, até sangrarem. 29Passou o meio-dia, e eles continuaram profetizando em transe até a hora do sacrifício da tarde. Mas não houve resposta alguma; ninguém respondeu, ninguém deu atenção.

30Então Elias disse a todo o povo: “Aproximem-se de mim”. O povo aproximou-se, e Elias reparou o altar do Senhor, que estava em ruínas. 31Depois apanhou doze pedras, uma para cada tribo dos descendentes de Jacó, a quem a palavra do Senhor tinha sido dirigida, dizendo-lhe: “Seu nome será Israel”. 32Com as pedras construiu um altar em honra ao nome do Senhor e cavou ao redor do altar uma valeta na qual poderiam ser semeadas duas medidas18.32 Hebraico: 2 seás. O seá era uma medida de capacidade para secos. As estimativas variam entre 7 e 14 litros. de sementes. 33Depois arrumou a lenha, cortou o novilho em pedaços e o pôs sobre a lenha. Então lhes disse: “Encham de água quatro jarras grandes e derramem-na sobre o holocausto18.33 Isto é, sacrifício totalmente queimado. e sobre a lenha”.

34“Façam-no novamente”, disse, e eles o fizeram de novo.

“Façam-no pela terceira vez”, ordenou, e eles o fizeram pela terceira vez. 35A água escorria do altar, chegando a encher a valeta.

36À hora do sacrifício, o profeta Elias colocou-se à frente do altar e orou: “Ó Senhor, Deus de Abraão, de Isaque e de Israel, que hoje fique conhecido que tu és Deus em Israel e que sou o teu servo e que fiz todas estas coisas por ordem tua. 37Responde-me, ó Senhor, responde-me, para que este povo saiba que tu, ó Senhor, és Deus e que fazes o coração deles voltar para ti”.

38Então o fogo do Senhor caiu e queimou completamente o holocausto, a lenha, as pedras e o chão, e também secou totalmente a água na valeta.

39Quando o povo viu isso, todos caíram prostrados e gritaram: “O Senhor é Deus! O Senhor é Deus!”

40Então Elias ordenou-lhes: “Prendam os profetas de Baal. Não deixem nenhum escapar!” Eles os prenderam, e Elias os fez descer ao riacho de Quisom e lá os matou.

41E Elias disse a Acabe: “Vá comer e beber, pois já ouço o barulho de chuva pesada”. 42Então Acabe foi comer e beber, mas Elias subiu até o alto do Carmelo, dobrou-se até o chão e pôs o rosto entre os joelhos.

43“Vá e olhe na direção do mar”, disse ao seu servo. E ele foi e olhou.

“Não há nada lá”, disse ele.

Sete vezes Elias mandou: “Volte para ver”.

44Na sétima vez o servo disse: “Uma nuvem tão pequena quanto a mão de um homem está se levantando do mar”.

Então Elias disse: “Vá dizer a Acabe: Prepare o seu carro e desça, antes que a chuva o impeça”.

45Enquanto isso, nuvens escuras apareceram no céu, começou a ventar e a chover forte, e Acabe partiu de carro para Jezreel. 46O poder do Senhor veio sobre Elias, e ele, prendendo a capa com o cinto, correu à frente de Acabe por todo o caminho até Jezreel.