1 Mafumu 16 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 16:1-34

1Ndipo Yehova anayankhula kudzera mwa Yehu mwana wa Hanani, mawu odzudzula Baasa kuti, 2“Ine ndinakukuza kuchokera pa fumbi ndipo ndinakupanga kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli, koma iwe wakhala ukuyenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchimwitsa anthu anga Aisraeli naputa mkwiyo wanga chifukwa cha machimo awo. 3Taonani, Ine ndatsala pangʼono kuwononga Baasa pamodzi ndi nyumba yake, ndipo ndidzachitira nyumba yake zimene ndinachita pa nyumba ya Yeroboamu mwana wa Nebati. 4Agalu adzadya aliyense wa banja la Baasa amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame za mu mlengalenga zidzadya iwo amene adzafere kuthengo.”

5Tsono ntchito zina za Baasa ndi zamphamvu zake zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 6Baasa anamwalira nayikidwa mʼmanda amene anayikidwa makolo ake ku Tiriza. Ndipo Ela mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake.

7Komatu Yehova anayankhula kwa Baasa pamodzi ndi banja lake lonse kudzera mwa mneneri Yehu mwana wa Hanani, chifukwa cha zoyipa zonse zimene iye anachita pamaso pa Yehova, kukwiyitsa Yehovayo nakhala ngati nyumba ya Yeroboamu ndiponso chifukwa anawonongeratu banja la Yeroboamu.

Ela Mfumu ya Israeli

8Mʼchaka cha 26 cha ufumu wa Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa anakhala mfumu ya Israeli, ndipo analamulira ku Tiriza zaka ziwiri.

9Zimuri, mmodzi mwa akuluakulu ake, amene ankalamulira theka la magaleta ake, anamuchitira chiwembu. Nthawi imeneyi Ela anali ku Tiriza, akumwa koledzera nako mʼnyumba ya Ariza, munthu amene ankayangʼanira nyumba yaufumu ku Tiriza. 10Zimuri anadzalowa, namukantha ndi kumupha mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda. Ndipo Zimuriyo anakhala mfumu mʼmalo mwake.

11Zimuri atangoyamba kulamulira, anapha banja lonse la Baasa. Sanasiyepo munthu wamwamuna ndi mmodzi yemwe, wachibale kapena bwenzi lake. 12Choncho Zimuri anawononga banja lonse la Baasa, molingana ndi mawu amene Yehova anayankhula motsutsa Baasa kudzera mwa mneneri Yehu, 13chifukwa cha machimo onse amene Baasa ndi mwana wake Ela anachita nachimwitsa Israeli, anakwiyitsa Yehova, Mulungu wa Israeli ndi mafano awo osapindulitsa.

14Tsono ntchito zina za Ela ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?

Zimuri Mfumu ya Israeli

15Mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda, Zimuri analamulira ku Tiriza masiku asanu ndi awiri. Gulu la ankhondo linali litamanga misasa pafupi ndi Gibetoni, mzinda wa Afilisti. 16Ankhondo amene anali ku misasa atamva kuti Zimuri wachita chiwembu ndi kupha mfumu, tsiku lomwelo ku misasako anasankha Omuri, mkulu wa ankhondo kukhala mfumu ya Israeli. 17Tsono Omuri ndi Aisraeli onse amene anali naye anachoka ku Gibetoni ndi kukazinga Mzinda wa Tiriza. 18Zimuri ataona kuti mzinda walandidwa, anathawira ku nsanja ya nyumba ya mfumu ndipo anatentha nyumbayo iye ali momwemo. Kotero iyeyo anafa, 19chifukwa cha machimo amene iye anachita, kuchita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kuyenda mʼnjira za Yeroboamu, nachimwitsa nazo Aisraeli.

20Tsono ntchito zina za Zimuri ndi chiwembu chake chimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?

Omuri Mfumu ya Israeli

21Pambuyo pake Aisraeli anagawikana pakati: theka linatsatira Tibini mwana wa Ginati kuti limulonge ufumu, ndipo theka lina linatsatira Omuri. 22Koma anthu otsatira Omuri anali amphamvu kupambana amene ankatsatira Tibini mwana wa Ginati. Choncho Tibini anafa ndipo Omuri anakhala mfumu.

23Mʼchaka cha 31 cha Asa mfumu ya Yuda, Omuri anakhala mfumu ya Israeli, ndipo analamulira zaka 12 ndi miyezi isanu ndi umodzi ku Tiriza. 24Iye anagula phiri la Samariya kwa Semeri pa mtengo wa ndalama 6,000 za siliva ndipo pa phiripo anamangapo mzinda, nawutcha Samariya, potsata dzina la Semeri, dzina la mwini wakale wa phirilo.

25Koma Omuri anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo anachimwa kuposa mafumu ena onse amene analipo iye asanakhale mfumu. 26Pakuti iye anayenda mʼnjira zonse za Yeroboamu mwana wa Nebati, ndipo tchimo lake anachimwitsa nalo Aisraeli, nakwiyitsa Yehova Mulungu wa Israeli ndi mafano awo opandapake.

27Tsono ntchito zina za Omuri ndi zamphamvu zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 28Choncho Omuri anamwalira nayikidwa mʼmanda amene anayikidwa makolo ake ku Samariya. Ndipo Ahabu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Ahabu Akhala Mfumu ya Israeli

29Mʼchaka cha 38 cha ufumu wa Asa, mfumu ya Yuda, Ahabu mwana wa Omuri anakhala mfumu ya Israeli nalamulira Israeli ku Samariya zaka 22. 30Ahabu mwana wa Omuri anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova kupambana mafumu onse akale. 31Iye sanachiyese ngati chinthu chochepa chabe kuchita machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, koma anakwatiranso Yezebeli, mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni, nayamba kutumikira Baala ndi kumupembedza. 32Iye anapangira Baala guwa lansembe mʼnyumba ya Baala imene anamanga ku Samariya. 33Ahabu anapanganso fano la Asera ndi kukwiyitsa kwambiri Yehova Mulungu wa Israeli, kupambana mafumu onse a Israeli amene analipo iye asanakhale mfumu.

34Pa nthawi ya Ahabu, Hiyeli wa ku Beteli anamanganso mzinda wa Yeriko. Pa nthawi yomanga maziko ake, mwana wake woyamba wa mwamuna, Abiramu anamwalira, ndipo pa nthawi yomanga zipata zake, mwana wa mngʼono wa mwamuna Segubu, anamwaliranso. Izi zinachitika monga momwe Yehova ananenera kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni.

King James Version

1 Kings 16:1-34

1Then the word of the LORD came to Jehu the son of Hanani against Baasha, saying, 2Forasmuch as I exalted thee out of the dust, and made thee prince over my people Israel; and thou hast walked in the way of Jeroboam, and hast made my people Israel to sin, to provoke me to anger with their sins; 3Behold, I will take away the posterity of Baasha, and the posterity of his house; and will make thy house like the house of Jeroboam the son of Nebat. 4Him that dieth of Baasha in the city shall the dogs eat; and him that dieth of his in the fields shall the fowls of the air eat. 5Now the rest of the acts of Baasha, and what he did, and his might, are they not written in the book of the chronicles of the kings of Israel? 6So Baasha slept with his fathers, and was buried in Tirzah: and Elah his son reigned in his stead. 7And also by the hand of the prophet Jehu the son of Hanani came the word of the LORD against Baasha, and against his house, even for all the evil that he did in the sight of the LORD, in provoking him to anger with the work of his hands, in being like the house of Jeroboam; and because he killed him.

8¶ In the twenty and sixth year of Asa king of Judah began Elah the son of Baasha to reign over Israel in Tirzah, two years. 9And his servant Zimri, captain of half his chariots, conspired against him, as he was in Tirzah, drinking himself drunk in the house of Arza steward of his house in Tirzah.16.9 steward…: Heb. which was over 10And Zimri went in and smote him, and killed him, in the twenty and seventh year of Asa king of Judah, and reigned in his stead.

11¶ And it came to pass, when he began to reign, as soon as he sat on his throne, that he slew all the house of Baasha: he left him not one that pisseth against a wall, neither of his kinsfolks, nor of his friends.16.11 neither…: or, both his kinsmen and his friends 12Thus did Zimri destroy all the house of Baasha, according to the word of the LORD, which he spake against Baasha by Jehu the prophet,16.12 by: Heb. by the hand of 13For all the sins of Baasha, and the sins of Elah his son, by which they sinned, and by which they made Israel to sin, in provoking the LORD God of Israel to anger with their vanities. 14Now the rest of the acts of Elah, and all that he did, are they not written in the book of the chronicles of the kings of Israel?

15¶ In the twenty and seventh year of Asa king of Judah did Zimri reign seven days in Tirzah. And the people were encamped against Gibbethon, which belonged to the Philistines. 16And the people that were encamped heard say, Zimri hath conspired, and hath also slain the king: wherefore all Israel made Omri, the captain of the host, king over Israel that day in the camp. 17And Omri went up from Gibbethon, and all Israel with him, and they besieged Tirzah. 18And it came to pass, when Zimri saw that the city was taken, that he went into the palace of the king’s house, and burnt the king’s house over him with fire, and died, 19For his sins which he sinned in doing evil in the sight of the LORD, in walking in the way of Jeroboam, and in his sin which he did, to make Israel to sin. 20Now the rest of the acts of Zimri, and his treason that he wrought, are they not written in the book of the chronicles of the kings of Israel?

21¶ Then were the people of Israel divided into two parts: half of the people followed Tibni the son of Ginath, to make him king; and half followed Omri. 22But the people that followed Omri prevailed against the people that followed Tibni the son of Ginath: so Tibni died, and Omri reigned.

23¶ In the thirty and first year of Asa king of Judah began Omri to reign over Israel, twelve years: six years reigned he in Tirzah. 24And he bought the hill Samaria of Shemer for two talents of silver, and built on the hill, and called the name of the city which he built, after the name of Shemer, owner of the hill, Samaria.16.24 Samaria: Heb. Shomeron

25¶ But Omri wrought evil in the eyes of the LORD, and did worse than all that were before him. 26For he walked in all the way of Jeroboam the son of Nebat, and in his sin wherewith he made Israel to sin, to provoke the LORD God of Israel to anger with their vanities. 27Now the rest of the acts of Omri which he did, and his might that he shewed, are they not written in the book of the chronicles of the kings of Israel? 28So Omri slept with his fathers, and was buried in Samaria: and Ahab his son reigned in his stead.

29¶ And in the thirty and eighth year of Asa king of Judah began Ahab the son of Omri to reign over Israel: and Ahab the son of Omri reigned over Israel in Samaria twenty and two years. 30And Ahab the son of Omri did evil in the sight of the LORD above all that were before him. 31And it came to pass, as if it had been a light thing for him to walk in the sins of Jeroboam the son of Nebat, that he took to wife Jezebel the daughter of Ethbaal king of the Zidonians, and went and served Baal, and worshipped him.16.31 as if…: Heb. was it a light thing, etc 32And he reared up an altar for Baal in the house of Baal, which he had built in Samaria. 33And Ahab made a grove; and Ahab did more to provoke the LORD God of Israel to anger than all the kings of Israel that were before him.

34¶ In his days did Hiel the Beth-elite build Jericho: he laid the foundation thereof in Abiram his firstborn, and set up the gates thereof in his youngest son Segub, according to the word of the LORD, which he spake by Joshua the son of Nun.