1 Mafumu 15 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 15:1-34

Abiya Mfumu ya Yuda

1Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Nebati, Abiya anakhala mfumu ya Yuda, 2ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zitatu. Amayi ake anali Maaka, mwana wa Abisalomu.

3Abiya anachita zoyipa zonse zimene abambo ake anazichita. Sanali wangwiro pamaso pa Yehova Mulungu wake, monga linachitira kholo lake Davide. 4Komabe chifukwa cha Davide, Yehova Mulungu wake anamupatsa nyale mu Yerusalemu pomupatsa mwana wolowa mʼmalo mwake ndi kumukhazikitsa kukhala wamphamvu mu Yerusalemu; 5pakuti Davide anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo sanalephere kusunga chilichonse chimene Yehova anamulamula masiku onse a moyo wake kupatula nkhani ija ya Uriya Mhiti.

6Panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu masiku onse a moyo wa Abiya. 7Tsono ntchito zina za Abiya, ndi zina zonse anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yeroboamu. 8Ndipo Abiya anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Asa, mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Asa Mfumu ya Yuda

9Mʼchaka cha makumi awiri cha Yeroboamu mfumu ya Israeli, Asa anakhala mfumu ya Yuda, 10ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 41. Agogo ake akazi anali Maaka mwana wa Abisalomu.

11Asa anachita zolungama pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake. 12Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zadama pochita chipembedzo chawo ndiponso anachotsa mafano onse amene makolo ake anawapanga. 13Iye anachotsanso gogo wake Maaka pa udindo wake wa amayi a mfumu, chifukwa choti anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo nakalitentha ku Chigwa cha Kidroni. 14Ngakhale sanachotse malo opembedzerapo mafano, mtima wa Asa unali wodzipereka kwathunthu kwa Yehova masiku onse a moyo wake. 15Asa anabweretsa ku Nyumba ya Yehova zinthu zimene abambo ake anazipereka, ndiponso zinthu zimene iye mwini anazipereka: zagolide, siliva ndi ziwiya zotengera.

16Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli nthawi yonse ya ulamuliro wawo. 17Baasa mfumu ya Israeli anapita kukathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo anamangira linga mzinda wa Rama kuletsa kuti wina aliyense asatuluke kapena kulowa mʼdziko la Asa, mfumu ya Yuda.

18Tsono Asa anatenga siliva yense pamodzi ndi golide zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso ku nyumba yake yaufumu. Anazipereka kwa atumiki ake, nawatuma kupita nazo kwa Beni-Hadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni, mfumu ya Aramu, amene ankakhala ku Damasiko ndipo anakamuwuza kuti, 19“Tiyeni tigwirizane inu ndi ine, monga panali mgwirizano pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Onani, ndikukutumizirani mphatso za siliva ndi golide. Tsopano kathetseni mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti andisiye.”

20Choncho Beni-Hadadi anamvera zimene ananena mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira magulu ake ankhondo ku mizinda ya Israeli. Ndipo iye anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Beti-Maaka ndi dera lonse la Kinereti kuphatikiza dziko lonse la Nafutali. 21Baasa atamva zimenezi, anasiya kumangira linga Rama ndipo anakakhala ku Tiriza. 22Pamenepo Mfumu Asa analamula anthu onse a ku Yuda osasiya ndi mmodzi yemwe, ndipo anachotsa ku Rama miyala ndi matabwa amene Baasa ankamangira kumeneko. Zipangizo zimenezi Mfumu Asa inamangira linga la Geba ku Benjamini ndi la ku Mizipa.

23Tsono ntchito zina za Asa, za mphamvu zake ndi mizinda imene anayimanga ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Koma pa nthawi ya ukalamba wake anadwala nthenda ya mapazi. 24Ndipo Asa anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide kholo lake. Ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Nadabu Mfumu ya Israeli

25Nadabu, mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli mʼchaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri. 26Nadabu anachita zoyipa pamaso pa Yehova, anayenda mʼnjira za abambo ake ndi mu uchimo womwe anachimwitsa nawo Israeli.

27Baasa mwana wa Ahiya, wa banja la Isakara anakonzera Nadabuyo chiwembu, ndipo anamukantha ku Gibetoni, mzinda wa Afilisti, pamene Nadabu ndi anthu onse a ku Israeli anali atawuzungulira. 28Baasa anapha Nadabu mʼchaka chachitatu cha Asa, mfumu ya ku Yuda ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.

29Iye atangoyamba kulamulira, anapha anthu onse a banja la Yeroboamu. Sanasiye ndi mmodzi yemwe wamoyo pa banjapo, koma anawononga anthu onse, molingana ndi mawu a Yehova amene anayankhula mwa mtumiki wake Ahiya wa ku Silo 30chifukwa cha machimo amene Yeroboamu anachita, ndiponso kuchimwitsa anthu a ku Israeli, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israeli.

31Tsono ntchito za Nadabu ndi zina zonse zimene anazichita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 32Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli pa nthawi yonse ya ulamuliro wawo.

Baasa Mfumu ya Israeli

33Chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Baasa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Aisraeli onse ku Tiriza, ndipo analamulira zaka 24. 34Anachita zoyipa pamaso pa Yehova, nayenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchita tchimo lake limene linachimwitsa anthu a ku Israeli.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

列王纪上 15:1-34

亚比央做犹大王

1尼八的儿子耶罗波安王执政第十八年,亚比央登基做犹大王, 2他在耶路撒冷执政三年,母亲是押沙龙的女儿玛迦

3亚比央和他父亲一样作恶多端,没有像他祖先大卫一样忠于他的上帝耶和华。 4但他的上帝耶和华因为大卫的缘故,仍然让他儿子在耶路撒冷继位,使耶路撒冷坚立。 5除了乌利亚事件以外,大卫一生都做耶和华视为正的事,没有违背耶和华的任何命令。

6罗波安耶罗波安之间常有战事,一直延续到亚比央王朝。 7亚比央耶罗波安之间也常有战事。亚比央其他的事及其一切所作所为都记在犹大的列王史上。 8亚比央与祖先同眠后葬在大卫城,他儿子亚撒继位。

亚撒做犹大王

9耶罗波安以色列王第二十年,亚撒登基做犹大王, 10他在耶路撒冷执政四十一年。他祖母是押沙龙的女儿玛迦11亚撒效法他祖先大卫,做耶和华视为正的事。 12他从国中驱逐了男庙妓,清除了他祖先制造的一切神像。 13亚撒还废除了他祖母玛迦的太后之位,因为她造了可憎的亚舍拉神像。亚撒把她的神像砍倒,放在汲沦溪烧掉。 14虽然他没有拆毁丘坛,但他一生忠于耶和华。 15他又把他父亲和他自己所献上的金银和器皿都带到耶和华的殿里。

16亚撒以色列巴沙之间常有争战。 17以色列巴沙上来攻打犹大,他修筑拉玛城,企图隔断犹大亚撒与外界的联系。 18于是,亚撒把耶和华殿里和王宫库房里剩余的金银交给臣仆,派他们送给大马士革亚兰王,即他伯利们的儿子、希旬的孙子便·哈达,说: 19“我们之间应立盟约,像我们的父亲之间立约一样,现在奉上金银为礼,请你取消与以色列巴沙立的盟约。这样,他就会从我境内退兵。” 20便·哈达接受了亚撒王的提议,派将领攻打以色列的城邑,攻占了以云亚伯·伯·玛迦基尼烈全境和拿弗他利全境。 21巴沙闻讯,就停止修筑拉玛,退回得撒去了。 22亚撒王令全国的犹大人出动,将巴沙修筑拉玛城的石头和木材搬走,用来修建便雅悯迦巴米斯巴23亚撒其他的事迹、功业和他兴建的城邑都记在犹大的列王史上。亚撒年老的时候,患了脚疾。 24他与祖先同眠后,葬在大卫城他的祖坟里。他儿子约沙法继位。

拿答做以色列王

25亚撒犹大王第二年,耶罗波安的儿子拿答登基做以色列王,执政两年。 26拿答像他父亲一样作恶多端,行耶和华视为恶的事,使以色列人陷入罪中。 27-28亚撒犹大王第三年,拿答以色列军围攻非利士基比顿城时,以萨迦支派亚希雅的儿子巴沙叛变,杀了拿答,篡位称王。 29巴沙一做王,立刻诛杀耶罗波安全家,无一幸免,应验了耶和华借祂仆人——示罗亚希雅所说的话。 30这是因为耶罗波安犯罪,并使以色列人陷入罪中,惹以色列的上帝耶和华发怒。 31拿答其他的事及其一切所作所为都记在以色列的列王史上。 32亚撒以色列巴沙执政期间,双方常常争战。

巴沙做以色列王

33犹大亚撒执政第三年,亚希雅的儿子巴沙得撒登基做以色列王,执政二十四年。 34他步耶罗波安的后尘,做耶和华视为恶的事,使以色列人陷入罪中。