1 Mafumu 10 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 10:1-29

Mfumu Yayikazi ya ku Seba Ibwera Kudzacheza ndi Solomoni

1Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni ndi za ubale wake ndi Yehova, inabwera kudzamuyesa ndi mafunso okhwima. 2Inafika mu Yerusalemu ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake. 3Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo. 4Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru zonse za Solomoni ndiponso nyumba yaufumu imene anamanga, 5chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo, atumiki opereka zakumwa, ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.

6Iyo inati kwa mfumu, “Mbiri imene ndinamva ndili ku dziko kwathu ya zomwe munachita komanso nzeru zanu ndi yoona. 7Koma sindinakhulupirire zinthu zimenezo mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe, pakuti nzeru ndi chuma zimene muli nazo zaposa zimene ndinamva. 8Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu! 9Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando waufumu wa Israeli. Chifukwa cha chikondi chake chamuyaya pa Israeli, wayika inu kuti mukhale mfumu kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”

10Ndipo mfumu yayikaziyo inapatsa Solomoni golide wolemera makilogalamu 4,000, zokometsera zakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yokongola. Sikunabwerenso zokometsera zakudya ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapatsa Mfumu Solomoni.

11(Ndiponso sitima zapamadzi za Hiramu zinabweretsa golide wochokera ku Ofiri. Ndipo kuchokera kumeneko kunabweranso mitengo yambiri ya alimugi ndi miyala yokongola. 12Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya alimugi ngati yochirikizira Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndipo anapangiranso azeze ndi apangwe a anthu oyimba. Mitengo yotere sinayitanitsidweponso kapena kuoneka mpaka lero lino).

13Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha, osawerengera mphatso zaufumu zimene anali atamupatsa. Choncho inabwerera ku dziko la kwawo pamodzi ndi atumiki ake.

Chuma ndi Ulemerero wa Solomoni

14Golide amene Solomoni ankalandira pa chaka ankalemera makilogalamu 23,000, 15osawerengera misonkho imene anthu odzacheza ndi amalonda amapereka. Golide wina ankachokera kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi kwa abwanamkubwa a mʼdzikomo.

16Mfumu Solomoni anapanga zishango zikuluzikulu 200 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu ndi theka. 17Anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera kilogalamu imodzi ndi theka. Ndipo mfumu inayika zishangozo mʼnyumba yake yotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni.

18Mfumu inapangitsanso mpando waufumu waukulu wa minyanga ya njovu, ndipo inawukutira ndi golide wabwino kwambiri. 19Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndipo chotsamira chake chinali chozungulira pamwamba pake. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, pamodzi ndi chifaniziro cha mkango mbali iliyonse. 20Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi limodziwo; mkango umodzi mbali iliyonse ya makwererowa. Mpando woterewu sunapangidwepo mu ufumu wina uliwonse. 21Zomwera zonse za Mfumu Solomoni zinali zagolide, ziwiya zonse za Nyumba Yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide weniweni. Panalibe chimene chinapangidwa ndi siliva chifukwa siliva sankayesedwa kanthu pa nthawi ya Solomoni. 22Mfumu inali ndi sitima zapamadzi zomwe zinali pa nyanja pamodzi ndi sitima za Hiramu. Kamodzi pakapita zaka zitatu zinkabwera zitanyamula golide, siliva ndi minyanga ya njovu, anyani ndi apusi.

23Mfumu Solomoni inali yopambana pa chuma ndi pa nzeru kuposa mafumu ena onse pa dziko lapansi. 24Anthu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuyankhulana ndi Solomoni kuti amve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake. 25Chaka ndi chaka aliyense amene amabwera ankabweretsa mphatso za siliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya, akavalo ndi abulu.

26Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndiponso oyendetsa akavalo 12,000, zimene anazisunga mʼmizinda ya magaleta ndiponso mu Yerusalemu. 27Mfumu inachititsa kuti siliva akhale ngati miyala wamba mu Yerusalemu, ndipo mkungudza unali wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya mʼmbali mwa phiri. 28Akavalo a Solomoni ankachokera ku Igupto komanso ku Kuwe. Anthu a malonda a mfumu ankatengera akavalowo ku Kuwe. 29Ankagula magaleta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo akavalo pa mtengo wa masekeli 150. Anthu amalondawo ankagulitsa zimenezi kwa mafumu onse a Ahiti ndi Asiriya.

Священное Писание

3 Царств 10:1-29

Царица Шевы посещает Сулеймана

(2 Лет. 9:1-12)

1Когда царица Шевы услышала о славе Сулеймана, связанной с именем Вечного, она явилась, чтобы испытать его трудными вопросами. 2Прибыв в Иерусалим с огромной свитой, с верблюдами, везущими пряности и великое множество золота и драгоценных камней, она пришла к Сулейману и говорила с ним обо всём, что было у неё на сердце. 3Сулейман ответил на все её вопросы: для царя не было ничего трудного, чего он не смог бы ей объяснить. 4Когда царица Шевы увидела всю мудрость Сулеймана и дворец, который он построил, увидела, 5что за яства у него на столе, что за жилища у его приближённых, как прислуживают его слуги, как они одеты, каковы его виночерпии и какие всесожжения он совершает в храме Вечного10:5 Или: «и какова лестница, по которой он поднимается в храм Вечного»., у неё захватило дух.

6Она сказала царю:

– Молва, которую я слышала в своей стране о твоих делах и мудрости, правдива, 7но я не верила слухам, пока не пришла и не увидела это своими глазами. И что же, мне не рассказали и половины: твои мудрость и богатство далеко превзошли ту молву, что я слышала! 8Благословенны твои люди! Благословенны твои приближённые, которые всегда стоят перед тобой и внимают твоей мудрости! 9Хвала Вечному, твоему Богу, Который благоволил к тебе, посадив тебя на престол Исраила! Ради Своей любви, бесконечной любви Вечного к Исраилу, Он сделал тебя царём, чтобы ты поступал справедливо и праведно.

10Она подарила царю четыре тысячи триста двадцать килограммов10:10 Букв.: «сто двадцать талантов». золота, великое множество пряностей и драгоценных камней. Никогда больше пряностей не привозили в таком изобилии, как тогда, когда царица Шевы подарила их Сулейману.

11(А Хирамовы корабли, что привозили золото из Офира, привезли оттуда большое количество красного дерева и драгоценных камней. 12Царь сделал из красного дерева опоры для храма Вечного и царского дворца, а также арфы и лиры для музыкантов. Такого количества красного дерева никогда не привозилось ни до, ни после этого дня.)

13Царь Сулейман подарил царице Шевы всё, что она пожелала и о чём просила, не считая того, что он подарил ей по своей царской щедрости. После этого она вернулась со свитой в свою страну.

Богатство и великолепие Сулеймана

(2 Лет. 1:14-17; 9:13-28)

14Ежегодно Сулейман получал почти двадцать четыре тонны10:14 Букв.: «шестьсот шестьдесят шесть талантов». золота, 15не считая того дохода, что поступал от купцов и торговцев, от всех царей Аравии и наместников страны.

16Царь Сулейман сделал двести больших щитов из кованого золота, на каждый из которых пошло по три с половиной килограмма10:16 Букв.: «шестьсот бек». золота. 17Ещё он сделал триста маленьких щитов из кованого золота, на каждый из которых ушло почти по два килограмма10:17 Букв.: «три мины». золота. Царь поместил их во дворце Ливанского леса.

18Ещё царь сделал огромный трон, выложенный слоновой костью и покрытый чистым золотом. 19У трона было шесть ступенек, а спинка его закруглялась кверху. По обеим сторонам сиденья были подлокотники, и у каждого из них стояло по льву. 20Двенадцать львов стояло на шести ступеньках – по одному с каждой стороны каждой ступеньки. Никогда ничего подобного не делалось ни в каком другом царстве.

21Все чаши царя Сулеймана были золотыми, и вся домашняя утварь во дворце Ливанского леса была из чистого золота. Серебряного ничего не было, потому что серебро в дни Сулеймана не ценилось.

22На море у царя был флот из торговых кораблей10:22 Букв.: «фарсисских кораблей»., наравне с кораблями Хирама. Раз в три года корабли возвращались, привозя золото, серебро, слоновую кость, обезьян и павлинов.

23Царь Сулейман превосходил богатством и мудростью всех царей земли. 24Все на земле искали встречи с Сулейманом, чтобы послушать мудрости, которую вложил в его сердце Всевышний. 25Всякий приходящий приносил дары – изделия из серебра и золота, одежды, оружие и пряности, лошадей и мулов, и так – из года в год.

26Сулейман преумножал количество своих колесниц и коней. У него было тысяча четыреста колесниц и двенадцать тысяч коней10:26 Или: «колесничих»; или: «всадников»., которые он держал в специально назначенных городах и у себя в Иерусалиме. 27В его правление серебро в Иерусалиме ценилось не выше простых камней, а кедра было так же много, как тутовых деревьев в предгорьях Иудеи. 28Кони Сулеймана поставлялись из Египта10:28 Или, возможно: «из Муцура». Муцур – область в Киликии, находившейся на севере от Исраила, на юге современной территории Турции. Также в ст. 29. и из Кувы – царские купцы покупали их в Куве. 29Колесницу привозили из Египта за семь килограммов серебра, а коня – почти за два килограмма10:29 Букв.: «шестьсот… сто пятьдесят шекелей».. Так же, через царских купцов, их доставляли всем царям хеттов и сирийцев.