1 Mafumu 1 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 1:1-53

Adoniya Adziyika Kukhala Mfumu

1Mfumu Davide atakalamba sankamva kufunda ngakhale akamufunditsa mabulangeti. 2Choncho nduna zake zinamuwuza kuti, “Tiloleni tifune namwali woti azikhala nanu ndi kumakusamalirani. Namwaliyo azigona pafupi nanu kuti mbuye wathu mfumu muzimva kufundira.”

3Kotero anafunafuna mʼdziko lonse la Israeli mtsikana wokongola ndipo anapeza Abisagi wa ku Sunemu, nabwera naye kwa mfumu. 4Mtsikanayo anali wokongola kwambiri ndipo ankasamalira mfumu ndi kumayitumikira, koma mfumuyo sinakhale naye malo amodzi.

5Nthawi imeneyi Adoniya, mwana wa Hagiti, anayamba kudzitukumula ndipo anati, “Ndidzakhala mfumu ndine.” Choncho anadzikonzera galeta ndi akavalo, pamodzi ndi anthu 50 woti azithamanga patsogolo pake. 6(Abambo ake sanalowererepo nʼkamodzi komwe ndipo sanafunsepo kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?” Adoniyayo anali wokongola kwambiri ndipo anali wopondana ndi Abisalomu).

7Adoniya anagwirizana ndi Yowabu mwana wa Zeruya ndiponso Abiatara wansembe, ndipo iwowa anamuthandiza. 8Koma Zadoki wansembe, Benaya mwana wa Yehoyada, mneneri Natani, Simei ndi Rei ndiponso asilikali amphamvu a Davide sanamutsate Adoniya uja.

9Kenaka Adoniya anapereka nsembe za nkhosa ndi ngʼombe ndiponso ana angʼombe onenepa ku Mwala wa Zohereti kufupi ndi Eni Rogeli. Iye anayitana abale ake onse, ana aamuna a mfumu ndiponso akuluakulu onse a ku Yuda, 10koma sanayitane mneneri Natani kapena Benaya kapenanso asilikali amphamvu a Davide ngakhalenso mʼbale wake Solomoni.

11Pamenepo Natani anafunsa Batiseba, amayi ake a Solomoni, kuti, “Kodi simunamve kuti Adoniya, mwana wa Hagiti, walowa ufumu popanda Davide mbuye wathu kudziwa? 12Tsopano ine ndikulangizeni inu mmene mungapulumutsire moyo wanu ndi moyo wa mwana wanu Solomoni. 13Pitani msanga kwa Mfumu Davide ndipo mukanene kuti, ‘Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbire kwa ine mdzakazi wanu kuti, ‘Ndithu mwana wako Solomoni ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwanga, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu?’ Nanga nʼchifukwa chiyani Adoniya walowa ufumu?’ 14Pamene inu muzikayankhula ndi mfumu, ine ndidzalowa ndi kuchitira umboni mawu anuwo.”

15Choncho Batiseba anapita nakalowa ku chipinda kukaonana ndi mfumu imene inali itakalamba kwambiri, kumene Abisagi wa ku Sunemu uja ankayisamalira. 16Batiseba anagwada nalambira mfumu.

Mfumu inamufunsa kuti, “Kodi nʼchiyani chimene ukufuna?”

17Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga, inu mwini munalumbira kwa ine mdzakazi wanu mʼdzina la Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwa ine, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu.’ 18Koma tsopano Adoniya ndiye walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu, simukuzidziwa zimenezi. 19Ndipo wapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndi nkhosa ndi mbuzi ndipo wayitana ana anu onse, wansembe Abiatara ndiponso Yowabu mkulu wa ankhondo, koma sanayitane kapolo wanu Solomoni. 20Mbuye wanga mfumu, maso a Aisraeli onse ali pa inu, kuti adziwe kuchokera kwa inu amene adzakhala pa mpando waufumu wa mbuye wanga mʼmalo mwanu. 21Mukapanda kutero, mbuye wanga, mukadzangotisiya nʼkulondola kumene kunapita makolo anu, ine pamodzi ndi mwana wangayu Solomoni adzatiyesa owukira.”

22Pamene Batiseba amayankhula ndi mfumu, mneneri Natani analowa. 23Ndipo anthu anawuza mfumu kuti, “Kwabwera mneneri Natani.” Kotero iye anafika pamaso pa mfumu ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi.

24Natani anafunsa kuti, “Mbuye wanga mfumu, kodi mwalengeza kuti Adoniya adzakhala mfumu mʼmalo mwanu, ndi kuti adzakhala pa mpando wanu waufumu? 25Lero lomwe lino wakapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndiponso nkhosa ndi mbuzi. Iye wayitana ana anu onse, atsogoleri a nkhondo, ndiponso wansembe Abiatara. Panopa onsewa akudya ndi kumwa naye ndipo akunena kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Adoniya!’ 26Koma ine kapolo wanu, wansembe Zadoki ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso kapolo wanu Solomoni sanatiyitane. 27Kodi zimenezi mbuye wanga mfumu mwazichita ndinu, osawawuza atumiki anu kuti adziwe amene adzakhale pa mpando waufumu mʼmalo mwanu?”

Davide Alonga Ufumu Solomoni

28Pamenepo mfumu Davide anati, “Muyitaneni Batiseba.” Kotero Batiseba analowa ndipo anayimirira pamaso pa mfumu.

29Tsono mfumu inalumbira kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene anandipulumutsa ine ku mavuto onse, 30ndithu ine lero ndichita zonse zimene ndinalumbira kwa Yehova Mulungu wa Israeli kuti, mwana wako Solomoni adzakhala mfumu mʼmalo mwanga ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu.”

31Pamenepo Batiseba anawerama, nagunditsa mutu wake pansi nalambira mfumu, ndipo anati, “Mbuye wanga Mfumu Davide mukhale ndi moyo wautali!”

32Mfumu Davide anati, “Ndiyitanireni wansembe Zadoki, mneneri Natani ndi Benaya mwana wa Yehoyada.” Atafika pamaso pa mfumu, 33mfumuyo inati kwa iwo, “Tengani atumiki anga ndipo mukweze mwana wanga Solomoni pa bulu wanga ndipo mupite naye ku Gihoni. Mukalize lipenga ndi kufuwula kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Solomoni!’ 34Kumeneko Zadoki wansembe ndi mneneri Natani akamudzoze kuti akhale mfumu ya Israeli. Kenaka mukalize lipenga ndi kumanena kuti ‘Akhale ndi moyo wautali Mfumu Solomoni.’ 35Ndipo pobwera muzikamutsata pambuyo. Iyeyo akabwere kuno ndi kudzakhala pa mpando wanga waufumu ndi kudzalamulira mʼmalo mwanga. Ndamusankha kukhala wolamulira Israeli ndi Yuda.”

36Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu kuti, “Ameni! Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu akhazikitse kuti zichitike motero. 37Monga momwe Yehova wakhalira ndi inu mbuye wanga mfumu, momwemonso akhale ndi Solomoni ndi kukhazikitsa ufumu wake kuti ukhale waukulu kuposa ufumu wa mbuye wanga Mfumu Davide!”

38Kotero Zadoki wansembe, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndiponso Apeleti, anthu oteteza mfumu, anapita kukamukweza Solomoni pa bulu wa Mfumu Davide ndi kupita naye ku Gihoni. 39Wansembe Zadoki anatenga nyanga ya mafuta yochokera ku malo opatulika ndi kumudzoza Solomoni. Kenaka analiza lipenga ndipo anthu onse anafuwula kuti, “Akhale ndi moyo wautali Mfumu Solomoni!” 40Ndipo anthu onsewo anapita namutsatira pambuyo akuyimba zitoliro ndi kukondwerera kwambiri, kotero nthaka inagwedezeka chifukwa cha phokoso lawo.

41Adoniya pamodzi ndi anthu onse oyitanidwa amene anali naye anamva zimenezi pamene ankamaliza madyerero awo. Atamva kulira kwa malipenga, Yowabu anafunsa kuti, “Kodi phokoso lonselo mu mzindamo likutanthauza chiyani?”

42Iye akuyankhula, Yonatani mwana wa wansembe Abiatara anafika. Adoniya anati, “Lowa. Munthu wabwino ngati iwe ayenera kubweretsa nkhani yabwino.”

43Yonatani anayankha Adoniya kuti, “Ayi ndithu, zinthu sizili bwino! Mbuye wathu Mfumu Davide walonga Solomoni ufumu. 44Mfumu yatuma Zadoki wansembe, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndi Apeleti ku Gihoni ndipo iwo amukweza pa bulu wa mfumu, 45ndipo Zadoki wansembe ndi mneneri Natani adzoza Solomoni ku Gihoni kuti akhale mfumu. Ndipo kuchokera kumeneko akhala akululutira, kotero kuti mu mzinda monse muli phokoso lokhalokha. Ndiyetu phokoso limene mukulimvalo. 46Ndipo Solomoni wakhala kale pa mpando wake waufumu. 47Kuwonjezera pamenepo, nduna za mfumu zabwera kale kudzayamika mbuye wathu Mfumu Davide, pomanena kuti, ‘Mulungu wanu atchukitse dzina la Solomoni kuposa dzina lanu ndipo ufumu wake ukule kupambana ufumu wanu!’ Ndipo mfumu inawerama niyamba kupembedza pa bedi lake, 48inati, ‘Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, amene wasankha wolowa mʼmalo mwanga ine ndikanali ndi moyo lero lino.’ ”

49Anthu onse amene Adoniya anawayitana ananjenjemera ndi mantha, ndipo anayimirira, kenaka anamwazikana. 50Koma Adoniya, poopa Solomoni, anapita ku Nyumba ya Mulungu nakagwira msonga za guwa lansembe. 51Tsono Solomoni anawuzidwa kuti, “Adoniya akukuopani inu Mfumu Solomoni ndipo wagwira msonga za guwa lansembe. Iye akuti, ‘Mfumu Solomoni alumbire kuti sadzapha kapolo wake ndi lupanga.’ ”

52Solomoni anayankha kuti, “Ngati iyeyo aonetse kuti ndi munthu wakhalidwe labwino, ngakhale tsitsi la mʼmutu mwake silidzathothoka ndi kugwera pansi, koma akapezeka kuti ali ndi khalidwe loyipa, adzafa ndithu.” 53Pamenepo Mfumu Solomoni inatuma anthu ndipo anakamutenga paguwa paja. Adoniya anabwera ndi kudzalambira Mfumu Solomoni, ndipo Solomoni anati, “Pita ku nyumba yako.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

列王紀上 1:1-53

王位之爭

1大衛王年紀老邁,雖然蓋了幾層被子,仍然覺得冷。 2他的臣僕建議:「不如選一位少女進宮伺候、照顧我主我王,讓她睡在王懷中給王取暖。」

3於是,他們在以色列全國尋找美貌女子,找到了一位名叫雅比莎書念少女,把她帶到王那裡。 4這女子長得花容月貌,她照顧、伺候王,但王沒有與她同房。

5那時,哈姬的兒子亞多尼雅妄自尊大,說:「我必做王。」他為自己製備了車輛和騎兵,派五十人在前面開路。 6他父親從不干涉、責問他:「你這是做什麼?」他是押沙龍的弟弟,長得英俊非凡。

7亞多尼雅洗魯雅的兒子約押及祭司亞比亞他商議,二人都答應支持他。 8不過,撒督祭司、耶何耶大的兒子比拿雅拿單先知、示每利以大衛的勇士卻沒有跟隨他。

9一天,亞多尼雅隱·羅結附近的瑣希列磐石那裡宰了牛羊和肥牛犢獻祭,並邀請了眾王子和猶大的群臣。 10可是他沒有邀請拿單先知、比拿雅大衛的勇士和他的兄弟所羅門

11拿單所羅門的母親拔示芭說:「你沒有聽說嗎?哈姬的兒子亞多尼雅做王了,我們的主大衛還不知道。 12事到如今,我有一個主意,可以保住你和你兒子所羅門的性命。 13你去見大衛王,對他說,『我主我王啊,你不是起誓說讓臣妾的兒子所羅門繼承王位嗎?怎麼現在亞多尼雅做了王呢?』 14你跟王說話的時候,我會進去證實你的話。」

15拔示芭就進內室去見年邁的王,書念的少女雅比莎正在伺候他。 16拔示芭向王屈身下拜。王問道:「你有什麼事嗎?」 17拔示芭回答說:「我主啊,你曾經憑你的上帝耶和華起誓說讓臣妾的兒子所羅門繼承你的王位,坐你的寶座。 18但現在亞多尼雅已經稱王了,我主我王還不知道。 19他宰了許多牛羊和肥牛犢獻祭,邀請眾王子、亞比亞他祭司和約押元帥,卻沒有邀請你的僕人所羅門20我主我王啊!以色列舉國拭目以待,等著王來指定誰繼承王位。 21不然,到我主我王與祖先同眠之後,我和我兒所羅門必被定為罪人。」

22她與王正說話間,拿單先知進宮來了。 23有人奏告王,說:「拿單先知來了。」拿單來到王面前,俯伏在地, 24說:「我主我王啊,你已經宣佈讓亞多尼雅繼承你的王位,坐你的寶座嗎? 25他今天宰了許多牛羊和肥犢獻祭,宴請眾王子、將領和亞比亞他祭司,他們正在他那裡一邊吃喝一邊說,『亞多尼雅王萬歲!』 26但他沒有邀請臣僕我、撒督祭司、耶何耶大的兒子比拿雅和你的僕人所羅門27這是我主我王的旨意嗎?王還沒有對臣僕們說過誰繼承王位。」

28於是,大衛王召見拔示芭拔示芭立刻晉見,侍立在王面前。 29王起誓說:「我憑救我脫離一切苦難的永活的耶和華起誓, 30我今天必實現我憑以色列的上帝耶和華向你起的誓。你的兒子所羅門必繼承王位,坐在我的寶座上。」

31拔示芭就向王俯伏下拜說:「我主我王萬歲!」

32大衛王又召見撒督祭司、拿單先知和耶何耶大的兒子比拿雅。他們都來到王面前。 33王囑咐道:「你們要率領我的隨從,讓我兒所羅門騎上我的騾子,護送他下到基訓34撒督祭司和拿單先知要在那裡膏立他為以色列王。你們要吹響號角,高喊,『所羅門王萬歲!』 35然後,你們要隨他回來,他要登基,繼承我的王位。我已立他做以色列猶大的君王了。」

36耶何耶大的兒子比拿雅說:「遵命,願我主我王的上帝耶和華成全這事。 37耶和華怎樣與我主我王同在,願祂也照樣與所羅門同在,使他的國比我主大衛王的國更強大。」 38於是,撒督祭司、拿單先知、耶何耶大的兒子比拿雅,以及基利提人和比利提人請所羅門騎上大衛王的騾子,護送他前往基訓39撒督祭司從聖幕裡拿來盛膏油的角,膏立所羅門為王。他們吹響號角,民眾高聲歡呼:「所羅門王萬歲!」 40眾人浩浩蕩蕩地隨著所羅門回京,一路上吹笛歡呼,聲音震動大地。 41亞多尼雅和他的眾賓客剛剛飲宴完畢,聽見了這聲音。約押聽見號角聲,便問:「城裡為什麼如此喧鬧?」 42就在這時候,亞比亞他祭司的兒子約拿單來了,亞多尼雅說:「進來!你是個忠勇的人,一定帶來了好消息。」

43約拿單說:「我們的主大衛王已經立所羅門為王了。 44王派撒督祭司、拿單先知、耶何耶大的兒子比拿雅,以及基利提人和比利提人護送所羅門騎上王的騾子。 45撒督祭司和拿單先知在基訓膏立他為王,他們一路上歡呼著回來了,全城轟動。你們聽到的就是他們的聲音。 46所羅門已經登基掌權, 47王的臣僕也來向我們的主大衛王道喜說,『願王的上帝使所羅門比王更聲名顯赫,使他的國比王的國更強大。』王在床上俯伏敬拜, 48說,『以色列的上帝耶和華當受稱頌,因為祂讓我親眼看見我的繼承人今天登基。』」

49亞多尼雅的眾賓客聽後,嚇得四散而去。 50亞多尼雅懼怕所羅門,就去抓住祭壇的角。 51有人告訴所羅門:「亞多尼雅懼怕王,現在正抓住祭壇的角,要王今天起誓不要殺他。」

52所羅門說:「如果他是個忠義的人,必毫髮無損;如果他作惡,必死無疑。」 53於是,所羅門王便派人去把亞多尼雅從祭壇上帶下來。亞多尼雅前來向所羅門王俯伏下拜,所羅門對他說:「你回家去吧。」