1 Atesalonika 5 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Atesalonika 5:1-28

Tsiku la Ambuye

1Tsono abale, za nthawi ndi nyengo yake nʼkosafunikira kuti tikulembereni, 2chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku. 3Pamene anthu akunena kuti, “Mtendere ndi chitetezo,” chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa.

4Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala. 5Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima. 6Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga. 7Pakuti amene akugona, amagona usiku, ndi amene amaledzera, amaledzera usiku. 8Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa. 9Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. 10Iye anatifera ndi cholinga chakuti, kaya tili ndi moyo kapena tagona, tikhale naye pamodzi. 11Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.

Malangizo Otsiriza

12Tsopano tikukupemphani abale kuti muziwalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene amakuyangʼanirani mwa Ambuye ndi amene amakulimbikitsani. 13Muziwachitira ulemu kwambiri mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo. Mukhale pa mtendere wina ndi mnzake. 14Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense. 15Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse.

16Kondwerani nthawi zonse. 17Pempherani kosalekeza. 18Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.

19Musazimitse moto wa Mzimu Woyera. 20Musanyoze mawu a uneneri. 21Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino. 22Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse.

23Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu. 24Amene anakuyitanani ndi wokhulupirika ndipo Iye adzachita zimenezi.

25Abale, mutipempherere. 26Perekani moni wachikondi kwa onse. 27Pamaso pa Ambuye ndikulamula kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.

28Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale nanu.