1 Atesalonika 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Atesalonika 4:1-18

Moyo Wokondweretsa Mulungu

1Potsiriza, abale, tinakulangizani kale momwe mukuyenera kukhalira kuti mukondweretse Mulungu, monga momwe mukukhaliramo. Tsopano tikukupemphani ndi kukulimbikitsani mwa Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale. 2Inu mukudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu.

3Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama; 4aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu, 5osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu. 6Pa zimenezi munthu asachimwire mʼbale wake kapena kumuonerera. Ambuye adzalanga anthu onse amene amachita machimo amenewa, monga tinakuwuzani kale ndi kukuchenjezani. 7Pakuti Mulungu sanatiyitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima. 8Choncho, aliyense amene akukana malangizo awa sakukana munthu koma Mulungu, Mulungu weniweniyo amene amakupatsani Mzimu Woyera.

9Tsono kunena za kukondana wina ndi mnzake, nʼkosafunikira kuti tikulembereni, popeza ndi Mulungu amene anakuphunzitsani za kukondana wina ndi mnzake. 10Ndipo kunena zoona, mumakonda abale onse a mʼbanja la Mulungu a ku Makedoniya. Komabe, abale tikukulimbikitsani kuti muzichita zimenezi koposa kale.

11Yesetsani kuti mukhale moyo wofatsa. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kugwira ntchito ndi manja ake. 12Mukatero akunja adzalemekeza makhalidwe anu a tsiku ndi tsiku, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.

Kubweranso kwa Ambuye

13Abale, ife sitikufuna mukhale osadziwa za amene akugona, kapena kumva chisoni ngati anthu ena opanda chiyembekezo. 14Ife timakhulupirira kuti Yesu anamwalira naukanso. Moteronso timakhulupirira kuti amene anamwalira ali mwa Yesu, Mulungu adzawaukitsa nʼkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo. 15Molingana ndi mawu a Ambuye mwini, tikukuwuzani kuti, ife amene tikanali ndi moyo, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sitidzawasiya kumbuyo amene anagona kale. 16Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba. 17Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya. 18Nʼchifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.