1 Atesalonika 2 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Atesalonika 2:1-20

Utumiki wa Paulo ku Atesalonika

1Abale, mukudziwa kuti kudzacheza kwathu kwa inu sikunali kosapindulitsa. 2Monga mukudziwa, ife nʼkuti titazunzika ndi kunyozedwa ku Filipi. Koma mothandizidwa ndi Mulungu wathu, tinalimba mtima mpaka kukulalikirani uthenga wake wabwino ngakhale ambiri ankatsutsana nafe. 3Pakuti kulalikira kumene tikuchita, sitikuchita ndi maganizo olakwika kapena zolinga zoyipa, kapenanso kufuna kukunamizani. 4Koma timayankhula monga anthu ovomerezeka ndi Mulungu ndi osungitsidwa Uthenga Wabwino. Ife sitikufuna kukondweretsa anthu koma Mulungu, amene amasanthula mitima yathu. 5Monga mukudziwa kuti sitinagwiritse ntchito mawu oshashalika kapena mtima wofuna phindu, Mulungu ndiye mboni yathu. 6Ife sitinafune kutamidwa ndi anthu, kapena ndi inu, kapena wina aliyense mwa inu. 7Ngati atumwi a Khristu tikanatha kukhala cholemetsa kwa inu, mʼmalo mwake tinali ngati ana aangʼono pakati panu.

Monga mmene amayi amasamalira ana awo angʼono, 8moteronso tinakusamalirani. Chifukwa tinakukondani kwambiri, tinali okondwa kugawana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso miyoyo yathu. 9Abale, pakuti mukumbukira kugwira ntchito kwathu kwambiri ndi kuvutika; ife tinagwira ntchito usana ndi usiku ndi cholinga chakuti tisakhale cholemetsa, kwa aliyense pamene ife tinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu.

10Inu ndinu mboni, ndiponso Mulungu, kuti tinali oyera mtima, olungama ndi wopanda chifukwa pakati panu amene munakhulupirira. 11Monga mudziwa kuti ife tinkasamala aliyense wa inu monga abambo amasamalira ana ake, 12kulimbikitsa, kutonthoza ndi kukupemphani kuti mukhale moyo oyenera Mulungu amene anakuyitanani kuti mulowe mu ufumu wake ndi ulemerero.

13Ndipo ifenso tikuyamika Mulungu kosalekeza chifukwa mutalandira Mawu a Mulungu, amene munawamva kuchokera kwa ife, munawalandira osati ngati mawu a anthu, koma monga momwe alili, Mawu a Mulungu, amene akugwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira. 14Pakuti inu abale, munakhala otsanzira mipingo ya Mulungu ya ku Yudeya, imene ili mwa Khristu Yesu. Munasautsidwa kuchokera kwa anthu a mtundu wanu, zinthu zomwezo zimene mipingo imeneyi inasautsidwa ndi Ayuda, 15amene anapha Ambuye Yesu ndi aneneri ndipo anatithamangitsanso ife. Iwo sakondweretsa Mulungu ndipo amadana ndi anthu onse 16ndikutiretsa ife kuti tisayankhule ndi a mitundu ina kuti angapulumuke. Motero iwo amadziwunjikira okha machimo awo. Mkwiyo wa Mulungu wa afikira tsopano.

Paulo Afunitsitsa Kuonanso Atesalonika

17Koma abale, titasiyana kwa nthawi pangʼono (mʼthupi osati mʼmaganizo), tinayesetsa koposa kuti tikuoneni. 18Pakuti ife tinafuna kubweranso kwa inu, makamaka ine Paulo, ndinayesa kangapo koma Satana anatiletsa. 19Nanga chiyembekezo chathu, chimwemwe chathu kapena chaufumu chimene ife tidzanyadira pamaso pa Ambuye athu Yesu Khristu pamene abwere ndi chiyani? Kodi si inu? 20Indedi, inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

帖撒罗尼迦前书 2:1-20

保罗在帖撒罗尼迦的工作

1弟兄姊妹,你们自己知道,我们那次探望你们并没有白费。 2你们也知道,我们之前在腓立比遭受了迫害和凌辱,遇到强烈的反对,但仍然靠着我们的上帝放胆向你们传扬祂的福音。 3我们的劝勉并非出于谬误、不良动机或诡诈。 4我们得到了上帝的认可,受委派传福音。我们不是要取悦人,而是要取悦鉴察我们内心的上帝。

5你们知道,我们没有花言巧语奉承人,也没有心存贪念,上帝可以为我们作证。 6我们不求得到你们或其他任何人的赞扬。 7身为基督的使徒,我们理当受到你们的尊重,然而我们像母亲抚育婴儿一样温柔地对待你们。 8我们深爱你们,对你们有深厚的感情,不仅乐意把上帝的福音传给你们,甚至把生命给你们也在所不惜。

9弟兄姊妹,你们一定记得我们的劳苦和艰难。我们一面向你们传福音,一面昼夜辛勤工作,免得成为你们任何人的负担。 10我们怎样以圣洁、公义、纯全的方式对待你们众信徒,你们自己可以作证,上帝也可以作证。 11你们也知道,我们对待你们就像父亲对待自己的孩子一样。 12我们安慰你们,劝勉你们,督促你们,好叫你们行事为人对得起上帝,祂呼召你们进入祂的国、享受祂的荣耀。

13我们不住地感谢上帝,因为你们从我们这里听了上帝的道后就接受了,确信这不是人的道理,而是上帝的道。这道正在你们信的人心里发挥作用。

14弟兄姊妹,你们的遭遇和犹太地区基督耶稣的众教会的遭遇一样。你们受到了自己同胞的迫害,他们也受到了犹太人的迫害。 15这些犹太人杀死了主耶稣和众先知,又迫害我们。他们不但冒犯上帝,还与所有的人为敌, 16阻止我们传福音给外族人,唯恐他们得救。这些人恶贯满盈,上帝的烈怒终于临到了他们头上。

保罗渴望去帖撒罗尼迦

17弟兄姊妹,我们暂时与你们分离,心灵却与你们在一起。我们非常渴望见到你们。 18我们想去你们那里,我保罗也一次又一次地想去,只是遭到撒旦的拦阻。 19我们主耶稣再来的时候,我们在祂面前的盼望、喜乐和可夸耀的冠冕是什么呢?不就是你们吗? 20因为你们是我们的荣耀和喜乐。