1 Atesalonika 1 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Atesalonika 1:1-10

1Paulo, Silivano ndi Timoteyo.

Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.

Chisomo ndi mtendere kwa inu.

Kuyamikira Chikhulupiriro cha Atesalonika

2Ife timayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu. Timakutchulani mʼmapemphero athu. 3Nthawi zonse timakumbukira ntchito yanu yachikhulupiriro, yachikondi ndi kupirira kwanu kwa chiyembekezo mwa Ambuye athu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.

4Abale okondedwa ndi Mulungu, tikudziwa kuti Mulungu anakusankhani, 5chifukwa uthenga wathu wabwino sunafike kwa inu ndi mawu okha, koma ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chachikulu. Mukudziwa mmene tinkakhalira pakati panu kuti tikuthandizeni. 6Inu mwakhala otitsatira athu ndi a Ambuye; ngakhale kuti panali masautso akulu, munalandira uthenga mwachimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera. 7Ndipo potero munakhala chitsanzo kwa abale onse a ku Makedoniya ndi Akaya. 8Kuchokera kwa inu, uthenga wa Ambuye unamveka ku Makedoniya ndi ku Akaya ndipo mbiri ya chikhulupiriro chanu mwa Mulungu yamveka ponseponse. Choncho sikofunikanso kuti tinene kanthu, 9pakuti iwo amafotokoza za momwe munatilandirira. Iwo amatiwuza za momwe munatembenukira kwa Mulungu kusiya mafano ndi kutumikira Mulungu wamoyo ndi woona. 10Ndipo mukudikira Mwana wake kuchokera kumwamba, Yesu, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwera.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

帖撒羅尼迦前書 1:1-10

1保羅西拉提摩太寫信給帖撒羅尼迦屬於父上帝和主耶穌基督的教會。

願恩典和平安歸給你們!

信徒的榜樣

2我們常常為你們眾人感謝上帝,為你們禱告, 3在我們的父上帝面前不斷地想到你們因信我們主耶穌基督而做的工作、因愛祂而受的勞苦和因祂所賜的盼望而激發的忍耐。

4上帝所愛的弟兄姊妹,我們知道上帝揀選了你們, 5因為我們傳福音給你們不只是靠言語,也靠上帝的能力、聖靈的同在和充分的確據。你們也知道,我們為了你們的緣故怎樣在你們中間行事為人。 6你們效法了我們和我們的主,儘管深受苦難,仍然懷著聖靈所賜的喜樂領受真道, 7成了馬其頓亞該亞所有信徒的榜樣。 8主的道從你們那裡不僅傳到了馬其頓亞該亞,還傳到了其他各地,你們對上帝的信心也廣為人知,我們無須再多說什麼。 9因為人們都在傳講你們如何接待我們,如何離棄偶像歸向上帝,事奉又真又活的上帝, 10等候祂的兒子從天降臨,就是祂使之從死裡復活、救我們脫離將來可怕審判1·10 可怕審判」希臘文是「烈怒」。的耶穌。