1 Akorinto 8 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Akorinto 8:1-13

Nyama ya Nsembe za Mafano

1Tsopano za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano: Ife tidziwa kuti tonse tili ndi chidziwitso. Komatu chidziwitso chokha chimadzitukumula, koma chikondi ndicho chimapindulitsa. 2Munthu amene amaganiza kuti amadziwa kanthu, ndiye kuti sakudziwa monga mmene amayenera kudziwira. 3Koma munthu amene amakonda Mulungu amadziwika ndi Mulunguyo.

4Choncho kunena za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano; ife tikudziwa kuti mafano si kanthu nʼpangʼonongʼono pomwe pa dziko lapansi, ndiponso kuti palibe Mulungu wina koma mmodzi yekha. 5Popeza kuti ngakhale pali yotchedwa milungu, kaya ndi kumwamba kapena pa dziko lapansi (poti ilipodi milungu yambirimbiri ndi ambuye ambirimbiri), 6koma kwa ife pali Mulungu mmodzi yekha, Atate, zinthu zonse zinachokera mwa Iye ndipo ndife ake. Komanso pali Ambuye mmodzi Yesu Khristu kumene zinthu zonse zinachokera ndipo mwa Iye ife tili ndi moyo.

7Koma saliyense amadziwa zimenezi. Alipo ena ozolowera mafano kwambiri mwakuti akadya chakudya chotere amaganiza kuti chakudyacho chinaperekedwa nsembe kwa mafano. Ndiye poti chikumbumtima chawo nʼchofowoka chimadetsedwadi. 8Koma chakudya sichitisendeza kufupi ndi Mulungu. Tikapanda kudya si vuto, tikadya sitisinthikanso.

9Komabe samalani kuti ufulu wanu ochita zinthu usafike pokhumudwitsa ofowoka. 10Pakuti ngati aliyense wachikumbumtima chofowoka akakuonani achidziwitsonu mukudya mʼnyumba yopembedzera mafano, kodi iyeyo sichidzamulimbitsa mtima kuti azidya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano? 11Kotero kuti chifukwa cha chidziwitso chanu mʼbale wofowokayu amene chifukwa cha iye, Khristu anafa, wawonongeka chifukwa cha chidziwitso chanu. 12Mukamachimwira abale anu motere ndikuwawonongera chikumbumtima chawo chofowokacho, mukuchimwira Khristu. 13Nʼchifukwa chake ngati zimene ine ndimadya zichititsa mʼbale wanga kugwa mu tchimo, sindidzadyanso chakudyacho kuti mʼbaleyo ndisamuchimwitse.