1 Akorinto 5 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Akorinto 5:1-13

Wachigololo Achotsedwe mu Mpingo

1Mbiri yamveka kuti pakati panu pakuchitika chigololo. Ndipo chigololo cha mtunduwu ngakhale pakati pa akunja sichingapezeke; munthu akumagonana ndi mkazi wa abambo ake. 2Ndipo inu mukudzitukumulabe. Kodi simukanayenera kudzazidwa ndi chisoni ndipo mukanamuchotsa pa chiyanjano chanu munthu wochita zimenezi? 3Ngakhale sindili nanu mʼthupi, ndili nanu mu mzimu. Ndipo ineyo ndapereka kale chiweruzo pa munthu amene amachita zotere, ngati kuti ndili komweko. 4Mukasonkhana mu dzina la Ambuye athu Yesu, ine ndili nanu mu mzimu, ndipo mphamvu ya Ambuye athu Yesu ili pomwepo, 5mumupereke munthuyu kwa Satana, kuti chikhalidwe chake cha uchimo chiwonongedwe ndikuti mzimu wake udzapulumuke pa tsiku la Ambuye.

6Kudziwa kwanu si kwabwino. Kodi simukudziwa kuti yisiti wochepa amafufumitsa mphumphu yaufa wonse wa tirigu? 7Chotsani yisiti wakale kuti mukhale ndi mphumphu yopanda yisiti, monga inu muli. Pakuti Khristu, Mwana Wankhosa wa Paska wathu, anaperekedwa nsembe. 8Choncho, tiyeni tisunge chikondwererochi, osati ndi yisiti wakale, wowononga ndi woyipa, koma ndi buledi wopanda yisiti, buledi woona mtima ndi choonadi.

9Ndakulemberani mʼkalata yanga kuti musayanjane nawo anthu achigololo. 10Pamenepatu sindikutanthauzatu anthu a dziko lapansi lino amene ndi achigololo, kapena aumbombo, kapena opeza ndalama mwachinyengo, kapena opembedza mafano. Kukanatero mukanangochoka mʼdziko lapansi lino. 11Koma tsopano ndikukulemberani kuti musayanjane ndi aliyense amene adzitcha mʼbale koma ndi wachigololo, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, kapena wonamizira anzake, woledzera kapena wopeza ndalama mwachinyengo. Munthu wotere ngakhale kudya, osadya naye pamodzi.

12Kodi ndipindulanji kuti ndiweruze anthu amene si a mu mpingo? Kodi simuyenera kuweruza iwo amene ali mu mpingo? 13Mulungu adzaweruza akunja. “Chotsani woyipayo pakati panu.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

哥林多前書 5:1-13

清除淫亂之罪

1我聽說在你們當中竟有人與繼母亂倫。這種淫亂的事,就是連異教徒都做不出來。 2你們竟然還自高自大!難道你們不該痛心,把做這事的人從你們當中趕出去嗎? 3現在,我雖然身在遠方,心卻在你們那裡。我已經審判了做這事的人,就像親自在場一樣。 4你們奉我們主耶穌的名聚會時,我的心並我們主耶穌的權能也與你們同在。 5你們要把這人交給撒旦去毀壞他的肉體,好使這人的靈魂在主耶穌再來的日子可以得救。

6你們自誇不是好事,豈不知一點麵酵能使整團麵發起來嗎? 7你們要把舊酵除掉,好成為真正無酵的新麵團,因為我們逾越節的羔羊——基督已經被獻為祭了。 8所以,我們不可帶著歹毒邪惡的舊酵守這逾越節,而要用真誠純潔的無酵餅。

9我以前曾經寫信吩咐你們,不可與淫亂的人交往。 10我的意思並不是指世上所有淫亂、貪婪、欺詐與祭拜偶像的人。那樣的話,你們將不得不離開這個世界。 11我的意思是,若有人自稱是信徒,卻淫亂、貪婪、祭拜偶像、毀謗、酗酒、欺詐,你們不要和他們交往,甚至不要和他們一起吃飯。

12我何必去審判教會以外的人呢?然而,教會裡面的人豈不是該由你們審判嗎? 13上帝自會審判教會以外的人,你們要把那邪惡的人從你們當中趕出去。