1 Akorinto 15 – CCL & HHH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Akorinto 15:1-58

Za Kuuka kwa Khristu

1Tsono abale, ndikufuna ndikukumbutseni za Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani. Munawulandira ndipo munawukhulupirira kolimba. 2Inu munapulumutsidwa ndi Uthenga Wabwinowu, ngati mwasunga mawu amene ndinakulalikirani. Kupanda kutero, mwangokhulupirira pachabe.

3Pakuti chimene ndinalandira ndinapereka kwa inu monga chofunika kuposa zonse, kuti Khristu anafera zoyipa zathu monga mwa Malemba, 4kuti anayikidwa mʼmanda, kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu monga mwa Malemba; 5ndipo kuti anaonekera kwa Petro, ndipo kenaka kwa Atumwi khumi ndi awiriwo. 6Pambuyo pake, Iye anaonekera kwa anthu oposa 500 mwa abale pa nthawi imodzi, ndipo ambiri mwa iwo akanali ndi moyo ngakhale kuti ena anagona tulo. 7Kenaka anaonekeranso kwa Yakobo, kenaka kwa atumwi onse. 8Potsiriza pa onse anaonekeranso kwa ine, monga mwana wobadwa nthawi isanakwane.

9Pakuti ine ndine wamngʼono kwa atumwi ndipo sindiyenera nʼkomwe kutchedwa mtumwi chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu. 10Koma mwachisomo cha Mulungu, ndili mmene ndililimu, ndipo chisomo chake kwa ine sichinali chopanda ntchito. Ndinagwira ntchito kuposa ena onse a iwo. Choncho sindine koma chisomo cha Mulungu chimene chinali ndi ine. 11Tsono kaya ndi ineyo kapena iwowo, izi ndi zomwe timalalikira, ndipo izi ndi zimene munakhulupirira.

Kuuka kwa Oyera Mtima

12Koma ngati timalalikira kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, zikutheka bwanji kuti ena mwa inu azinena kuti kulibe kuuka kwa akufa? 13Ngati kulibe kuuka kwa akufa, ndiye kuti ngakhale Khristu sanaukenso. 14Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, ndiye kuti kulalikira kwathu nʼkopanda ntchito, ndipo chikhulupiriro chanu nʼchopandanso ntchito. 15Kuwonjezera pamenepa, ndiye kuti ndife mboni zabodza pa za Mulungu, pakuti tikuchita umboni kuti Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa. Ngati nʼzoona kuti akufa saukitsidwa, ndiye kuti Mulungu sanaukitsenso Khristu. 16Pakuti ngati akufa saukitsidwa, ndiye kuti nayenso Khristu sanaukitsidwe. 17Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu nʼchopanda ntchito; mukanali mu machimo anu. 18Ndiye kuti nawonso amene agona tulo mwa Ambuye ndi otayika. 19Ngati kukanakhala kuti tili ndi chiyembekezo mwa Khristu mʼmoyo uno wokha, tikanakhala omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse.

20Koma nʼzoonadi kuti Khristu anaukitsidwa kwa kufa, chipatso choyamba cha onse ogona tulo. 21Pakuti monga imfa inadza kudzera mwa munthu, kuuka kwa akufa kwabweranso kudzera mwa munthu. 22Pakuti monga mwa Adamu onse amafa, chomwechonso mwa Khristu onse adzakhala ndi amoyo. 23Koma aliyense adzauka pa nthawi yake. Khristu ndiye woyambirira, pambuyo pake, pamene Khristu adzabwera, iwo amene ali ake adzauka. 24Pamenepo chimaliziro chidzafika, pamene Iye adzapereka ufumu kwa Mulungu Atate, atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse. 25Pakuti Iye ayenera kulamulira mpaka Mulungu atayika pansi pa mapazi ake adani ake onse. 26Mdani wotsiriza kuwonongedwa ndi imfa. 27Pakuti Mulungu “wayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.” Ponena kuti wayika “zinthu zonse pansi pa mapazi ake,” nʼchodziwikiratu kuti sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene anayika zinthu zonse pansi pa Khristu. 28Pamene adzatsiriza kuchita zimenezi, Mwana weniweniyo adzakhala pansi pa ulamuliro wa Iye amene anayika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.

29Tsono ngati kulibe kuuka kwa akufa, kodi iwo amene akubatizidwa chifukwa cha akufa, adzatani? Ngati akufa saukitsidwa nʼkomwe, bwanji nanga anthu akubatizidwa mʼmalo mwawo? 30Ndipo kwa ife, tikuyikiranji moyo wathu pachiswe nthawi ndi nthawi? 31Abale, ndimafa tsiku ndi tsiku, ndikunenetsa zimenezi, mongotsimikizira monga ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu. 32Ngati ndinalimbana ndi zirombo za kuthengo ku Efeso pa zifukwa za umunthu chabe, ndapindulanji? Ngati akufa sadzaukitsidwa,

“Tiyeni tidye ndi kumwa,

pakuti mawa tifa.”

33Musasocheretsedwe, “Kukhala mʼmagulu oyipa kumawononga makhalidwe abwino.” 34Ganizani bwino monga kuyenerera, ndiye lekani kuchimwa; pakuti pali ena amene sadziwa Mulungu. Ndikunena izi kuti muchite manyazi.

Kuukitsidwa kwa Thupi

35Koma wina akhoza kufunsa kuti, “Kodi akufa amaukitsidwa motani? Adzauka ndi thupi la mtundu wanji?” 36Wopusa iwe! Chimene mudzala sichikhala ndi moyo pokhapokha chitayamba chafa. 37Mukadzala, simudzala thupi limene lidzamere, koma mbewu chabe, mwina ya tirigu kapena ya china chake. 38Koma Mulungu amayipatsa thupi monga Iye wafunira, ku mbewu ya mtundu uliwonse amapereka thupi lakelake. 39Mnofu siwofanana. Anthu ali ndi mnofu wa mtundu wina, nyama zili ndi wina, mbalame zili ndi wina, nsomba zili ndi winanso. 40Palinso matupi akumwamba ndipo palinso matupi a dziko lapansi; koma ulemerero wa matupi akumwamba ndi wina, ndi wa matupi a dziko lapansi ndi winanso. 41Dzuwa lili ndi ulemerero wake, ndipo pali ulemerero wina wa mwezi, palinso ulemerero winanso wa nyenyezi. Ulemerero wa nyenyezi ndi wosiyanasiyana.

42Zidzaterenso pamene akufa adzauka. Thupi loyikidwa mʼnthaka ngati mbewu limavunda, koma likadzauka lidzakhala losavunda. 43Limayikidwa mʼmanda mopanda ulemu, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi ulemerero. Limayikidwa mʼmanda lili lofowoka, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi mphamvu. 44Limayikidwa mʼmanda thupi la mnofu chabe, koma likadzaukitsidwa lidzakhala lauzimu.

Ngati pali thupi la mnofu, palinso thupi lauzimu. 45Kwalembedwa kuti, “Munthu woyamba Adamu anakhala wamoyo,” Adamu wotsiriza anakhala wopatsa moyo. 46Zauzimu sizinabwere koyambirira, koma zachilengedwe, pambuyo pake zauzimu. 47Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba. 48Monga analili munthu wa dziko lapansi, momwemonso anthu onse amene ndi a dziko lapansi. Ndipo monga alili munthu wakumwamba, momwemonso anthu onse amene ndi akumwamba. 49Ndipo monga momwe tinabadwa ofanana ndi munthu wa dziko lapansi uja, momwemonso tidzakhala ofanana ndi munthu wakumwamba.

50Ndikunenetsa, abale, kuti thupi ndi magazi sizingathe kulowa mu ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimavunda sizingathe kulowa kumene zinthu sizivunda. 51Tamverani, ndikuwuzeni chinsinsi. Tonse sitidzagona tulo, koma tonse tidzasandulika. 52Zidzachitika mwadzidzidzi, mʼkamphindi kochepa, monga ngati kuphethira kwa diso, pa lipenga lotsiriza. Pakuti lipenga lidzalira, akufa adzaukitsidwa opanda chovunda, ndipo ife tidzasandulika. 53Pakuti chovunda chiyenera kuvala chosavunda, ndi thupi ili lakufa liyenera kuvala losafa. 54Pamene thupi lovundali likadzasanduka losavunda, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzakwaniritsidwa zimene zinalembedwa zakuti, “Imfa yogonjetsedwa kwathunthu.”

55“Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti?

Iwe imfa, ululu wako uli kuti?”

56Ululu wa imfa ndi tchimo, ndipo mphamvu ya tchimo ndi lamulo. 57Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

58Choncho, abale anga okondedwa imani njii. Musasunthike ndi chilichonse. Nthawi zonse mudzipereke kwathunthu ku ntchito ya Ambuye, chifukwa mukudziwa kuti ntchito zanu mwa Ambuye sizili zopanda phindu.

Habrit Hakhadasha/Haderekh

אגרת פולוס הראשונה אל-הקורנתים 15:1-58

1אחי, ברצוני להזכיר לכם את הבשורה שהבאתי לכם – אותה בשורה שקיבלתם בשמחה ושאתם עדיין מאמינים בה. 2בשורה זאת היא המושיעה אתכם, אם אתם עדיין מאמינים בה, אלא אם כן מעולם לא האמנתם בה באמת.

3סיפרתי לכם כל מה שסופר לי, ודברים אלה הם בעלי חשיבות ראשונה במעלה: שהמשיח מת בעד חטאינו, כפי שניבאו הכתובים, 4שהוא נקבר, ושלאחר שלושה ימים קם לתחייה כפי שחזו הנביאים. 5המשיח נראה ל‎כֵּיפָא, לאחר מכן נראה לשנים־עשר התלמידים. 6הוא נגלה גם ליותר מחמש־מאות מאמינים שהתאספו יחד. רובם עדיין חיים ויכולים להעיד על כך, ואחדים מהם כבר מתו. 7אחר כך נראה המשיח ליעקב אחיו ולכל השליחים. 8לאחר שנראה אל כל האחרים הוא נראה לבסוף גם אלי, כאל מי שלא נולד בזמנו. 9כי אני השליח הקטן מכולם בחשיבותו, ולמעשה איני ראוי כלל להיקרא ”שליח“, שכן לפני בואי לאמונה רדפתי את קהילת אלוהים והטרדתי אותה.

10אולם בזכות טוב־לבו וחסדו של אלוהים אני היום מה שאני. חסדו בהחלט לא היה לשווא, כי פעלתי יותר מכל השליחים האחרים – כלומר, לא אני פעלתי, אלא אלוהים הוא שפעל דרכי. 11בעצם לא חשוב מי פעל יותר, הם או אני; העיקר שבישרנו לכם את הבשורה ושאתם האמנתם.

12איני מבין אתכם! אם אתם מאמינים שהמשיח קם מן המתים, מדוע אינכם מאמינים בתחיית־המתים? 13אם אין תחייה למתים, הרי שגם המשיח לא קם לתחייה, כלומר, הוא עדיין מת! 14ואם המשיח עדיין מת, אין כל ערך למה שסיפרנו לכם, וביטחונכם בה׳ חסר יסוד ותקווה. 15מכאן גם משתמע שכולנו, השליחים, שקרנים. כי סיפרנו לכם שאלוהים הקים את ישוע מן המתים – דבר שאינו אפשרי אם המתים אינם יכולים לקום לתחייה. 16ואם המתים אינם יכולים לקום לתחייה אזי גם המשיח לא קם, והוא עדיין מת. 17אם המשיח עדיין מת, איזה ערך יש לאמונתכם שה׳ הושיע אתכם? אתם עדיין משועבדים לחטא וצפויים לעונש! 18במקרה כזה, כל המאמינים שכבר מתו הם בעצמם אבודים. 19ואם אנו מאמינים ומקוים במשיח רק בעולם הזה, אומללים אנו מכל אדם!

20אולם תודה לאל על כך שהמשיח אכן קם מן המתים! הוא היה הראשון מבין הרבים שיקומו לתחייה יום אחד.

21כשם שהמוות בא לעולם בעקבות חטאו של אדם אחד – האדם הראשון – כך באה גם תחיית המתים לעולם על־ידי אדם אחד – המשיח. 22כולנו עתידים למות בגלל השתייכותנו למין האנושי והחוטא של אדם, והעונש על החטא הוא מוות. אך השייכים למשיח יקומו לתחייה. 23כל אחד יקום בתורו: המשיח היה הראשון שקם לתחייה, וכאשר ישוב אלינו, יקומו גם כל המאמינים השייכים לו.

24לאחר מכן יבוא הקץ – לאחר שהמשיח יכרית ויכניע את כל האויבים, הכוחות והשלטונות, ויחזיר את המלכות לאלוהים אביו. 25כי המשיח ימלוך עד שיכניע לרגליו את כל אויביו, 26והאויב האחרון שיכניע יהיה המוות. 27אלוהים אביו העניק לו שלטון וסמכות על הכול, חוץ מאשר על אלוהים עצמו שהוא נותן הכוח. 28לאחר שינצח המשיח את כל אויביו הוא ייכנע לשלטון אביו, כדי שהאלוהים אשר העניק לו את הניצחון על הכול יישאר מעל לכול.

29אם המתים לא יקומו לתחייה, מה התועלת במעשה האנשים שנטבלים בשם המתים? איזה ערך יש למעשה כזה, אם אינכם מאמינים שיום אחד יקומו המתים לתחייה? 30מלבד זאת, למה לנו לסכן את חיינו כל הזמן? 31הלא יודעים אתם שאני מסכן את חיי בכל יום; זוהי עובדה ממש כמו העובדה שאני גאה מאוד בהתפתחותכם הרוחנית. 32לשם מה נלחמתי בחיות הפרא – באנשי אפסוס – האם רק למען תועלתי בעולם הזה? אם לא נקום לתחייה לאחר מותנו, מה יש לנו להפסיד? הבה ”נהנה מהחיים, נאכל ונשתה כי מחר נמות!“15‏.32 טו 32 ישעיהו כב 13

33התרחקו מאנשים שחיים כך. אם תקשיבו להם, תושפעו מהם ותנהגו כמוהם. 34חשבו בהגיון ובתבונה והפסיקו לחטוא. עליכם להתבייש על שיש ביניכם אנשים שאינם מאמינים באלוהים ואף פעם לא האמינו – הם רק מעמידים פנים!

35אם ישאל מישהו: ”כיצד יוכלו המתים לקום לתחייה? כיצד ייראו? איזה גוף יהיה להם?“ 36השאלה אמנם טיפשית, אך את התשובה תמצאו. כשאתה טומן זרע באדמה, הוא לא יצמח עד שלא תקברהו תחילה. 37הגבעול הירקרק שצומח מהזרע שונה בצורתו מהזרע שזרעת, כי הרי טמנת באדמה זרע קטנטן ויבש, 38ואלוהים העניק לו גוף חדש כפי בחירתו. לכל זרע יש גוף שונה. 39כשם שיש זרעים שונים וצמחים שונים, כך יש גם מינים שונים של בשר וגוף. בני־אדם, חיות, דגים וציפורים – לכל אחד יש בשר אחר וגוף אחר.

40למלאכים בשמים יש גוף השונה משלנו, וגם היופי וההדר שלהם הוא ממין אחר שאינו דומה לשלנו. 41היופי וההוד של השמש שונה מזה של הירח והכוכבים, ולכל כוכב יש יופי וזוהר משלו.

42כך גם גופנו, שהוא בר־מיתה, שונה מהגוף שנקבל לאחר תחיית המתים, כי גופנו החדש יהיה בן־אלמוות! 43עכשיו נוטה גופנו לחלות ולמות, אך כשנקום לתחייה הוא יהיה מלא כוח וגבורה. 44עד המוות גופנו הוא גוף אנושי – בשר ודם; אולם בתחיית המתים הוא יהיה גוף רוחני על־טבעי.

45כתבי־הקודש מספרים לנו:15‏.45 טו 45 בראשית ב 7 ”ויהי האדם הראשון לנפש חיה“. כלומר, לאדם חי, ואילו האדם האחרון (המשיח) – לרוח שמעניק חיים.

46מכאן אתם רואים שה׳ מעניק תחילה גוף פיזי, ולאחר מכן גוף רוחני. 47האדם הראשון נברא מעפר האדמה, ואילו המשיח בא מהשמים. 48לכל בני־האדם יש גוף בשר ודם שנברא מעפר, כמו לאדם הראשון; אולם לכל מי ששייך למשיח יהיה גוף על־טבעי כמו למשיח. 49כשם שלכל אחד מאיתנו יש גוף כמו לאדם הראשון, כך יום אחד יהיה לכולנו גוף כמו למשיח.

50אני רוצה לומר לכם, אחים יקרים, שבשר ודם לא יוכל לרשת את מלכות האלוהים, כי בר־חלוף אינו יכול לרשת את הנצח ולשלוט בו. 51ברצוני לגלות לכם סוד נפלא: לא כולנו נמות, אבל לכולנו יהיה גוף אחר. 52הכול יתרחש במהירות הבזק, כהרף עין! כאשר תישמע תקיעת השופר האחרון מן השמים, כל המאמינים שמתו יקומו לתחייה בגוף חדש שאינו בר־מיתה, ואלה מאיתנו שחיים עדיין יקבלו גוף חדש לגמרי. 53כי גוף הבשר שיש לנו עתה ישתנה ויהפוך לגוף רוחני ונצחי.

54כאשר כל זה יתרחש, יתקיים הכתוב: ”המוות נוצח!“15‏.54 טו 54 כלשונו: ”בלע המות לנצח“. ישעיהו כה 8 55‏-56מוות, היכן ניצחונך? היכן עוקצך? החטא – העוקץ שגרם למוות – ייעלם, והתורה המצביעה על חטאינו שוב לא תשפוט אותנו. 57כל השבח והתהילה לאלוהים אבינו, על אשר עשה אותנו למנצחים על־ידי ישוע המשיח אדוננו.

58ובכן, אחים יקרים, הואיל והניצחון מובטח לנו, התחזקו, התעודדו ואל תתייאשו, כי יודעים אתם שכל עמלכם למען האדון אינו לשווא.