1 Akorinto 14 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Akorinto 14:1-40

Mphatso ya Uneneri ndi ya Malilime

1Funafunani chikondi, ndikufunitsitsa mphatso zauzimu, makamaka mphatso ya uneneri. 2Pakuti aliyense amene amayankhula malilime sayankhula kwa anthu, koma kwa Mulungu. Zoonadi, palibe amene amamva zimene akunena chifukwa Mzimu ndiye amamuyankhulitsa zachinsinsi. 3Koma amene amanenera amayankhula kwa anthu kuti awapatse mphamvu, awalimbikitse ndi kuwakhazikitsa mtima pansi. 4Iye amene amayankhula malilime amadzilimbikitsa yekha, koma amene amanenera amalimbikitsa mpingo. 5Nʼkanakonda kuti aliyense mwa inu atamayankhula malilime, koma ndi bwino kuti muzinenera. Amene amanenera amaposa amene amayankhula malilime, pokhapokha atatanthauzira kuti mpingo upindule.

6Tsono, abale, mudzapindula chiyani nditabwera kwa inu ndi kukuyankhulani mʼmalilime? Koma mudzapindula ngati nditakubweretserani vumbulutso lina lake, kapena chidziwitso, kapena chiphunzitso. 7Ngakhale mu zinthu zopanda moyo monga chitoliro kapena gitala, zimene zimatulutsa liwu; kodi munthu akhoza kudziwa bwanji nyimbo imene ikuyimbidwa ngati mawu sakumveka mogwirizana bwino? 8Komanso ngati lipenga silimveka bwino, ndani angakonzekere nkhondo? 9Chimodzimodzinso inu. Ngati simungayankhule mawu omveka bwino mʼchiyankhulo chanu, wina angadziwe bwanji chimene mukunena? Muzingodziyankhulira nokha. 10Mosakayika, pali ziyankhulo zosiyanasiyana pa dziko lapansi, koma palibe nʼchimodzi chomwe chimene chilibe tanthauzo. 11Tsono ngati sindingatolepo tanthauzo la zimene wina akuyankhula, ndiye kuti ndine mlendo kwa oyankhulayo ndipo iyeyo ndi mlendo kwa ine. 12Chimodzimodzinso inu. Popeza mumafunitsitsa mphatso za Mzimu, yesetseni kuchita bwino pa mphatso zimene zimamanga mpingo.

13Pa chifukwa ichi munthu amene amayankhula malilime apemphere kuti azitha kutanthauzira zimene akunena. 14Popeza ngati ndipemphera mʼmalilime, ndi mzimu wanga umene ukupemphera, koma nzeru zanga sizikupindula kanthu. 15Tsono pamenepa nʼkutani? Ndidzapemphera ndi mzimu wanga, komanso ndidzapemphera ndi nzeru zanga. Ndidzayimba ndi mzimu wanga, komanso ndidzayimba ndi nzeru zanga. 16Ngati mutamanda Mulungu mu mzimu, kodi munthu amene wapezeka pakati pa amene akuyankhula zomwe sakumva, adzavomereza bwanji kuti “Ameni” pa pemphero lanu loyamikalo popeza sakumva chimene mukunena? 17Mukhoza kumathokoza mokwanira, koma munthu winayo sanathandizikepo.

18Ndikuyamika Mulungu chifukwa ndimayankhula malilime kuposa nonsenu. 19Koma mu mpingo ndi kwabwino kuti ndiyankhule mawu asanu okha omveka bwino kuti ndilangize bwino ena kusiyana ndikuyankhula mawu ambirimbiri mʼmalilime.

20Abale, lekani kuganiza ngati ana. Mukhale ana pa nkhani ya zoyipa koma mʼmaganizo anu mukhale okhwima. 21Zinalembedwa mʼMalamulo kuti,

“Ndidzayankhula kwa anthu awa,

kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo

ndiponso ndi milomo yachilendo.

Koma ngakhale nthawi imeneyo sadzandimvera Ine,

akutero Ambuye.”

22Kotero, malilime ndi chizindikiro, osati cha kwa okhulupirira koma kwa osakhulupirira. Koma kunenera ndi chizindikiro kwa okhulupirira osati kwa osakhulupirira. 23Kotero kuti ngati mpingo wonse utasonkhana pamodzi ndipo aliyense namayankhula malilime, ndipo wina amene sangazindikire kapena ena osakhulupirira nabwerapo, kodi sadzanena kuti mwachita misala? 24Koma ngati wosakhulupirira kapena wina amene sakuzindikira abwera pamene aliyense akunenera, adzatsutsika mu mtima ndi zonse zimene akumva ndipo adzaweruzidwa ndi onse 25ndipo zinsinsi za mu mtima mwake zidzawululika. Kotero kuti adzadzigwetsa pansi ndi kupembedza Mulungu akufuwula kuti, “Mulungu ali pakati panudi!”

Kupembedza Mwadongosolo

26Kodi tsono abale, tinene chiyani? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense amakhala ali ndi nyimbo yoti ayimbe, kapena mawu oti alangize, vumbulutso, malilime, kapena kumasulira kwake. Zonsezi cholinga chake chikhale kulimbikitsa mpingo. 27Ngati wina ayankhula malilime, awiri kapena akachulukapo atatu ndiye ayankhule mmodzimmodzi, ndipo wina ayenera kutanthauzira zimene ayankhulazo. 28Ngati palibe wotanthauzira, woyankhulayo akhale chete mu mpingo ndipo adziyankhulire iye mwini ndi Mulungu.

29Aneneri awiri kapena atatu anenere, ndipo enawo asanthule mosamalitsa zimene anenerazo. 30Ndipo ngati vumbulutso labwera kwa munthu amene wakhala pansi, amene akuyankhulayo akhale chete. 31Pakuti nonse mukhoza kunenera mmodzimmodzi motsatana kuti aliyense alangizidwe ndi kulimbikitsidwa. 32Mizimu ya aneneri imamvera ulamuliro wa aneneri. 33Pakuti Mulungu si Mulungu wachisokonezo koma wamtendere. Monga mwa mipingo yonse ya oyera mtima.

Amayi Akhale Chete mu Mpingo

34Amayi akhale chete mʼmisonkhano ya mpingo. Iwo asaloledwe kuyankhula, koma azikhala omvera monga mmene lamulo linenera. 35Ngati ali ndi mafunso, akafunse amuna awo ku nyumba. Nʼchochititsa manyazi kuti mkazi ayankhule mu msonkhano wa mpingo.

36Kodi kapena mawu a Mulungu anachokera kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha? 37Ngati wina aliyense akuganiza kuti ndi mneneri kapena kuti ali ndi mphatso za Mzimu, ayenera kudziwa kuti zimene ndikukulemberanizi ndi lamulo la Ambuye. 38Ngati munthu savomereza zimenezi, iyeyonso sadzavomerezedwa.

39Nʼchifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse anthu kuyankhula malilime. 40Koma chilichonse chichitike moyenera ndi mwadongosolo.