1 Akorinto 12 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Akorinto 12:1-31

Mphatso za Mzimu Woyera

1Tsopano abale anga okondedwa, sindikufuna mukhale osadziwa za mphatso za Mzimu. 2Inu mukudziwa kuti pamene munali akunja, ankakusocheretsani mʼnjira zosiyanasiyana ndi kukukokerani ku mafano osayankhula. 3Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti palibe munthu amene ali ndi Mzimu wa Mulungu angayankhule kuti, “Yesu atembereredwe,” ndiponso palibe munthu anganene kuti “Yesu ndi Ambuye,” popanda kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.

4Pali mphatso zosiyanasiyana, koma Mzimu yemweyo. 5Pali mautumiki osiyanasiyana koma Ambuye yemweyo. 6Pali magwiridwe antchito osiyanasiyana, koma Mulungu yemweyo amagwira ntchito monsemo mwa anthu onse.

7Tsono Mzimu amapereka mphatso kwa aliyense kuti ipindulire onse. 8Mzimu amapereka kwa munthu wina mawu anzeru, Mzimu yemweyonso amapereka kwa wina mawu achidziwitso. 9Kwa wina, Mzimu yemweyo amapereka chikhulupiriro, kwa wina mphatso zamachiritso, Mzimu yemweyo. 10Kwa wina mphamvu zochita zodabwitsa, kwa wina mawu a uneneri, kwa wina mphatso yozindikira mizimu, kwa wina malilime osiyanasiyana, ndiponso kwa wina kutanthauzira malilimewo. 11Zonsezi ndi ntchito za Mzimu mmodzi yemweyo, ndipo amapereka kwa munthu aliyense monga momwe Mzimuyo wafunira.

Thupi Limodzi Ziwalo Zambiri

12Thupi ndi limodzi, ngakhale kuti lapangidwa ndi ziwalo zambiri. Ndipo ngakhale ziwalo zake zonse ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi. Momwemonso ndi mmene alili Khristu. 13Pakuti tonse tinabatizidwa ndi Mzimu mmodzi mʼthupi limodzi. Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu tonse tinapatsidwa kuti timwe Mzimu mmodzi yemweyo. 14Tsopano thupi silinapangidwe ndi chiwalo chimodzi koma ndi ziwalo zambiri.

15Ngati phazi litanena kuti, “Pakuti sindine dzanja, sindine chiwalo cha thupi.” Chifukwa chimenechi sichingachititse phazi kuti lisakhale chiwalo cha thupi. 16Ndipo ngati khutu litanena kuti, “Pakuti sindine diso, sindine chiwalo cha thupi.” Chifukwa chimenechi sichingachititse khutu kuti lisakhale chiwalo cha thupi. 17Kodi thupi lonse likanakhala diso, tikanamamva bwanji? Nanga thupi lonse likanakhala khutu, tikanamanunkhiza bwanji? 18Koma zoona nʼzakuti, Mulungu anayika ziwalo mʼthupi, chilichonse monga momwe Iye anafunira. 19Nanga zonse zikanakhala chiwalo chimodzi, ndiye thupi likanakhala lotani? 20Mmene zililimu, pali ziwalo zambiri koma thupi ndi limodzi lokha.

21Diso silingawuze dzanja kuti, “Iwe sindikukufuna!” Ndipo mutu sungawuze phazi kuti “Iwe sindikukufuna!” 22Mʼmalo mwake, ziwalo zathupi zimene zimaoneka ngati zofowoka ndizo zili zofunikira kwambiri, 23ndipo ziwalo zathupi zimene timaziyesa zopanda ulemu, ndizo timazilemekeza kwambiri. Ndipo ziwalo zosaoneka bwino ndizo zimalandira ulemu wapadera. 24Koma ziwalo zooneka bwino, nʼkosafunika kuti tizisamalire mwapadera. Mulungu polumikiza ziwalo zathupi, anapereka ulemu wopambana kwa ziwalo zimene zimafunadi ulemuwo 25kuti pasakhale kugawikana mʼthupi koma kuti ziwalo zonse zisamalirane. 26Ngati chiwalo chimodzi chikumva kuwawa, ziwalo zonse zimamvanso kuwawa. Ngati chiwalo chimodzi chilandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwera nawo.

27Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense wa inu ndi chiwalo cha thupilo. 28Ndipo Mulungu mu mpingo anayika poyamba atumwi, kachiwiri aneneri, kachitatu aphunzitsi, kenaka ochita zozizwitsa, ena a mphatso zamachiritso, ena a mphatso yothandiza anzawo, ena a mphatso yotsogolera ndiponso ena a mphatso ya malilime. 29Kodi onse ndi atumwi? Kodi onse ndi aneneri? Kodi onse ndi aphunzitsi? Kodi onse amachita zozizwitsa? 30Kodi onse ali ndi mphatso zamachiritso? Kodi onse amayankhula malilime? Kodi onse amatanthauzira malilime? 31Koma funitsitsani mphatso zopambana.

Tsopano ndikuonetsani njira yopambana kwambiri.