馬太福音 20 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

馬太福音 20:1-34

葡萄園工人的比喻

1耶穌接著說:「因為天國就像一個園主清早去外面請工人到他的葡萄園做工。 2他跟工人講好一天的工錢是一個銀幣,然後派他們去葡萄園。

3「大約上午九點鐘,園主出去看見一些人站在街市上無所事事, 4就對他們說,『你們到我的葡萄園來工作吧,我會給你們合理的工錢。』

5「他們便去了。正午和下午三點鐘,他又出去繼續請人到葡萄園做工。 6到了下午五點鐘的時候,他再次出去,看見還有人閒站在那裡,就問他們,『為什麼你們整天站在這裡無所事事呢?』 7他們回答說,『因為沒有人僱用我們。』園主說,『你們也到我的葡萄園來吧!』

8「到了傍晚,園主對工頭說,『叫工人來領工錢吧,最晚來的先領,最先來的後領。』

9「下午五點來的工人每人得了一個銀幣。 10最早來的工人來領的時候,以為必定可以多得一點工錢,誰知也各得一個銀幣。

11「他們拿著工錢滿腹牢騷地對園主說, 12『那些最晚來的人只工作了一小時,而我們在烈日之下辛苦了一整天,怎麼會領同樣的工錢呢?』

13「園主對他們當中的一個人說,『朋友,我並沒有欠你呀!我們不是講好付你一個銀幣嗎? 14拿著你的工錢走吧。我給那後來的和你一樣的工錢,是我願意。 15難道我不可隨意使用自己的錢嗎?因為我慷慨,你就眼紅嗎?』 16因此,為首的將要殿後,殿後的將要為首。」

耶穌第三次預言自己受難

17在去耶路撒冷的途中,耶穌把十二個門徒帶到一邊,對他們說: 18「你們要留意,我們現在前往耶路撒冷,人子將被交給祭司長和律法教師。他們要判祂死刑, 19把祂交給外族人,受嘲弄、鞭打,被釘在十字架上。但第三天祂必復活。」

一個母親的請求

20當時,西庇太的妻子帶著兩個兒子上前,跪在耶穌面前,有事要求祂。

21耶穌問她:「你要什麼呢?」

她說:「在你的國度,請讓我這兩個兒子一個坐在你右邊,一個坐在你左邊。」

22耶穌回答說:「你們不知道自己在求什麼。我要喝的那一杯,你們能喝嗎?」

他們說:「我們能。」

23耶穌對他們說:「我要喝的那一杯,你們也要喝。不過誰坐在我的左右不是我來定,而是我父為誰預備的,就讓誰坐。」

24其他十個門徒聽見這事,都對他們兄弟二人十分惱火。 25於是,耶穌把他們叫來,說:「外族人有君王統治他們,有大臣管理他們。但你們不可這樣。 26你們中間,誰要當首領,誰就要做大家的僕人; 27誰要居首位,誰就要做大家的奴僕。 28正如人子不是來受人服侍,而是來服侍人,並且犧牲性命,作許多人的贖價。」

治好兩個瞎子

29耶穌和祂的門徒離開耶利哥時,有一大群人跟著祂。 30有兩個瞎子正坐在路旁,聽說耶穌經過,就高聲喊叫:「主啊,大衛的後裔啊,可憐我們吧!」 31眾人責備他們,叫他們不要出聲,他們卻喊得更大聲了:「主啊,大衛的後裔啊,可憐我們吧!」

32耶穌停下腳步,叫了他們來,問他們:「你們要我為你們做什麼?」 33他們說:「主啊,我們想能夠看見。」 34耶穌就動了慈心,摸他們的眼睛,他們立刻得見光明,並跟從了耶穌。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 20:1-34

Fanizo la Aganyu Mʼmunda wa Mphesa

1“Ufumu wakumwamba uli ngati mwini munda amene anapita mmawa kukalemba anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa. 2Anagwirizana kuwalipira dinari monga malipiro a tsiku limodzi ndipo anawatumiza mʼmunda wake wamphesa.

3“Nthawi 9 koloko mmawa, anatulukanso naona ena atayimirira pa msika akungokhala. 4Anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa, ndipo ndidzakulipirani malipiro oyenera.’ 5Ndipo anapita.

“Anatulukanso nthawi ya 12 koloko masana, ndi nthawi ya 3 koloko masananso nachita chimodzimodzi. 6Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’

7“Iwo anayankha kuti, ‘Chifukwa palibe munthu amene watilemba ganyu.’

“Iye anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa.’

8“Ndipo pofika madzulo, mwini munda wamphesa anayitana kapitawo wake nati, ‘Itana antchito ndipo uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira aja mpaka oyamba.’

9“Antchito amene anawalemba ganyu pa 5 koloko masana anafika ndipo aliyense analandira dinari. 10Ndipo atabwera kwa amene analembedwa poyamba anayembekezera kuti alandira zambiri. Koma aliyense wa iwo analandira dinari. 11Atalandira, anayamba kuderera kwa mwini mundayo. 12Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’

13“Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari? 14Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe. 15Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi ndalama zanga? Kapena ukuyipidwa chifukwa ndine wopereka mowolowamanja?’

16“Momwemo omalizira adzakhala oyamba ndipo oyamba adzakhala omalizira.”

Yesu Anenanso za Imfa Yake

17Tsopano pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, anatengera pambali ophunzira ake khumi ndi awiriwo nati kwa iwo, 18“Tikupita ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo adzamuweruza kuti aphedwe, 19ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amunyoze ndi kumukwapula ndi kumupachika. Pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa!”

Pempho la Mkazi wa Zebedayo

20Amayi a ana a Zebedayo anabwera ndi ana ake kwa Yesu, nagwada pansi namupempha Iye.

21Yesu anawafunsa kuti, “Mukufuna chiyani?”

Amayiwo anati, “Lolani kuti ana anga awiriwa adzakhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja ndi wina ku dzanja lanu lamazere mu ufumu wanu.”

22Yesu anawawuza kuti, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwera chikho chimene ndidzamwera Ine?”

Iwo anayankha nati, “Inde tingathe.”

23Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kuti mudzakhale ku dzanja langa lamanja kapena lamazere si kwa Ine kupereka. Malo awa ndi a iwo amene anakonzeredweratu ndi Atate anga.”

24Ophunzira khumi aja, anawapsera mtima abale awiriwo. 25Yesu anawayitana onse pamodzi nati, “Mukudziwa kuti olamulira a mitundu ina ali ndi mphamvu pa iwo, ndipo akuluakulu awo amawalamulira. 26Siziyenera kutero ndi inu. Mʼmalo mwake, aliyense amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu akhale wotumikira wanu. 27Ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyamba akhale kapolo wanu. 28Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”

Yesu Achiritsa Anthu Awiri Osaona

29Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankachoka ku Yeriko, gulu lalikulu la anthu linawatsata. 30Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”

31Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”

32Yesu anayima ndi kuwayitana ndipo anawafunsa kuti, “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?”

33Anamuyankha nati, “Ambuye, tikufuna tione!”

34Yesu anamva nawo chifundo ndipo anakhudza maso awo. Nthawi yomweyo anaona namutsata Iye.