馬太福音 1 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

馬太福音 1:1-25

耶穌基督的家譜

1耶穌基督是亞伯拉罕的子孫、大衛的後裔,以下是祂的家譜:

2亞伯拉罕以撒

以撒雅各

雅各猶大和他的兄弟,

3猶大她瑪法勒斯謝拉

法勒斯希斯崙1·3 」希臘文是「亞蘭」。

希斯崙

4亞米拿達

亞米拿達拿順

拿順撒門

5撒門喇合波阿斯

波阿斯路得俄備得

俄備得耶西

6耶西大衛王。

大衛烏利亞的妻子生所羅門

7所羅門羅波安

羅波安亞比雅

亞比雅亞撒

8亞撒約沙法

約沙法約蘭

約蘭烏西雅

9烏西雅約坦

約坦亞哈斯

亞哈斯希西迦

10希西迦瑪拿西

瑪拿西亞們

亞們約西亞

11約西亞耶哥尼雅和他的兄弟,

那時以色列人被擄往巴比倫

12被擄到巴比倫以後,

耶哥尼雅撒拉鐵

撒拉鐵所羅巴伯

13所羅巴伯亞比玉

亞比玉以利亞敬

以利亞敬亞所

14亞所撒督

撒督亞金

亞金以律

15以律以利亞撒

以利亞撒馬但

馬但雅各

16雅各約瑟

約瑟就是瑪麗亞的丈夫,

那被稱為基督1·16 基督」意思是「受膏者」。的耶穌就是瑪麗亞生的。

17這樣,從亞伯拉罕大衛共有十四代,從大衛到被擄至巴比倫也是十四代,從被擄至巴比倫到基督降生也是十四代。

耶穌的降生

18以下是耶穌基督降生的經過。

耶穌的母親瑪麗亞約瑟訂了婚,還沒有成親就從聖靈懷了孕。 19約瑟是個義人,不願公開地羞辱她,便決定暗中和她解除婚約。 20他正在考慮這事的時候,主的一位天使在夢中向他顯現,說:「大衛的後裔約瑟,不要怕,把瑪麗亞娶過來,因為她所懷的孕是從聖靈來的。 21她將生一個兒子,你要給祂取名叫耶穌1·21 耶穌」意思是「救主」。,因為祂要把自己的子民從罪惡中救出來。」

22這一切應驗了主藉著先知所說的話: 23「必有童貞女懷孕生子,祂的名字要叫以馬內利,意思是『上帝與我們同在』。」 24約瑟醒來,就遵從主的天使的吩咐和瑪麗亞結婚, 25只是在她生下孩子之前沒有與她同房。約瑟給孩子取名叫耶穌。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 1:1-25

Makolo a Yesu Khristu Monga mwa Thupi

1Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu:

2Abrahamu anabereka Isake,

Isake anabereka Yakobo,

Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake.

3Yuda anabereka Perezi ndi Zara, amene amayi awo anali Tamara.

Perezi anabereka Hezironi,

Hezironi anabereka Aramu.

4Aramu anabereka Aminadabu,

Aminadabu anabereka Naasoni,

Naasoni anabereka Salimoni.

5Salimoni anabereka Bowazi amene amayi ake anali Rahabe,

Bowazi anabereka Obedi amene amayi ake anali Rute,

Obedi anabereka Yese.

6Yese anabereka Mfumu Davide.

Ndipo Davide anabereka Solomoni, amene amayi ake anali mkazi wa Uriya.

7Solomoni anabereka Rehabiamu,

Rehabiamu anabereka Abiya,

Abiya anabereka Asa,

8Asa anabereka Yehosafati,

Yehosafati anabereka Yoramu,

Yoramu anabereka Uziya.

9Uziya anabereka Yotamu,

Yotamu anabereka Ahazi,

Ahazi anabereka Hezekiya.

10Hezekiya anabereka Manase,

Manase anabereka Amoni,

Amoni anabereka Yosiya.

11Yosiya anali atabala Yekoniya ndi abale ake pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babuloni.

12Ali ku ukapolo ku Babuloni,

Yekoniya anabereka Salatieli,

Salatieli anabereka Zerubabeli.

13Zerubabeli anabereka Abiudi,

Abiudi anabereka Eliakimu,

Eliakimu anabereka Azoro.

14Azoro anabereka Zadoki,

Zadoki anabereka Akimu,

Akimu anabereka Eliudi.

15Eliudi anabereka Eliezara,

Eliezara anabereka Matani,

Matani anabereka Yakobo.

16Yakobo anabereka Yosefe, mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabereka Yesu wotchedwa Khristu.

17Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi.

Kubadwa kwa Yesu Khristu

18Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. 19Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera.

20Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera. 21Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”

22Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti, 23“Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.”

24Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake. 25Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu.