路加福音 20 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

路加福音 20:1-47

質問耶穌的權柄

1有一天,耶穌正在聖殿裡教導人、傳講福音,祭司長、律法教師和長老上前, 2質問祂:「告訴我們,你憑什麼權柄做這些事?誰授權給你了?」

3耶穌回答說:「我也問你們一個問題。你們告訴我, 4約翰的洗禮是從天上來的還是從人來的?」

5他們彼此議論說:「如果我們說『是從天上來的』,祂一定會問,『那你們為什麼不相信他?』 6如果我們說『是從人來的』,百姓會拿石頭打死我們,因為他們相信約翰是先知。」 7於是,他們回答說:「我們不知道約翰的洗禮是從哪裡來的。」

8耶穌說:「我也不告訴你們我憑什麼權柄做這些事。」

利慾薰心的佃戶

9接著耶穌對眾人講了個比喻:「有人開墾了一個葡萄園,把園子租給幾個佃戶,就出遠門了。 10到了收穫的季節,他差奴僕去葡萄園向佃戶收取他應得的收成,但那些佃戶卻把奴僕揍了一頓,使他空手而歸。 11園主又派另一個奴僕去,那些佃戶照樣將他毆打並羞辱一番,使他空手而歸。 12園主又派第三個奴僕去,他們又把他打傷,拋在園外。

13「園主說,『我該怎樣辦呢?不如叫我所疼愛的兒子去吧。他們大概會尊敬他。』

14「豈料那些佃戶看見來人是園主的兒子,便彼此商量說,『這個人是產業繼承人,我們把他殺掉,這葡萄園就歸我們了!』 15於是他們把園主的兒子拖到葡萄園外殺了。

「那麼,園主會怎樣處治他們呢? 16他必來殺掉這些佃戶,把葡萄園轉租給別人。」

眾人聽了就說:「但願這種事永遠不會發生!」

17耶穌定睛看著他們,問道:「那麼,聖經上說,

『工匠丟棄的石頭已成了房角石』,

這句話是什麼意思呢? 18凡跌在這石頭上的人,將粉身碎骨;這石頭落在誰身上,將把誰砸爛。」

納稅問題

19律法教師和祭司長聽出這比喻是針對他們說的,便想立刻下手捉拿耶穌,但又害怕百姓。 20於是,他們密切地監視耶穌,又派遣密探假裝好人,想從祂的話裡找把柄抓祂去見總督。

21那些密探問耶穌:「老師,我們知道你所講所傳的道都是正確的,也知道你不看人的情面,只按真理傳上帝的道。 22那麼,我們向凱撒納稅對不對呢?」

23耶穌看破他們的陰謀, 24就叫他們拿一個銀幣來,問他們:「上面刻的是誰的像和名號?」他們說:「凱撒的。」

25耶穌說:「屬於凱撒的,要給凱撒;屬於上帝的,要給上帝。」

26耶穌的回答令他們驚奇,他們無法當眾找到把柄,只好閉口不言。

論死人復活

27撒督該人向來不相信有復活的事。有幾個這一派的人來問耶穌: 28「老師,按摩西為我們寫的律例,如果有人娶妻後沒有孩子就死了,他的兄弟應當娶嫂嫂,替哥哥傳宗接代。 29有弟兄七人,老大結了婚,沒有孩子就死了。 30二弟、 31三弟、一直到七弟都相繼娶了嫂嫂,都沒有留下孩子就死了。 32最後那個女人也死了。 33那麼,到復活的時候,她將是誰的妻子呢?因為七個人都娶過她。」

34耶穌說:「今世的人才有嫁娶, 35但那些配得將來的世界、從死裡復活的人也不娶也不嫁, 36就像天使一樣永遠不會死。他們既然從死裡復活,就是上帝的兒女。 37在記載關於燃燒的荊棘的篇章中,摩西也證實死人會復活,因為他稱主是『亞伯拉罕的上帝,以撒的上帝,雅各的上帝』。 38上帝不是死人的上帝,而是活人的上帝。因為在祂那裡的人都是活人。」

39幾位律法教師說:「老師答得好!」 40此後,再沒有人敢問耶穌問題了。

論基督

41耶穌問他們:「人怎麼說基督是大衛的後裔呢? 42大衛曾在詩篇裡說,

『主對我主說,

你坐在我的右邊,

43等我使你的仇敵成為你的腳凳。』

44既然大衛稱基督為主,基督又怎麼會是大衛的後裔呢?」

45大家正在細聽,耶穌對門徒說: 46「你們要提防律法教師。他們愛穿著長袍招搖過市,喜歡人們在大街上問候他們,又喜歡會堂裡的上座和宴席中的首位。 47他們侵吞寡婦的財產,還假意做冗長的禱告。這種人必受到更嚴厲的懲罰!」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 20:1-47

Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake

1Tsiku lina pamene Iye ankaphunzitsa anthu mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu ndi kuphunzitsa Uthenga Wabwino, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, pamodzi ndi akuluakulu anabwera kwa Iye. 2Iwo anati, “Mutiwuze mukuchita izi ndi ulamuliro wayani? Ndani anakupatsani ulamuliro uwu?”

3Iye anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani, mundiyankhe, 4‘Kodi ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena wochokera kwa anthu?’ ”

5Iwo anakambirana pakati pawo ndikuti, “Ngati ife tinena kuti, ‘Kuchokera kumwamba’ Iye akatifunsa kuti, ‘chifukwa chiyani simunamukhulupirire iye?’ 6Koma ngati ife tinena kuti, ‘kuchokera kwa anthu,’ anthu onse atigenda miyala, chifukwa amatsimikiza kuti Yohane anali mneneri.”

7Pamenepo iwo anayankha kuti, “Ife sitidziwa kumene unachokera.”

8Yesu anati, “Ngakhale Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira zimenezi.”

Fanizo la Olima Mʼmunda Wamphesa

9Iye anapitirira kuwawuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wamphesa, nabwereketsa kwa alimi ena ndipo anachoka kwa nthawi yayitali. 10Pa nthawi yokolola, iye anatumiza wantchito wake kwa alimi aja kuti amupatseko zina mwa zipatso za munda wamphesawo. Koma alimi aja anamumenya namubweza wopanda kanthu. 11Iye anatumiza wantchito wina, koma uyunso anamumenya namuchita zachipongwe ndi kumubweza wopanda kanthu. 12Iye anatumizanso wina wachitatu ndipo iwo anamuvulaza namuponya kunja.

13“Kenaka mwini mundawo anati, ‘Kodi ndichite chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga wamwamuna, amene ndimukonda; mwina iwo adzamuchitira ulemu.’

14“Koma alimiwo ataona mwanayo, anakambirananso. Iwo anati, ‘Uyu ndiye wodzamusiyira chumachi. Tiyeni timuphe ndipo chumachi chikhala chathu.’ 15Ndipo anamuponya kunja kwa mundawo ndi kumupha.

“Nanga tsono mwini munda wamphesayo adzawatani anthuwa? 16Iye adzabwera ndi kupha alimi aja ndi kupereka mundawo kwa ena.”

Pamene anthu anamva izi, anati, “Musatero ayi.”

17Yesu anawayangʼanitsitsa ndipo anafunsa kuti, “Kodi tanthauzo lake ndi chiyani la zimene zinalembedwa kuti,

“ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana

wasanduka mwala wa pa ngodya.

18Aliyense amene agwa pa mwalawu adzapweteka, koma iye amene udzamugwera udzamuphwanya.’ ”

19Aphunzitsi amalamulo ndi akulu a ansembe amafuna njira yoti amuphe nthawi yomweyo, chifukwa anadziwa kuti ananena fanizo ili powatsutsa iwo. Koma iwo anali ndi mantha chifukwa cha anthu.

Za Kupereka Msonkho kwa Kaisara

20Pamene ankamulondalonda Iye, iwo anatumiza akazitape amene amaoneka ngati achilungamo. Iwo ankafuna kumutapa mʼkamwa Yesu mu china chilichonse chimene Iye ananena kuti amupereke Iye kwa amene anali ndi mphamvu ndi ulamuliro oweruza. 21Potero akazitapewo anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi, tidziwa kuti mumayankhula ndi kuphunzitsa zimene zili zoonadi, ndi kuti simuonetsa tsankho koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mwachoonadi. 22Kodi ndi bwino kwa ife kumapereka msonkho kwa Kaisara kapena kusapereka?”

23Iye anaona chinyengo chawo ndipo anawawuza kuti, 24“Onetseni ndalama. Chithunzi ndi malembawa ndi zayani?”

25Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.”

Iye anawawuza kuti, “Ndiye perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zimene ndi za Mulungu.”

26Iwo analephera kumupeza cholakwa pa zimene ankayankhula pamaso pa anthu. Ndipo pothedwa nzeru ndi yankho lake, iwo anakhala chete.

Za Kuuka kwa Akufa ndi Ukwati

27Ena mwa Asaduki, amene ankanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Yesu ndi funso. 28Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 29Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyambayo anakwatira mkazi ndipo anafa wopanda mwana. 30Wachiwiri 31ndipo kenaka wachitatuyo anamukwatira iye, ndipo chimodzimodzi asanu ndi awiri aja anafa osasiya ana. 32Pa mapeto pake mkaziyo anafanso. 33Tsopano, pa nthawi ya kuukanso, kodi mkaziyu adzakhala wayani popeza onse asanu ndi awiri anamukwatirapo?”

34Yesu anayankha kuti, “Anthu a mʼbado uno amakwatira ndi kukwatiwa. 35Koma mʼmoyo umene ukubwerawo, anthu amene adzaukitsidwe kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa. 36Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa. 37Ngakhale pa nkhani yachitsamba choyaka moto, Mose anaonetsa kuti akufa amauka, pakuti anatcha Ambuye ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.’ 38Mulungu si Mulungu wa akufa, koma wa amoyo, pakuti kwa Iye onse ali ndi moyo.”

39Ena mwa aphunzitsi amalamulo anayankha kuti, “Mwanena bwino mphunzitsi!” 40Ndipo panalibe wina amene akanalimba mtima kumufunsa Iye mafunso ena.

Khristu ndi Mwana wa Ndani?

41Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Zikutheka bwanji kuti aziti Khristu ndi mwana wa Davide? 42Davide mwini wake akunenetsa mʼbuku la Masalimo kuti,

“Ambuye anati kwa Ambuye anga:

‘Khalani ku dzanja langa lamanja,

43mpaka Ine nditasandutsa adani anu

chopondapo mapazi anu?’

44Davide akumutcha Iye ‘Ambuye.’ Nanga zingatheke bwanji kuti Iye akhale mwana wake?”

Achenjeza za Aphunzitsi Amalamulo

45Pamene anthu onse ankamvetsera, Yesu anati kwa ophunzira ake, 46“Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando. 47Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”