詩篇 63 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 63:1-11

第 63 篇

渴慕上帝

大衛在曠野時作的詩。

1上帝啊,你是我的上帝,

我迫切地尋求你!

在乾旱荒涼之地,

我的心渴慕你,渴慕你!

2我曾在你的聖所瞻仰你的榮面,

目睹你的權能和榮耀。

3你的慈愛比生命更寶貴,

我的嘴唇要讚美你。

4我一生都要讚美你,

奉你的名舉手禱告。

5我心滿意足,如享盛宴,

唱起歡快的歌讚美你。

6我躺在床上的時候思念你,

整夜地思想你。

7因為你是我的幫助,

我在你翅膀的蔭庇下歡歌。

8我的心依戀你,

你的右手扶持我。

9那些圖謀毀滅我的人必下到陰間。

10他們必喪身刀下,

成為豺狼的食物。

11但王要因上帝而歡欣,

凡信靠祂的人必歡喜快樂,

說謊者的口必被封住。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 63:1-11

Salimo 63

Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda.

1Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,

moona mtima ine ndimakufunafunani;

moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,

thupi langa likulakalaka inu,

mʼdziko lowuma ndi lotopetsa

kumene kulibe madzi.

2Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika

ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.

3Chifukwa chikondi chanu

ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.

4Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,

ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.

5Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona.

Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.

6Pa bedi panga ndimakumbukira inu;

ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.

7Chifukwa ndinu thandizo langa,

ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.

8Moyo wanga umakangamira Inu;

dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.

9Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa;

adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.

10Iwo adzaperekedwa ku lupanga

ndi kukhala chakudya cha ankhandwe.

11Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;

onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo,

koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.