詩篇 47 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 47:1-9

第 47 篇

至高的主宰

可拉後裔的詩,交給樂長。

1萬民啊,你們要鼓掌,

向上帝高聲歡呼!

2因為至高者耶和華當受敬畏,

祂是普天下的大君王。

3祂使列國降服於我們,

讓列邦伏在我們腳下。

4祂為我們選定產業,

就是祂所愛的雅各引以為榮的產業。(細拉)

5在歡呼聲中,上帝登上寶座;

在號角聲中,耶和華登上寶座。

6要頌讚,頌讚上帝!

要頌讚,頌讚我們的君王!

7因為上帝是普天下的君王,

要向祂唱讚美的樂章。

8祂坐在聖潔的寶座上治理列國。

9列邦的首領聚集在一起,

要做亞伯拉罕之上帝的子民,

因為上帝是主宰天下的君王,

祂至高無上。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 47:1-9

Salimo 47

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

1Ombani mʼmanja, inu anthu onse;

fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.

2Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;

Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!

3Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;

anayika anthu pansi pa mapazi athu.

4Iye anatisankhira cholowa chathu,

chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.

Sela

5Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,

Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.

6Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;

imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.

7Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;

imbirani Iye salimo la matamando.

8Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;

Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.

9Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana

monga anthu a Mulungu wa Abrahamu,

pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;

Iye wakwezedwa kwakukulu.