詩篇 37 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 37:1-40

第 37 篇

義人和惡人的結局

大衛的詩。

1不要因為惡人而煩惱,

也不要羡慕作惡之人,

2因為他們如瞬息枯萎的草芥,

又如轉眼消逝的綠草。

3要信靠耶和華,要行善,

要在這片土地上安然度日。

4要以耶和華為樂,

祂必成全你的願望。

5要把一切交托給耶和華,

信靠祂,祂必幫助你,

6使你的公義如晨光照耀,

你的仁義如日中天。

7要在耶和華面前安靜,

耐心等候祂,

不要因惡人道路通達、陰謀得逞而憤憤不平。

8你要抑制怒氣,除掉憤怒;

不要心懷不平,

那會導致你作惡。

9因為作惡的終必滅亡,

但等候耶和華的必承受土地。

10再過片刻,惡人必不復存在,

無處可尋。

11但謙卑人必承受土地,

得享太平。

12惡人謀害義人,

對他們咬牙切齒。

13但耶和華嗤笑邪惡人,

因為祂知道他們末日將臨。

14惡人拔劍張弓要消滅窮苦人,

殺戮正直人,

15但他們的劍必刺穿自己的心,

他們的弓必被折斷。

16義人淡泊一生強過惡人財富如山。

17因為惡人的勢力終必瓦解,

耶和華必扶持義人。

18耶和華天天看顧純全無過的人,

他們的產業永遠長存。

19他們在災難中不致絕望,

在饑荒時仍得飽足。

20但惡人必滅亡,

上帝的仇敵必像野地枯萎的花草,

消逝如煙。

21惡人借債不還,

義人慷慨給予。

22蒙耶和華賜福的人必承受土地,

被耶和華咒詛的人必遭剷除。

23耶和華引領義人的腳步,

喜悅他們所走的路。

24他們即使失腳,也不會跌倒,

因為耶和華的手扶持他們。

25從幼年到老年,

我從未見過義人遭棄,

也未見其後人討飯。

26他們樂善好施,

後代都蒙祝福。

27你要離惡行善,

就必永遠安居。

28因為耶和華喜愛正義,

不丟棄信靠祂的人,

永遠保護他們。

惡人的後代必被剷除。

29義人必承受土地,

在地上永遠安居。

30義人口出智慧,訴說正義,

31銘記上帝的律法,

從不失腳。

32惡人窺探義人,

伺機謀害。

33但耶和華不會讓惡人得逞,

也不會讓義人在審判時被定罪。

34要等候耶和華,

堅守祂的道,

祂必賜你土地,使你有尊榮。

你必親眼看見惡人被剷除。

35我見過邪惡殘暴之人,

乍看如蔥蘢的黎巴嫩香柏樹,

36再一看,

他已經消失得無影無蹤,

無處可尋。

37你看那純全正直、愛好和平的人,

他們前途美好。

38罪人必遭毀滅,

惡人必被剷除。

39耶和華拯救義人,

患難時作他們的庇護所。

40耶和華幫助他們,

拯救他們脫離惡人,

因為他們投靠祂。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 37:1-40

Salimo 37

Salimo la Davide.

1Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa

kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa;

2pakuti monga udzu iwo adzafota msanga,

ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga.

3Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino;

khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.

4Udzikondweretse wekha mwa Yehova

ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.

5Pereka njira yako kwa Yehova;

dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:

6Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha,

chiweruzo chako ngati dzuwa la masana.

7Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa;

usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo,

pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.

8Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali,

usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa.

9Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa,

koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko.

10Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso;

ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso.

11Koma ofatsa adzalandira dziko

ndipo adzasangalala ndi mtendere waukulu.

12Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama

ndipo amawakukutira mano;

13koma Ambuye amaseka oyipa

pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera.

14Oyipa amasolola lupanga

ndi kupinda uta

kugwetsa osauka ndi osowa,

kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama.

15Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe,

ndipo mauta awo anathyoka.

16Zabwino zochepa zimene olungama ali nazo

ziposa chuma cha anthu oyipa ambiri;

17pakuti mphamvu ya oyipa idzasweka,

koma Yehova amasunga olungama.

18Masiku a anthu osalakwa amadziwika ndi Yehova,

ndipo cholowa chawo chidzakhala mpaka muyaya.

19Pa nthawi ya mavuto iwo sadzafota;

mʼmasiku a njala adzakhala ndi zinthu zambiri.

20Koma oyipa adzawonongeka;

adani a Yehova adzakhala ngati kukongola kwa kuthengo,

iwo adzazimirira ngati utsi.

21Oyipa amabwereka ndipo sabweza

koma olungama amapereka mowolowamanja.

22Iwo amene Yehova amawadalitsa adzalandira dziko,

koma amene Iye amawatemberera adzachotsedwa.

23Ngati Yehova akondwera ndi njira ya munthu,

amakhazikitsa mayendedwe ake;

24ngakhale atapunthwa sadzagwa,

pakuti Yehova amamutchinjiriza ndi dzanja lake.

25Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba

koma sindinaonepo olungama akusiyidwa

kapena ana awo akupempha chakudya.

26Iwo ndi owolowamanja nthawi zonse ndipo amabwereketsa mwaufulu;

ana awo adzadalitsika.

27Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino;

pamenepo udzakhazikika mʼdziko kwamuyaya.

28Pakuti Yehova amakonda wolungama

ndipo sadzasiya okhulupirika ake.

Iwo adzatetezedwa kwamuyaya,

koma zidzukulu za oyipa zidzachotsedwa;

29olungama adzalandira dziko

ndipo adzakhazikikamo kwamuyaya.

30Pakamwa pa munthu wolungama pamayankhula za nzeru,

ndipo lilime lake limayankhula zolungama.

31Lamulo la Mulungu wake lili mu mtima mwake;

mapazi ake saterereka.

32Oyipa amabisala kudikira olungama;

kufunafuna miyoyo yawoyo;

33koma Yehova sadzawasiya pansi pa mphamvu yawo

kapena kuti atsutsidwe pamene abweretsedwa pa milandu.

34Khulupirira Yehova,

ndipo sunga njira yake;

Iye adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako;

udzaona anthu oyipa akuwonongeka.

35Ine ndinaona munthu woyipa ndi munthu wopanda chifundo

akupeza bwino ngati mtengo wobiriwira pa nthaka ya makolo ake.

36Koma sanachedwe kumwalira ndipo sanaonekenso;

ngakhale ndinamuyangʼanayangʼana, sanapezekenso.

37Ganizira za munthu wosalakwa, yangʼanitsitsa munthu wolungama;

udzaona kuti ali ndi tsogolo labwino ndipo ali ndi zidzukulu zambiri.

38Koma anthu ochimwa adzawonongeka;

iwowo pamodzi ndi zidzukulu zawo zomwe.

39Chipulumutso cha olungama chimachokera kwa Yehova;

Iye ndiye linga lawo pa nthawi ya masautso.

40Yehova amawathandiza ndi kuwalanditsa;

Iye amawalanditsa kwa oyipa ndi kuwapulumutsa,

pakuti amathawira kwa Iye.