箴言 23 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

箴言 23:1-35

1你若與官長同席,

要注意面對的是誰。

2如果你是貪吃的人,

就要節制食慾23·2 節制食慾」希伯來文是「把刀放在喉嚨上」。

3不可貪戀他的美食,

這美食是圈套。

4別為錢財耗盡心力,

要明智,適可而止。

5錢財眨眼之間消逝無蹤,

它必長出翅膀如鷹飛去。

6不要吃吝嗇人的飯,

不可貪圖他的美味。

7因為他總是精於算計,

嘴上說「請吃,請喝」,

心裡卻另有盤算。

8你必嘔出所吃的那點飯,

你說的美言都必枉費。

9不要和愚人說話,

他必藐視你的智言。

10不可挪移古時的界石,

不可侵佔孤兒的田地。

11因他們的救贖主強大,

祂必對付你,替他們伸冤。

12你要專心接受教誨,

側耳傾聽智言。

13不要疏於管教孩子,

杖責不會使他斃命,

14杖責能救他脫離死亡。

15孩子啊,

你若心裡有智慧,

我心裡也會歡喜。

16你的口若說正直的話,

我的內心也歡暢不已。

17不要心裡羡慕罪人,

要終日敬畏耶和華。

18這樣,你必前途光明,

你的盼望不會幻滅。

19孩子啊,聽我的話,

要有智慧,心守正道。

20不要結交酒肉朋友,

21因為好酒貪吃者必窮困,

貪睡的人必穿破衣爛衫。

22要聽從生養你的父親,

不可輕視年老的母親。

23要買真理、智慧、教誨和悟性,

不可賣掉。

24義人的父親喜樂無限,

智慧之子使父母歡欣。

25你要使父母快樂,

叫生你的人歡欣。

26孩子啊,把你的心交給我,

歡然走我的道路。

27妓女是深坑,淫婦是陷阱;

28她像強盜般埋伏,

使世間增添奸徒。

29誰有災禍?誰有憂傷?

誰有爭吵?誰有怨言?

誰無故受傷?誰兩眼發紅?

30就是那些沉迷醉鄉,

品嚐醇和之酒的人!

31雖然鮮紅的酒在杯中閃爍,

喝下去痛快,但不要盯著它。

32它終必像蛇一樣傷你,

像毒蛇一樣咬你。

33你的眼會看見怪異的景象,

你會神智不清,胡言亂語。

34你好像躺在怒海中,

又像臥在桅杆頂上。

35你會說:「人打我,我不痛;

人揍我,我不知。

什麼時候醒了,再乾一杯!」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 23:1-35

1Ngati ukhala pansi kuti udye pamodzi ndi wolamulira,

uyangʼane bwino zimene zili pamaso pako,

2ngati ndiwe munthu wadyera

udziletse kuti usaonetse dyera lakolo.

3Usasirire zakudya zake,

pakuti zimenezo ndi zakudya zachinyengo.

4Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma,

ukhale ndi nzeru ya kudziretsa.

5Ukangoti wachipeza chumacho uwona posachedwa kuti palibepo.

Chumacho chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi

ndi kuwuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.

6Usadye chakudya cha munthu waumbombo,

usalakalake zakudya zake zokoma;

7paja iye ndi munthu amene

nthawi zonse amaganizira za mtengo wake

ngakhale amati kwa iwe, “Idya ndi kumwa,”

koma sakondweretsedwa nawe.

8Udzasanza zimene wadyazo

ndipo mawu ako woyamikira adzapita pachabe.

9Usayankhule munthu wopusa akumva,

pakuti adzanyoza mawu ako anzeru.

10Usasunthe mwala wa mʼmalire akalekale

kapena kulowerera mʼminda ya ana amasiye,

11paja Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu;

iye adzawateteza pa milandu yawo kutsutsana nawe.

12Mtima wako uzikhala pa malangizo

ndipo makutu ako azimvetsera mawu a chidziwitso.

13Usaleke kumulangiza mwana;

ngati umulanga ndi chikwapu sadzafa.

14Ukamukwapula ndi tsatsa

udzapulumutsa moyo wake.

15Mwana wanga, ngati mtima wako ukhala wanzeru,

inenso mtima wanga udzakondwera.

16Mtima wanga udzakondwera

pamene ndidzakumva ukuyankhula zolungama.

17Mtima wako usachite nsanje ndi anthu ochimwa,

koma uziopa Yehova tsiku ndi tsiku.

18Ndithu za mʼtsogolo zilipo

ndipo chiyembekezo chakocho sichidzalephereka.

19Tamvera mwana wanga, ndipo ukhale wanzeru,

mtima wako uwuyendetse mʼnjira yabwino.

20Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera

kapena pakati pa anthu amene amadya nyama mwadyera.

21Paja anthu oledzera ndi adyera amadzakhala amphawi

ndipo aulesi adzavala sanza.

22Mvera abambo ako amene anakubala,

usanyoze amayi ako pamene akalamba.

23Gula choonadi ndipo usachigulitse;

ugulenso nzeru, mwambo ndiponso kumvetsa zinthu bwino.

24Abambo a munthu wolungama ali ndi chimwemwe chachikulu;

Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.

25Abambo ndi amayi ako asangalale;

amene anakubereka akondwere!

26Mwana wanga, undikhulupirire

ndipo maso ako apenyetsetse njira zanga.

27Paja mkazi wachiwerewere ali ngati dzenje lozama;

ndipo mkazi woyendayenda ali ngati chitsime chopapatiza.

28Amabisala ngati mbala yachifwamba,

ndipo amuna amakhala osakhulupirika chifukwa cha iyeyu.

29Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni?

Ndani ali pa mkangano? Ndani ali ndi madandawulo?

Ndani ali ndi zipsera zosadziwika uko zachokera? Ndani ali ndi maso ofiira?

30Ndi amene amakhalitsa pa mowa,

amene amapita nalawa vinyo osakanizidwa.

31Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo,

pamene akuwira mʼchikho

pamene akumweka bwino!

32Potsiriza pake amaluma ngati njoka,

ndipo amajompha ngati mphiri.

33Maso ako adzaona zinthu zachilendo

ndipo maganizo ndi mawu ako adzakhala osokonekera.

34Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja,

kapena ngati munthu wogona pa msonga ya mlongoti ya ngalawa.

35Iwe udzanena kuti, “Anandimenya, koma sindinapwetekedwe!

Andimenya koma sindinamve kanthu!

Kodi ndidzuka nthawi yanji?

Ndiye ndifunefunenso vinyo wina.”