箴言 10 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

箴言 10:1-32

所羅門的箴言

1以下是所羅門的箴言:

智慧兒使父親快樂,

愚昧兒叫母親擔憂。

2不義之財毫無益處,

公義救人脫離死亡。

3耶和華不讓義人挨餓,

祂使惡人的奢望成空。

4遊手好閒招致貧窮,

勤奮努力帶來富足。

5精明兒夏季時貯藏,

不肖子收成時酣睡。

6祝福臨到義人的頭,

殘暴充滿惡人的口。

7義人流芳於世,

惡人名聲朽爛。

8心存智慧的接受誡命;

說話愚昧的自招滅亡。

9行正道者活得安穩,

走歪路者終必敗露。

10擠眉弄眼,帶來憂傷;

胡言亂語,導致滅亡。

11義人的口是生命之泉,

惡人的口卻充滿殘暴。

12恨能挑起各樣紛爭,

愛能遮掩一切過犯。

13明哲人口中有智慧,

無知者背上受鞭打。

14智者儲藏知識,

愚人口惹禍端。

15錢財是富人的堅壘,

貧乏帶給窮人毀滅。

16義人的報酬是生命,

惡人的果子是懲罰。

17聽從教誨的,走生命之路;

拒絕責備的,必步入歧途。

18暗藏仇恨的滿口虛謊,

散佈流言的愚不可及。

19言多必失,智者慎言。

20義人之舌似純銀,

惡人之心無價值。

21義人的口滋養眾人,

愚人因無知而死亡。

22耶和華的祝福使人富足,

祝福中不加任何憂愁10·22 祝福中不加任何憂愁」或譯「勞苦無法使其加增」。

23愚人以惡為樂,

哲士喜愛智慧。

24惡人所怕的必臨到他,

義人的心願必得實現。

25暴風掃過,

惡人消逝無蹤,

義人永不動搖。

26雇用懶惰人,

如醋倒牙,如煙薰目。

27敬畏耶和華的享長壽,

惡人的壽數必被縮短。

28義人的憧憬帶來歡樂,

惡人的希望終必破滅。

29耶和華的道保護正直人,

毀滅作惡之人。

30義人永不動搖,

惡人無處容身。

31義人的口發出智慧,

詭詐的舌必被割掉。

32義人說話得體合宜,

惡人的口胡言亂語。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 10:1-32

Miyambo ya Solomoni

1Miyambo ya Solomoni:

Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,

koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.

2Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa,

koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.

3Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala;

koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa.

4Wochita zinthu mwaulesi amasauka,

koma wogwira ntchito mwakhama amalemera.

5Amene amakolola nthawi yachilimwe ndi mwana wanzeru,

koma amene amangogona nthawi yokolola ndi mwana wochititsa manyazi.

6Madalitso amakhala pa mutu wa munthu wolungama,

koma pakamwa pa munthu woyipa pamaphimba chiwawa.

7Munthu wolungama anzake adzamukumbukira ngati mdalitso,

koma dzina la munthu woyipa lidzayiwalika.

8Munthu wa mtima wanzeru amasamala malamulo,

koma chitsiru chomangolongolola chidzawonongeka.

9Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka;

koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.

10Aliyense wotsinzinira maso mwachinyengo amabweretsa mavuto,

koma wodzudzula chitsiru molimba mtima amabweretsa mtendere.

11Pakamwa pa munthu wolungama ndi kasupe wamoyo,

koma pakamwa pa munthu woyipa pamabisa chiwawa.

12Udani umawutsa mikangano,

koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

13Nzeru imapezeka pa milomo ya munthu wozindikira zinthu,

koma pa msana pa munthu wopanda nzeru sipachoka chikwapu.

14Anzeru amasunga chidziwitso

koma pakamwa pa chitsiru pamatulutsa zowononga.

15Chuma cha munthu wolemera

ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka.

16Moyo ndiye malipiro a munthu wolungama,

koma phindu la anthu oyipa ndi uchimo ndi imfa.

17Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo,

koma wonyoza chidzudzulo amasochera.

18Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama,

ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.

19Mawu akachuluka zolakwa sizisowa,

koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.

20Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri,

koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu.

21Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri;

koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru.

22Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma,

ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.

23Kwa chitsiru kuchita zinthu zoyipa ndiye chinthu chomusangalatsa,

koma kwa munthu womvetsa bwino zinthu nzeru ndiyo imamusangalatsa.

24Chimene munthu woyipa amachiopa chidzamuchitikira;

chimene munthu wolungama amachilakalaka adzachipeza.

25Pamene namondwe wawomba, anthu oyipa amachotsedwa,

koma anthu olungama amakhazikika mpaka muyaya.

26Momwe amakhalira vinyo wosasa mʼkamwa ndi momwe umakhalira utsi mʼmaso,

ndi momwenso amakhalira munthu waulesi kwa amene amutuma.

27Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo;

koma zaka za anthu oyipa zidzafupikitsidwa.

28Chiyembekezo cha olungama chimapatsa chimwemwe,

koma chiyembekezo cha anthu ochimwa chidzafera mʼmazira.

29Njira za Yehova ndi linga loteteza anthu ochita zabwino,

koma wochita zoyipa adzawonongeka.

30Munthu wolungama sadzachotsedwa, pamalo pake

koma oyipa sadzakhazikika pa dziko.

31Pakamwa pa munthu wolungama pamatulutsa za nzeru,

koma lilime lokhota lidzadulidwa.

32Milomo ya anthu olungama imadziwa zoyenera kuyankhula,

koma pakamwa pa anthu ochimwa pamatulutsa zokhota zokhazokha.