民數記 26 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

民數記 26:1-65

第二次人口統計

1瘟疫過後,耶和華對摩西亞倫祭司的兒子以利亞撒說: 2「你們要統計以色列全體會眾,按宗族登記所有二十歲以上、有作戰能力的男子。」 3摩西以利亞撒祭司就在約旦河邊、耶利哥對面的摩押平原對以色列人說: 4「你們要按照耶和華的吩咐統計二十歲以上的男子。」

以下是從埃及出來的以色列人。

5以色列的長子是呂便呂便的子孫有哈諾族、法路族、 6希斯倫族和迦米族, 7共登記了四萬三千七百三十人。 8法路的兒子是以利押9以利押的兒子是尼姆利大坍亞比蘭大坍亞比蘭原是會眾所推選的首領,他們與可拉一夥一起反叛摩西亞倫,反叛耶和華, 10以致大地裂開將他們全部吞了下去,當時大火還燒滅了二百五十人——成了後人的警戒。 11然而,可拉的子孫沒有被滅絕。

12西緬的子孫有尼姆利族、雅憫族、雅斤族、 13謝拉族和掃羅族, 14共登記了兩萬二千二百人。

15迦得的子孫有洗分族、哈基族、書尼族、 16阿斯尼族、以利族、 17亞律族和亞列利族, 18共登記了四萬零五百人。

19猶大的兒子俄南死在迦南20猶大的子孫有示拉族、法勒斯族、謝拉族。 21法勒斯的子孫有希斯倫族和哈姆勒族。 22這些是猶大各宗族,共登記了七萬六千五百人。

23以薩迦的子孫有陀拉族、普瓦族、 24雅述族和伸崙族, 25共登記了六萬四千三百人。

26西布倫的子孫有西烈族、以倫族和雅利族, 27共登記了六萬零五百人。

28約瑟的兒子有瑪拿西以法蓮29瑪拿西的子孫有瑪吉族和基列族。基列瑪吉的兒子。 30基列的子孫有伊以謝族、希勒族、 31亞斯烈族、示劍族、 32示米大族和希弗族。 33希弗的兒子西羅非哈沒有兒子,只有女兒瑪拉挪阿曷拉密迦得撒34這些是瑪拿西各宗族,共登記了五萬二千七百人。

35以法蓮的子孫有書提拉族、比結族和他罕族。 36書提拉的子孫有以蘭族。 37這些是以法蓮各宗族,共登記了三萬二千五百人,都是約瑟的子孫。

38便雅憫的子孫有比拉族、亞實別族、亞希蘭族、 39書反族和戶反族。 40比拉的子孫有亞勒族和乃幔族。 41這些是便雅憫各宗族,共登記了四萬五千六百人。

42的子孫有書含族, 43共登記了六萬四千四百人。

44亞設的子孫有音拿族、亦施韋族和比利亞族。 45比利亞的子孫有希別族和瑪結族。 46亞設的女兒名叫西拉47這些是亞設各宗族,共登記了五萬三千四百人。

48拿弗他利的子孫有雅薛族、沽尼族、 49耶色族和示冷族, 50共登記了四萬五千四百人。

51登記的以色列男子共有六十萬一千七百三十人。

52耶和華對摩西說: 53「你要按著各支派登記的人數把土地分給他們作產業; 54人數多的多分產業,人數少的少分產業,要按登記的人數分配。 55以色列人要按各自的支派抽籤分地,承受產業。 56無論大小支派,都要用抽籤的方法分配產業。」

57利未的子孫有革順族、哥轄族和米拉利族。 58立尼族、希伯崙族、瑪利族、姆示族和可拉族也是利未的子孫。哥轄暗蘭59暗蘭的妻子叫約基別,是利未女子,出生在埃及。她給暗蘭生了亞倫摩西和他們的姐姐米利暗60亞倫拿答亞比戶以利亞撒以他瑪61拿答亞比戶因用凡火向耶和華獻祭而被擊殺。 62利未人中一個月以上的男性共登記了兩萬三千人,他們的人數沒有登記在以色列人中,因為他們在以色列人中不分產業。

63以上是摩西以利亞撒祭司在約旦河邊、耶利哥對面的摩押平原統計的人數, 64其中沒有一個是摩西和祭司亞倫從前在西奈曠野登記的人。 65因為耶和華說過,那批人都要死在曠野。果然,除了耶孚尼的兒子迦勒的兒子約書亞以外,上次登記的人無一存活。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 26:1-65

Kalembera Wachiwiri

1Utatha mliri Yehova anati kwa Mose ndi Eliezara mwana wa Aaroni, 2“Werengani Aisraeli onse mwa mabanja awo, onse a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli.” 3Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti, 4“Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.”

Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa:

5Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi:

kuchokera mwa Hanoki, fuko la Ahanoki;

kuchokera mwa Palu, fuko la Apalu;

6kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi;

kuchokera mwa Karimi, fuko la Akarimi.

7Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730.

8Mwana wa Palu anali Eliabu, 9ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova. 10Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo. 11Koma ana a Kora sanafe nawo.

12Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele;

kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini;

kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini;

13kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera;

kuchokera mwa Sauli, fuko la Asauli.

14Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200.

15Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi:

kuchokera mwa Zefoni, fuko la Azefoni;

kuchokera mwa Hagi, fuko la Ahagi;

kuchokera mwa Suni, fuko la Asuni;

16kuchokera mwa Ozini, fuko la Aozini;

kuchokera mwa Eri, fuko la Aeri;

17kuchokera mwa Arodi, fuko la Aarodi;

kuchokera mwa Arieli, fuko la a Areli.

18Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500.

19Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani.

20Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Sela, fuko la Asera;

kuchokera mwa Perezi, fuko la Aperezi;

kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera.

21Zidzukulu za Perezi zinali izi:

kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi;

kuchokera mwa Hamuli, fuko la Ahamuli.

22Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500.

23Zidzukulu za Isakara monga mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Tola, fuko la Atola;

kuchokera mwa Puwa, fuko la Apuwa;

24kuchokera mwa Yasubu, fuko la Ayasubu.

Kuchokera mwa Simironi, fuko la Asimironi.

25Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300.

26Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Seredi, fuko la Aseredi;

kuchokera mwa Eloni, fuko la Aeloni;

kuchokera mwa Yahaleeli, fuko la Ayahaleeli.

27Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500.

28Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi:

29Zidzukulu za Manase:

kuchokera mwa Makiri, fuko la Amakiri (Makiri anali abambo ake a Giliyadi);

kuchokera mwa Giliyadi, fuko la Agiliyadi.

30Izi ndizo zinali zidzukulu za Giliyadi;

kuchokera mwa Iyezeri, fuko la Aiyezeri;

kuchokera mwa Heleki, fuko la Aheleki;

31kuchokera mwa Asirieli, fuko la Aasirieli;

kuchokera mwa Sekemu, fuko la Asekemu;

32kuchokera mwa Semida, fuko la Asemida;

kuchokera mwa Heferi, fuko la Aheferi.

33(Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.)

34Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700.

35Zidzukulu za Efereimu monga mwa mafuko awo zinali izi;

kuchokera mwa Sutela, fuko la Asutela;

kuchokera mwa Bekeri, fuko la Abekeri;

kuchokera mwa Tahani, fuko la Atahani.

36Zidzukulu za Sutela zinali izi:

kuchokera mwa Erani, fuko la Aerani.

37Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500.

Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo.

38Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi:

kuchokera mwa Bela, fuko la Abela;

kuchokera mwa Asibeli, fuko la Aasibeli;

kuchokera mwa Ahiramu, fuko la Ahiramu;

39kuchokera mwa Sufamu, fuko la Asufamu;

kuchokera mwa Hufamu, fuko la Ahufamu;

40Zidzukulu za Bela kupyolera mwa Aridi ndi Naamani zinali izi:

kuchokera mwa Aridi, fuko la Aaridi;

kuchokera mwa Naamani, fuko la Anaamani;

41Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600.

42Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi:

kuchokera mwa Suhamu fuko la Asuhamu.

Izi zinali zidzukulu za Dani. 43Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400.

44Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Imina, fuko la Aimuna;

kuchokera mwa Isivi, fuko la Ayisivi;

kuchokera mwa Beriya, fuko la Aberiya;

45ndipo kupyolera mwa zidzukulu za Beriya:

kuchokera mwa Heberi, fuko la Aheberi;

kuchokera mwa Malikieli, fuko la Amalikieli;

46(Aseri anali ndi mwana wamkazi dzina lake Sera)

47Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400.

48Zidzukulu za Nafutali mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Yahazeeli, fuko la Ayahazeeli;

kuchokera mwa Guni, fuko la Aguni;

49kuchokera mwa Yezeri, fuko la Ayezeri;

kuchokera mwa Silemu, fuko la Asilemu.

50Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400.

51Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730.

52Yehova anawuza Mose kuti, 53“Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo. 54Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa. 55Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo. 56Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.”

57Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa:

kuchokera mwa Geresoni, fuko la Ageresoni;

kuchokera mwa Kohati, fuko la Akohati;

kuchokera mwa Merari, fuko la Amerari.

58Awanso anali mabanja a Alevi:

banja la Alibini,

banja la Ahebroni,

banja la Amali,

banja la Amusi, fuko la Kora

banja la Akohati,

(Kohati anali abambo a Amramu. 59Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo. 60Aaroni anali abambo a Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. 61Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo).

62Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo.

63Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko. 64Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai; 65Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.