撒迦利亞書 1 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

撒迦利亞書 1:1-21

呼喚人民歸向耶和華

1大流士王二年八月,耶和華對易多的孫子、比利迦的兒子撒迦利亞先知說: 2「耶和華曾對你們的祖先大發怒氣。 3因此,你要告訴百姓,萬軍之耶和華說,『你們要歸向我,我就回到你們那裡。這是萬軍之耶和華說的。 4不要像你們的祖先一樣。以前的先知曾呼喚他們要聽從萬軍之耶和華的話,改邪歸正,停止作惡,他們卻置若罔聞,不予理會。這是耶和華說的。 5現在你們的祖先在哪裡呢?那些先知能活到永遠嗎? 6然而,我吩咐我僕人——眾先知的訓言和律例豈不應驗在你們祖先的頭上了嗎?後來他們悔改了,說,萬軍之耶和華按著我們的所作所為報應了我們,正如祂所言。』」

有關騎士的異象

7大流士王二年十一月,即細罷特月二十四日,耶和華的話傳給了易多的孫子、比利迦的兒子撒迦利亞先知。 8我在夜間看到異象,見有人騎著一匹紅馬,站在谷中的番石榴樹林間,後面有紅馬、棕馬和白馬騎士。 9我就問:「主啊,這是什麼意思?」那位跟我說話的天使說:「我會告訴你這是什麼意思。」 10站在番石榴樹林間的那位對我說:「這些是耶和華派來巡視大地的。」 11其他騎士向站在番石榴樹林間的那位耶和華的天使報告說:「我們已經巡視了大地,到處都安寧平靜。」

12耶和華的天使說:「萬軍之耶和華啊,你向耶路撒冷猶大的城邑發怒已經七十年了,還要多久你才會憐憫他們呢?」 13耶和華用仁慈、安慰的話回答那位與我說話的天使。

14那位天使對我說:「你要宣告,萬軍之耶和華說,『我對耶路撒冷,對錫安充滿了火熱的愛。 15我對安逸的列國充滿憤怒,因為我只是對我的子民稍微不滿,列國卻大肆禍害他們。』 16因此,耶和華說,『我必懷著憐憫的心回到耶路撒冷,我的殿必在那裡重建,必有準繩丈量耶路撒冷。這是萬軍之耶和華說的。』 17你還要宣告,萬軍之耶和華說,『我的城邑必再次繁榮昌盛,耶和華必再次安慰錫安,揀選耶路撒冷。』」

有關角和工匠的異象

18我又舉目觀看,見有四個角。 19於是,我問與我說話的天使:「這是什麼?」他回答說:「這些是驅散猶大以色列耶路撒冷的角。」 20耶和華又讓我看見四個工匠。 21於是我問:「他們來做什麼?」他說:「這些角驅散了猶大,以致無人能抬頭,但這些工匠是來威嚇列國,並打掉他們用來攻擊和驅散猶大的角。」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 1:1-21

Yuda Abwerera kwa Yehova

1Mwezi wachisanu ndi chitatu, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi mneneri Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido, kuti:

2“Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu. 3Choncho awuze anthuwa kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Bwererani kwa Ine,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. 4Musakhale ngati makolo anu, amene aneneri akale anawalalikira kuti: Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Tsopano lekani njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu oyipawo.’ Koma iwo sanamvere kapena kulabadira za Ine, akutero Yehova. 5Kodi makolo anuwo ali kuti tsopano? Nanga aneneri, kodi amakhalapo mpaka muyaya? 6Kodi mawu anga ndi malangizo anga, amene ndinawawuza atumiki anga aneneri, suja anawachitira makolo anu?

“Tsono iwo analapa ndi kunena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse watichitira zomwe zikuyenera njira zathu ndi machitidwe athu, monga anatsimikiza kuti adzachita.’ ”

Munthu Pakati pa Mitengo ya Mchisu

7Tsiku la 24 la mwezi wa 11, mwezi wa Sebati, chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido.

8Nthawi ya usiku ndinaona masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Iye anayima pakati pa mitengo ya mchisu mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali akavalo ofiira, akhofi ndi oyera.

9Ine ndinafunsa kuti, “Mbuye wanga, kodi zimenezi ndi chiyani?”

Mngelo amene amayankhula nane anayankha kuti, “Ndidzakuonetsa kuti zimenezi ndi chiyani.”

10Pamenepo munthu amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu anafotokoza kuti, “Amenewa ndiwo amene Yehova wawatuma kuti ayendere dziko lonse lapansi.”

11Ndipo okwera pa akavalo enawo anafotokoza kwa mngelo wa Yehova, amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu kuti, “Ife tayendera dziko lonse lapansi ndipo tapeza kuti dziko lonselo lili pa bata ndi mtendere.”

12Tsono mngelo wa Yehova anati, “Yehova Wamphamvuzonse, kodi mpaka liti mudzakhala osaonetsa chifundo chanu kwa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda, amene mwawakwiyira kwa zaka izi 70?” 13Choncho Yehova anayankhula mawu abwino ndi achitonthozo kwa mngelo amene ankayankhula nane.

14Pamenepo mngelo amene ankayankhula nane anati, “Lengeza mawu awa: Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndikuchitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni, 15koma ndakwiya kwambiri ndi anthu a mitundu ina amene akuganiza kuti ali pa mtendere. Ndinakwiyira anthu anga pangʼono pokha, koma iwo anawonjeza kuzunza anthu angawo.’

16“Choncho, Yehova akuti, ‘Ndidzabwerera ku Yerusalemu ndi mtima wachifundo, nyumba yanga adzayimanganso kumeneko. Ndipo adzatenganso chingwe choyezera kuti amange Yerusalemu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.

17“Lengezanso kuti, Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Mizinda yanga idzakhalanso ndi zokoma zosefukira ndipo Yehova adzatonthoza Ziyoni ndi kusankhanso Yerusalemu.’ ”

Nyanga Zinayi ndi Amisiri Azitsulo Anayi

18Kenaka ndinayangʼananso, ndipo patsogolo panga panali nyanga zinayi. 19Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi ndi chiyani?”

Iye anandiyankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, Israeli ndi Yerusalemu.”

20Kenaka Yehova anandionetsa amisiri azitsulo anayi. 21Ndinafunsa kuti, “Amisiri a zitsulowa akudzachita chiyani?”

Iye anayankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda kotero kuti panalibe wina amene akanalimbana nazo, koma amisiri a zitsulowa abwera kudzaziopseza ndi kugwetsa nyanga zimenezi za mitundu ya anthu amene analimbana ndi dziko la Yuda ndi kubalalitsa anthu ake.”