撒母耳記下 9 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

撒母耳記下 9:1-13

大衛恩待米非波設

1大衛問:「掃羅一家還有什麼人嗎?我要因為和約拿單的情義而恩待他。」 2有人就去叫掃羅家一個名叫洗巴的僕人來見大衛,王問他:「你就是洗巴嗎?」他說:「僕人正是洗巴。」 3王說:「掃羅家中還有什麼人?我要以上帝的慈愛來待他。」洗巴答道:「約拿單還有一個兒子,是雙腳殘廢的。」 4王說:「他在哪裡?」洗巴答道:「他住在羅·底巴,在亞米利的兒子瑪吉家裡。」 5於是,大衛王派人去羅·底巴把他從亞米利的兒子瑪吉家裡接來。 6掃羅的孫子、約拿單的兒子米非波設來到大衛面前,向他俯伏叩拜。大衛說:「米非波設!」米非波設答道:「僕人在這裡。」 7大衛說:「你不用害怕,我要因為和你父親約拿單的情義而恩待你。我要把你祖父掃羅所有的田地歸還給你,你要常與我同席吃飯。」 8米非波設再次叩拜,說:「僕人算什麼?不過像一條死狗罷了,你竟這樣眷顧我!」

9王又把掃羅的僕人洗巴召來,對他說:「我已把掃羅全家的產業都賜給了你主人的孫子米非波設10你和你的兒子及僕人要為米非波設種田,把出產拿來供養他。他還要常常與我同席吃飯。」洗巴有十五個兒子,二十個僕人。 11洗巴對王說:「僕人必遵行我主我王的一切吩咐。」於是,米非波設像王子一樣常與大衛同席吃飯。 12米非波設有一個小兒子名叫米迦洗巴家中的人都做了米非波設的僕人。 13從此,雙腳殘廢的米非波設就住在耶路撒冷,常常與王同席吃飯。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 9:1-13

Davide ndi Mefiboseti

1Davide anafunsa kuti, “Kodi alipo amene watsala mʼbanja la Sauli kuti ndimuchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?”

2Tsono panali mtumiki wina wa banja la Sauli wotchedwa Ziba. Iwo anamuyitana kuti aonekere pamaso pa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Ziba?”

Iyeyo anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”

3Mfumu inafunsa kuti, “Kodi palibe amene watsala wa banja la Sauli amene ndingamuchitire chifundo cha Mulungu?”

Ziba anayankha mfumu kuti, “Alipo mwana wa Yonatani, koma ndi wolumala mapazi ake onse.”

4Mfumu inafunsa kuti, “Ali kuti?”

Ziba anayankha kuti, “Iye ali ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli ku Lodebara.”

5Kotero mfumu inamubweretsa kuchokera ku Lodebara, ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli.

6Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye.

Davide anati, “Mefiboseti!”

Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”

7Davide anati kwa iye, “Usachite mantha, pakuti ndidzakuchitira ndithu chifundo chifukwa cha abambo ako Yonatani. Ine ndidzakubwezera iwe dziko lonse limene linali la agogo ako Sauli, ndipo iweyo udzadya ndi ine nthawi zonse.”

8Mefiboseti anawerama pansi ndipo anati, “Mtumiki wanu ndine yani kuti musamale galu wakufa ngati ine?”

9Kenaka Davide anayitanitsa Ziba, mtumiki wa Sauli, ndipo anati, “Ine ndapereka kwa chidzukulu cha mbuye wako chilichonse chimene chinali cha Sauli ndi banja lake. 10Iwe ndi ana ndi antchito anu muzimulimira mʼdziko lake ndipo muzibweretsa zokololazo kuti chidzukulu cha mbuye wako chikhale ndi chakudya. Ndipo Mefiboseti, chidzukulu cha mbuye wako adzadya ndi ine nthawi zonse.” (Tsono Ziba anali ndi ana aamuna khumi ndi asanu ndi antchito makumi awiri).

11Ndipo Ziba anati kwa mfumu, “Mtumiki wanu adzachita chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mudzalamulire wantchito wanu kuti achite.” Kotero Mefiboseti ankadya ndi Davide monga mmodzi wa ana a mfumu.

12Mefiboseti anali ndi mwana wamngʼono wamwamuna wotchedwa Mika, ndipo onse a banja la Ziba anali antchito a Mefiboseti. 13Ndipo Mefiboseti anakhala mu Yerusalemu chifukwa nthawi zonse amadya ndi mfumu. Iye anali wolumala mapazi ake onse.