撒母耳記下 7 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

撒母耳記下 7:1-29

上帝對大衛的應許

1大衛住在王宮裡,耶和華使他安享太平,不受四圍的仇敵侵擾。 2一天,王對拿單先知說:「你看!我住在香柏木造的王宮中,但上帝的約櫃還留在帳篷裡。」 3拿單答道:「你只管照著自己的想法去做吧,因為耶和華與你同在。」 4當晚耶和華對拿單說: 5「你去告訴我的僕人大衛,『耶和華說,你豈是為我建造殿宇的人? 6從我把以色列人帶出埃及那天起,直到今天,我從未住過殿宇,一路上都住在帳篷裡。 7在我與以色列人同行的日子,我從未責問任何我委派牧養我子民的士師,你為何不為我建香柏木的殿宇呢?』

8「現在你要告訴我的僕人大衛,萬軍之耶和華說,『你原本在草場牧羊,我召你來做我以色列子民的首領。 9無論你去哪裡,我都與你同在,為你剷除所有仇敵。現在我要使你聲名遠播,與世上的偉人齊名。 10-11我必為我的以色列子民預備一個地方,栽培他們,讓他們住在自己的家園,不再受驚擾,不會像從前我設立士師治理他們的時候那樣受惡人壓迫。我必使你安定,免受仇敵的侵擾。我耶和華向你宣告,我必建立你的王室。 12你壽終正寢、與祖先同眠之後,我必立你的後裔接替你的王位,使他江山穩固。 13他必為我的名建造聖殿,我必使他的王位堅立,直到永遠。 14我要做他的父親,他要做我的兒子。如果他犯了罪,我必用人的杖、世人的鞭子來懲治他, 15但我的慈愛卻不會像離開從你面前被廢的掃羅那樣離開他。 16你的家和你的國必在我面前永遠堅立,你的王位必永遠穩固。』」

17拿單就把所聽到的啟示全部告訴大衛

大衛的禱告

18於是,大衛王走進會幕,在耶和華面前坐下,說:「主耶和華啊,我是誰?我的家算什麼?你竟如此厚待我。 19主耶和華啊,你覺得這還不夠,你還要施恩賜福給你僕人的後代。主耶和華啊,這樣的福分豈是常人可以得到的? 20主耶和華啊,我還能對你說什麼呢?你深知你的僕人。 21你讓僕人知道你憑自己的應許、按自己的旨意行了這大事。 22主耶和華啊,你真偉大!我們從未聽過有誰能與你相比,你是獨一無二的上帝。 23世上哪個民族比得上你的以色列子民呢?你從埃及救出他們,讓他們做你的子民,又彰顯你的大名,行神蹟奇事,把列國及其神明從你的以色列子民面前趕走。 24你讓以色列人永遠做你的子民,你耶和華做他們的上帝。

25「耶和華上帝啊,求你永遠信守你對僕人和僕人家的應許。 26這樣,你的名必永遠被尊崇,人們必說,『萬軍之耶和華是治理以色列的上帝。』願你僕人大衛的家在你面前堅立。 27以色列的上帝——萬軍之耶和華啊,因為你曾啟示僕人,說你要使我家世代為王,僕人才有勇氣這樣向你禱告。 28主耶和華啊,只有你是上帝,你的話真實可靠,你給了僕人美好的應許。 29現在求你賜福給僕人家,讓僕人家在你面前永續不斷。主耶和華啊,這些都是你的應許,願你永遠賜福給僕人家。」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 7:1-29

Lonjezo la Mulungu kwa Davide

1Mfumu itakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, Yehova atayipatsa mpumulo kwa adani ake onse woyizungulira, 2mfumuyo inawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Mulungu lili mu tenti.”

3Natani anayankha mfumu kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu chifukwa Yehova ali nanu.”

4Usiku umenewo mawu a Yehova anafika kwa Natani ndipo anati,

5“Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti: kodi ndiwe amene udzandimangira Ine nyumba yokhalamo? 6Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali mu tenti. 7Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense atsogoleri awo, amene ndinamulamula kuweta anthu anga Aisraeli kuti, nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ”

8“Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli. 9Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi. 10Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja, 11monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzakupatsaninso mpumulo kwa adani anu onse.

“ ‘Yehova akulengeza kwa iwe kuti Iye mwini adzakhazikitsa banja lako: 12Masiku ako akadzatha ndipo ukadzakapuma ndi makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, imene idzachokera mʼthupi mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. 13Iye ndiye amene adzamangire nyumba Dzina langa, ndipo Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya. 14Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Akadzachita choyipa, Ineyo ndidzamulanga ndi ndodo ndi zikwapu za anthu. 15Koma sindidzasiya kumukonda, monga ndinachitira ndi Sauli, amene ndinamuchotsa iwe usanakhale mfumu. 16Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhala zamuyaya pamaso panga. Mpando wako waufumu udzakhazikika kwamuyaya!’ ”

17Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira.

Pemphero la Davide

18Choncho Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati:

“Inu Yehova Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa?” 19Ndipo kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse, mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Kodi umu ndi mmene mumachitira ndi munthu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse?

20Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu? Pakuti Inu Ambuye Wamphamvuzonse mukumudziwa mtumiki wanu. 21Chifukwa cha mawu anu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwachiwulula kwa mtumiki wanu.

22Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu. 23Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina ndi milungu yawo pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto? 24Inu mwawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo.

25“Ndipo tsopano Yehova Mulungu, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake. Chitani monga mwalonjezera, 26kotero dzina lanu lidzakhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.

27“Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, mwaululira mtumiki wanu ponena kuti, ‘Ine ndidzakumangira iwe nyumba!’ Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. 28Inu Ambuye Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu! Mawu anu ndi odalirika, ndipo mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu. 29Ndipo tsopano chikukomereni kudalitsa banja la mtumiki wanu, kuti likhale mpaka muyaya pamaso panu. Pakuti Inu, Yehova Wamphamvuzonse, mwayankhula, ndipo ndi mʼdalitso wanu banja la mtumiki wanu lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”