撒母耳記下 1 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

撒母耳記下 1:1-27

大衛得知掃羅的死訊

1大衛戰勝了亞瑪力人之後便回到洗革拉,在那裡住了兩天。那時掃羅已經死了。 2第三天,有一個衣服撕裂、頭蒙灰塵的人從掃羅軍營中跑到大衛面前,俯伏下拜。 3大衛問他:「你從哪裡來?」那人答道:「我是從以色列軍營逃出來的。」 4大衛說:「請告訴我那邊的情況。」他說:「以色列軍潰逃,傷亡慘重,掃羅和他兒子約拿單都死了!」 5大衛又問報信的青年:「你怎麼知道掃羅和他兒子約拿單死了?」 6青年說:「我偶然到基利波山,看見掃羅在那裡扶槍而立,敵人的戰車騎兵緊緊追來。 7他回頭看到我,便呼喚我。我說,『我在這裡。』 8他問我是什麼人。我告訴他我是亞瑪力人。 9掃羅說他痛苦難當,卻又死不掉,要我殺了他。 10我知道他身受重傷,必死無疑,就把他殺了,並取下他頭上的王冠和臂上的鐲子帶來獻給我主。」

11大衛就撕裂衣服,他的隨從也撕裂衣服。 12他們因掃羅、他的兒子約拿單和耶和華的子民——以色列同胞陣亡而悲哀痛哭,禁食直到黃昏。 13大衛又問報信的青年:「你是哪裡的人?」他答道:「我是寄居在以色列亞瑪力人。」 14大衛說:「你怎麼敢下手殺耶和華所膏立的王? 15-16你是咎由自取!因為你親口承認自己殺了耶和華所膏立的王。」大衛隨即命令一個年輕的隨從殺死他,隨從便殺死了他。

大衛的哀歌

17大衛作了一首輓歌哀悼掃羅和他兒子約拿單18並吩咐人教導猶大人唱這首弓歌。這首歌記在《雅煞珥書》上,歌詞說:

19以色列啊,

你榮耀的王伏屍山上,

偉大的勇士竟然倒下!

20不要在迦特宣告,

不要在亞實基倫的街上傳揚,

免得非利士的婦女幸災樂禍,

免得未受割禮之人的女子歡喜雀躍。

21基利波山啊,願你沒有雨露,

你的田地不長獻祭用的五穀,

因為在那裡勇士的盾牌污跡斑斑,

掃羅的盾牌沒有抹油。

22約拿單的弓射敵無數,

掃羅的劍不殺強敵不收回。

23掃羅約拿單深受愛戴,

生死不分離。

他們比鷹更敏捷,

比獅子還強壯。

24以色列的女子啊,

掃羅哀哭吧!

他曾使你們衣服華美,

穿金戴銀。

25「勇士竟戰死沙場!

約拿單竟伏屍山上!

26我的兄弟約拿單啊,

我為你悲傷,

你對我情深義重,

你對我的愛勝過女人的戀情。

27「偉大的勇士竟然倒下!

兵器竟然長埋!」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 1:1-27

Davide Amva za Imfa ya Sauli

1Atamwalira Sauli, Davide anabwerako kumene anakagonjetsa Aamaleki ndipo anakakhala ku Zikilagi masiku awiri. 2Pa tsiku lachitatu munthu wina wochokera ku msasa wa Sauli anafika, zovala zake zitangʼambika ndiponso anali atathira dothi pamutu pake. Atafika kwa Davide, anadzigwetsa pansi, kupereka ulemu kwa Davideyo.

3Davide anamufunsa iye kuti, “Kodi iwe wachokera kuti?”

Iye anayankha kuti, “Ine ndathawa ku misasa ya Aisraeli.”

4Davide anafunsa, “Tandiwuza, chachitika ndi chiyani?”

Iye anati, “Anthu athawa ku nkhondo ndipo ambiri aphedwa. Sauli ndi mwana wake Yonatani aphedwa.”

5Ndipo Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa nkhaniyi, “Ukudziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afa?”

6Mnyamatayo anati, “Zinangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa, ndipo Sauli anali komweko ataweramira pa mkondo wake, pamodzi ndi magaleta ndi okwera ake atamuyandikira. 7Pamene anatembenuka ndi kundiona ine, iye anandiyitana, ndipo ndinati, ‘Kodi ndichite chiyani?’ ”

8Iye anandifunsa, “Iwe ndiwe yani?”

Ine ndinayankha kuti, “Ndine Mwamaleki.”

9“Kenaka iye anati kwa ine, ‘Bwera pafupi ndipo undiphe! Ndikumva ululu kwambiri, koma ndikanali ndi moyo!’

10“Kotero ndinabwera pafupi ndi kumupha, chifukwa ndinadziwa kuti mmene anagweramo sakanakhalanso ndi moyo. Ndipo ndatenga chipewa chaufumu chimene chinali pamutu pake ndi khoza la pa dzanja lake ndipo ndazibweretsa kwa inu mbuye wanga.”

11Apo Davide ndi anthu onse amene anali nawo anangʼamba zovala zawo. 12Iwo analira maliro ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi mwana wake Yonatani, komanso chifukwa cha gulu la ankhondo la Yehova ndi nyumba ya Israeli, chifukwa anaphedwa ndi lupanga.

13Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa uthengawo, “Iwe umachokera kuti?”

Iye anayankha kuti, “Ine ndine mwana wa mlendo Mwamaleki.”

14Davide anamufunsanso kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunaope kukweza dzanja lako ndi kupha wodzozedwa wa Yehova?”

15Kenaka Davide anayitana mmodzi mwa anyamata ake ndipo anati, “Pita ukamukanthe!” Kotero iye anapita kukamukantha, ndipo mnyamata uja anafa. 16Pakuti Davide anali atanena kwa iye kuti, “Iwe wadzipha wekha. Pakamwa pako pakunena zokutsutsa wekha, pamene unanena kuti, ‘Ine ndapha wodzozedwa wa Yehova.’ ”

Davide Alira Maliro a Sauli ndi Yonatani

17Davide anayimba nyimbo iyi ya maliro, kulira Sauli ndi mwana wake Yonatani. 18Ndipo analamula kuti anthu a ku Yuda aphunzitsidwe nyimbo ya maliroyi imene yalembedwa mʼbuku la Yasari:

19“Ulemerero wako iwe Israeli, wagona utaphedwa ku zitunda.

Taonani amphamvu agwa kumeneko!

20“Musakanene zimenezi ku Gati,

musazilengeze ku misewu ya ku Asikeloni,

kuti ana aakazi a Afilisti angasangalale,

ana aakazi a osachita mdulidwe angakondwere.

21“Inu mapiri a ku Gilibowa,

musakhalenso ndi mame kapena mvula,

kapena minda yobereka zopereka za ufa.

Pakuti kumeneko chishango cha munthu wamphamvu chinadetsedwa,

chishango cha Sauli sanachipakenso mafuta.

22“Pa magazi a ophedwa,

pa mnofu wa amphamvu,

uta wa Yonatani sunabwerere,

lupanga la Sauli silinabwere chabe.

23“Sauli ndi Yonatani,

pa moyo wawo anali okondedwa ndi okoma mtima,

ndipo pa imfa yawo sanasiyanitsidwe.

Iwo anali ndi liwiro loposa ziwombankhanga,

anali ndi mphamvu zoposa mkango.

24“Inu ana aakazi a Israeli,

mulireni Sauli,

amene anakuvekani zovala zofiira ndi zofewa,

amene anakometsera zovala zanu ndi zokometsera zagolide.

25“Taonani amphamvu agwa ku nkhondo!

Yonatani wagona ataphedwa ku zitunda.

26Ine ndikuvutika mumtima chifukwa cha iwe mʼbale wanga Yonatani,

unali wokondedwa kwambiri kwa ine.

Chikondi chako pa ine chinali chopambana,

chopambana kuposa chikondi cha akazi.

27“Taonani amphamvu agwa!

Zida zankhondo zawonongeka!”