尼希米記 9 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

尼希米記 9:1-38

以色列人認罪禱告

1這月二十四日,以色列人聚集禁食。他們身披麻衣,頭撒塵土。 2以色列人與其他外族人隔離,站著承認自己的罪惡和祖先的過犯。 3他們站在自己的地方,宣讀他們上帝耶和華的律法書,長達三個小時9·3 三個小時」希伯來文是「一天的四分之一」。。他們又用了三個小時認罪,敬拜他們的上帝耶和華。 4利未耶書亞巴尼甲篾示巴尼布尼示利比巴尼基拿尼站在臺上,大聲呼求他們的上帝耶和華。 5利未耶書亞甲篾巴尼哈沙尼示利比荷第雅示巴尼毗他希雅說:「起來稱頌你們的上帝耶和華,直到永永遠遠。耶和華啊,你榮耀的聖名當受稱頌!願你的名被尊崇,超過一切稱頌和讚美!

6「你,唯有你是耶和華!你造了天、天上的天和天上的萬象、地和地上的一切、海和海中的一切,你賜給他們生命。眾天軍都敬拜你。 7你是耶和華上帝,你揀選了亞伯蘭,帶他離開迦勒底吾珥,又給他改名為亞伯拉罕8你知道他對你忠心,就與他立約,把迦南人、人、亞摩利人、比利洗人、耶布斯人及革迦撒人的土地賜給他的後代。你實現了你的應許,因為你是公義的。

9「你看見我們祖先在埃及所受的苦,又聽見他們在紅海邊的呼求, 10就行神蹟奇事對付法老及其所有的臣僕和國民,因為你知道他們對以色列人行事狂傲。你使自己威名遠揚直到今日。 11你在我們祖先面前把海水分開,使他們在海中走乾地過去;你把追趕他們的人扔進深海,好像把石頭扔進大水中。 12白天,你用雲柱帶領他們;夜間,你用火柱照亮他們當走的路。 13你降臨在西奈山,從天上與他們說話,賜給他們公正的典章、信實的律法、美好的律例和誡命。 14你使他們知道你的神聖安息日,藉你僕人摩西賜給他們誡命、律例和法度。 15他們餓了,你賜下天糧給他們吃;他們渴了,你使磐石流出水給他們喝。你吩咐他們去佔領你起誓賜給他們的土地。 16但我們的祖先行事狂傲,頑固不化,不肯聽從你的誡命。 17他們拒絕聽從,忘記了你為他們所行的奇事,頑固不化,自立首領要回埃及做奴隸。但你是樂意饒恕,有恩典,有憐憫,不輕易發怒,充滿慈愛的上帝,你沒有離棄他們。 18縱使他們為自己鑄造了一頭牛犢,聲稱那是把他們帶出埃及的上帝,大大褻瀆了你, 19你還是對他們大施憐憫,沒有在曠野離棄他們。白天,雲柱沒有離開他們,仍然引導他們前行;夜間,火柱仍然照亮他們當走的路。 20你差遣你良善的靈去教導他們,沒有停止賜他們嗎哪吃,也沒有停止賜他們水喝。 21在曠野的四十年間,你供養他們,使他們一無所缺,他們的衣服沒有穿破,腳也沒有走腫。

22「你將列國和萬民賜給他們,為他們劃分疆界,他們佔領了希實本西宏巴珊的土地。 23你使他們的子孫多如天上的星星,你帶領他們進入你應許他們祖先的土地。 24他們的子孫進去佔領了那地方,你在他們面前制伏了那裡的迦南人,把迦南諸王和那地方的人交在他們手裡,任由他們處置。 25他們奪取堅固的城池、肥沃的土地、裝滿美物的房屋、挖好的水井、葡萄園、橄欖園以及各樣的果樹。他們吃得飽足,身體發胖,享受你的厚恩。

26「然而,他們不順從你,背叛你,把你的律法拋在背後,又殺掉勸誡他們歸向你的眾先知,大大褻瀆了你。 27於是你把他們交在欺壓他們的仇敵手中。他們在患難中向你呼求,你就從天上垂聽,懷著豐盛的憐憫賜給他們拯救者,把他們從仇敵手中拯救出來。 28可是,他們得享平安後,又在你面前作惡,於是你離棄他們,把他們交在敵人手中,使敵人統治他們。他們回轉向你呼求,你就從天上垂聽,你一次次地懷著憐憫拯救他們。 29你警告他們,要使他們遵守你的律法,但他們行事狂傲,不聽從你的誡命,干犯你的典章。人若遵行這典章就必存活,但他們背棄你,頑固不化,不肯聽從。 30你多年來容忍他們,差遣你的靈藉著你的眾先知警告他們,但他們依然不肯聽從,於是你把他們交在列邦手中。 31然而,你大施憐憫,沒有完全毀滅他們,也沒有離棄他們,因為你是有恩典和憐憫的上帝。

32「因此,我們的上帝啊,你是偉大、全能、可畏、守約、施慈愛的上帝,求你不要輕看我們的王、首領、祭司、先知、祖先和你的子民從亞述諸王時代直到今天所受的苦難。 33在這臨到我們的一切事上,你都是公義的,因為你行事信實,我們行事邪惡。 34我們的王、首領、祭司和祖先沒有遵行你的律法,也沒有留心聽從你的誡命和你給他們的警告。 35他們即使在本國,在你賜給他們廣闊肥沃的土地上得享你的厚恩,也不事奉你,不離開惡道。 36今天,我們淪為奴隸,在你賜給我們祖先的土地上,在你讓我們祖先享用其出產和各樣美物的土地上,我們淪為奴隸。 37因為我們的罪過,這地方的豐富出產都歸給了那些你派來統管我們的王。他們隨意統管我們和我們的牲畜。我們生活在極大的苦難中。

38「鑒於這一切,我們鄭重立約,記載下來。我們的首領、利未人和祭司都在上面蓋了印。」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nehemiya 9:1-38

Aisraeli Avomereza Kuchimwa Kwawo

1Pa tsiku la 24 la mwezi womwewo, Aisraeli anasonkhana pamodzi ndi kusala chakudya, kuvala ziguduli ndi kudzithira dothi pa mutu. 2Aisraeliwa anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anayimirira nayamba kuwulula machimo awo ndi zolakwa za makolo awo. 3Anthuwo anayimirira pomwepo, ndipo anamva mawu a mʼbuku la malamulo a Yehova akuwerengedwa kwa maora enanso atatu ndipo anakhala maora ena atatu akuwulula machimo awo ndi kupembedza Yehova Mulungu wawo. 4Pa makwerero okhalapo alevi anayimirirapo anthu awa: Yesuwa, Bani, Kadimieli, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani. Iwowa ankapemphera mokweza mawu kwa Yehova Mulungu wawo. 5Ndipo Alevi awa: Yesuwa, Kadimieli, Bani, Hasabaneya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya anati: “Imirirani ndipo mutamande Yehova Mulungu wanu, amene ndi wamuyaya.”

“Litamandike dzina lake laulemerero limene liposa madalitso ndi matamando onse. 6Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani.

7“Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumutulutsa mʼdziko la Uri wa ku Kaldeya ndi kumutcha dzina lake Abrahamu. 8Inu munaona kuti mtima wake unali wokhulupirika kwa inu, ndipo munapangana naye pangano lakuti mudzapereka kwa zidzukulu zake dziko la Akanaani Ahiti, Aamori, Aperezi, Ayebusi ndi Agirigasi. Inu mwasunga lonjezo lanu chifukwa ndinu wolungama.

9“Munaona kuzunzika kwa makolo athu ku Igupto. Munamva kufuwula kwawo pa Nyanja Yofiira. 10Inu munachita zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa kutsutsana ndi Farao, pamaso pa Farao, nduna zake ndi anthu onse a mʼdziko lake, pakuti Inu munadziwa kuti anazunza makolo athu. Inu munadzipangira nokha dzina, monga zilili mpaka lero lino. 11Inu munagawa nyanja anthu anu akupenya, kotero kuti anadutsa powuma, koma munamiza mʼmadzi akuya anthu amene ankawalondola monga mmene uchitira mwala mʼmadzi ozama. 12Masana munkawunikira ndi chipilala cha mtambo ndipo usiku munkawunikira ndi chipilala cha moto njira yonse imene ankayendamo.

13“Munatsika pa Phiri la Sinai, ndipo munawayankhula kuchokera kumwamba. Munawapatsa malangizo olungama, ziphunzitso zoona ndiponso malamulo abwino. 14Inu munawadziwitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi loyera ndipo munawapatsa malamulo ndi ziphunzitso. 15Pamene anali ndi njala munawapatsa buledi wochokera kumwamba. Pamene anali ndi ludzu munawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe. Munawawuza kuti apite kukalanda dziko limene munalonjeza kuti mudzawapatsa.”

16“Koma makolo athu anadzikuza ndi kuwumitsa khosi, ndipo iwo sanamvere malamulo anu. 17Anakana kumvera ndipo sanakumbukire zodabwitsa zimene munachita pakati pawo. Koma iwo anawumitsa khosi, nakuwukirani podzisankhira okha mtsogoleri kuti awatsogolere kubwerera ku ukapolo ku dziko la Igupto. Koma ndinu Mulungu wokhululukira, wokoma mtima ndi wachifundo wosapsa mtima msanga ndi wachikondi chachikulu chosasinthika. Choncho Inu simunawasiye. 18Ngakhale pamene iwo anadziwumbira fano la mwana wangʼombe ndi kuti, ‘Uyu ndi mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto,’ kapena pamene anachita chipongwe choopsa.

19“Koma Inu ndi chifundo chanu chachikulu, simunawasiye mʼchipululu. Chipilala cha mtambo sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo masana ndipo chipilala cha moto sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo usiku. 20Inu munawapatsa mzimu wanu wabwino kuti uwalangize. Inu simunawamane chakudya cha mana chija, ndipo munawapatsa madzi akumwa. 21Munawasunga zaka makumi anayi mʼchipululu ndipo sanasowe kanthu kalikonse. Zovala zawo sizinathe kapena mapazi awo kutupa.”

22“Inu munawapatsa mafumu ndi mayiko mʼmanja mwawo. Munawagawiranso mayiko achilendo akutali kwambiri. Munabwera nawo mʼdziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani kuti alowemo nʼkulitenga kukhala lawo. 23Munachulukitsa ana awo aamuna ngati nyenyezi za mlengalenga. Ndipo munawabweretsa mʼdziko limene munawuza makolo awo kuti alilowe ndi kulitenga. 24Choncho zidzukulu zawo zinapita ndi kukalandira dzikolo. Inu munagonjetsa pamaso pawo, Akanaani amene amakhala mʼdzikolo. Inde munapereka mʼmanja mwawo mafumu awo pamodzi ndi anthu a mʼdzikomo kuti achite nawo monga angafunire. 25Iwo analanda mizinda yotetezedwa ndi dziko lachonde. Anatenganso nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino, zitsime zokumbidwa kale, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndi mitengo yambiri ya zipatso. Ndipo anadya nakhuta ndipo anali athanzi. Choncho ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu wopambana.

26“Komabe iwo anakhala osamvera ndipo anakuwukirani nafulatira malamulo anu. Anapha aneneri anu, amene anakawadandaulira kuti abwerere kwa Inu. Anachita chipongwe choopsa. 27Pamene anazunzidwa anafuwulira kwa Inu, ndipo Inu munawamvera muli kumwambako. Ndipo mwa chifundo chanu chachikulu munkawapatsa atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo.”

28“Koma akangokhala pa mtendere ankayambanso kuchita zoyipa pamaso panu. Choncho munkawapereka mʼmanja mwa adani awo amene ankawalamulira. Komabe pamene ankabwerera ndi kumalira kwa Inu, Inu munkawamva muli kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chochuluka, nthawi zonse munkawapulumutsa.

29“Inu munkawachenjeza kuti abwerere ndi kuyamba kutsata malamulo anu. Koma iwo ankadzitukumula ndipo sankamvera malamulo anu. Iwo anachimwira malangizo anu amene munati ‘Amapatsa moyo kwa munthu wowamvera.’ Iwo ankakufulatirani, nawumitsa makosi awo osafuna kukumverani. 30Munapirira nawo kwa zaka zambiri. Munkawachenjeza ndi Mzimu wanu kudzera mwa aneneri anu, koma iwo sankakumverani. Choncho munawapereka mʼmanja mwa anthu a mayiko ena. 31Komabe mwachifundo chanu chachikulu simuwatheretu kapena kuwataya pakuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo.

32“Nʼchifukwa chake, tsono, Inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa kwambiri mumasunga pangano ndi chikondi chosasinthika. Musalole kuti mavuto onse amene atigwera ife, mafumu athu, atsogoleri athu, ansembe athu, aneneri athu, makolo athu ndi anthu ena onse kuyambira nthawi ya mafumu a ku Asiriya mpaka lero aoneke ochepa pamaso panu. 33Koma Inu mwakhala wolungama pa zonse zimene zakhala zikutichitikira. Mwachita zokhulupirika, koma ife tachita zolakwa. 34Ndipotu mafumu athu, atsogoleri athu, ansembe athu ndi makolo athu sanatsatire mawu anu. Iwo sanalabadire za malamulo anu ngakhale mawu anu owachenjeza amene munawapatsa. 35Ngakhale ankadzilamulira okha, nʼkumalandira zabwino zochuluka mʼdziko lalikulu ndi lachonde limene munawapatsa, koma iwo sanakutumikireni kapena kusiya ntchito zawo zoyipa.

36“Tsono, taonani! Ife lero ndife akapolo, ndife akapolo mʼdziko limene munapereka kwa makolo athu kuti azidya zipatso zake ndi zabwino zake zonse. 37Tsono chifukwa cha machimo athu, mafumu amene munawayika kuti azitilamulira angodzilemeretsa ndi chuma chambiri cha dzikoli. Iwo ali ndi mphamvu zolamulira matupi athu ndi ngʼombe zathu momwe afunira. Zedi, ife tili mʼmavuto aakulu.”

Mgwirizano wa Anthu

38“Chifukwa cha zonsezi, ife tikuchita mgwirizano wokhazikika, pochita kulemba, ndipo atsogoleri athu, Alevi athu ndi ansembe athu asindikiza chidindo chawo pa mgwirizanowo.”