士師記 7 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

士師記 7:1-25

基甸打敗米甸人

1耶路·巴力,也就是基甸,清早起來,率領眾人在哈律泉旁紮營,米甸人的軍營在他們北邊靠近摩利山的谷中。

2耶和華對基甸說:「你的人太多了,我不能把米甸人交在你們手中,免得以色列人以為是靠自己的力量救了自己。 3你要向他們宣佈,膽小害怕的人可以離開基列山回家。」結果兩萬二千人離去,只剩下一萬人。

4但耶和華對基甸說:「人還是太多,你帶他們到下面的泉水邊,我會在那裡為你挑選人員。」 5於是,基甸把他們帶到泉水邊,耶和華對他說:「把像狗一樣用舌頭舔水喝的和跪著喝水的分開。」 6那時有三百人捧水舔著喝,其餘的都跪著喝。 7耶和華對基甸說:「我要用這三百舔水喝的人拯救你們,我要把米甸人交在你手中。讓其餘的人都回家吧。」 8於是,基甸留下這三百人,把其餘人的食物和號角收集起來,讓他們回家。米甸人的軍營就在他們下面的山谷裡。

9當天晚上,耶和華吩咐基甸說:「起來,下去攻打敵營吧!我已把敵人交在你手中了。 10如果你害怕,可以和你的僕人普拉一起下到敵營, 11聽聽他們說什麼,你就有膽量攻打敵營了。」於是,基甸就帶著僕人普拉下到敵營旁。 12米甸人、亞瑪力人及東方人像蝗蟲一樣佈滿山谷,他們的駱駝如海邊的沙一樣不計其數。 13基甸到了那裡,聽見一個人對同伴說:「我做了個夢,夢見一個大麥餅滾進我們的營中,把一個帳篷撞翻在地。」 14他的同伴說:「那不是別的,正是以色列約阿施的兒子基甸的刀,上帝把米甸人和整個軍營都交在他手中了。」

15基甸聽了這夢和夢的解釋,就俯伏敬拜上帝。他回到以色列人的營中,大聲喊道:「起來吧,耶和華已經把米甸軍營交在你們手中了。」 16基甸把三百人分成三隊,分給他們號角和藏有火把的瓦瓶, 17對他們說:「你們要看我的行動,當我們走到敵營旁邊時,我怎麼做,你們也要怎麼做。 18我們這隊吹響號角時,你們也要在敵營四周吹響號角,高喊,『為了耶和華!為了基甸!』」

19午夜初,守衛剛換班,基甸帶著一百人來到米甸營旁。他們吹響號角,打破手中的瓦瓶。 20其餘的二百人也吹響號角,打破瓦瓶。他們左手舉著火把,右手拿著號角,高喊:「為耶和華和基甸而戰!」 21他們在敵營周圍各守其位,米甸全軍邊喊邊逃。 22基甸的三百人一起吹響號角時,耶和華使米甸人自相殘殺。他們逃往西利拉伯·哈示他,一直逃到靠近他巴亞伯·米何拉的邊境。

23基甸號召拿弗他利亞設瑪拿西以色列人追殺米甸敗軍, 24又派人到整個以法蓮山區,吩咐當地人攻打米甸人,佔據遠至伯·巴拉一帶的約旦河渡口。以法蓮人都依言而行, 25還生擒了米甸人的兩名首領俄立西伊伯。他們在俄立磐石上殺死了俄立,在西伊伯榨酒池殺了西伊伯。他們繼續追殺米甸人,並帶著俄立西伊伯的人頭穿過約旦河,交給基甸

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 7:1-25

Gideoni Agonjetsa Amidiyani

1Yeru-Baala (Gideoni) ndi anthu ake onse anadzuka mʼmamawa nakamanga misasa pambali pa kasupe ku Harodi. Misasa ya Amidiyani inali mʼchigwa kumpoto kwa phiri la More. 2Yehova anati kwa Gideoni, “Anthu uli nawowa andichulukira kwambiri kuti ndigonjetse Amidiyani chifukwa Aisraeli angamadzitukumule pamaso panga ndi kumanena kuti, ‘Tadzipulumutsa ndi mphamvu zathu.’ 3Tsono lengeza kwa anthu kuti, ‘Aliyense amene akuchita mantha ndi kunjenjemera abwerere kwawo, ndipo achoke kuno ku phiri la Giliyadi.’ ” Choncho anthu 22,000 anachoka, ndipo anatsalira anthu 10,000.

4Koma Yehova anawuza Gideoni kuti, “Anthuwa achulukabe. Uwatenge upite nawo ku mtsinje ndipo ndikawayesa kumeneko mʼmalo mwako. Ndikadzanena kuti, ‘Uyu apite nawe’ adzapita nawe; koma ndikanena kuti ‘Uyu asapite nawe,’ sadzapita nawe.”

5Choncho Gideoni anatenga anthuwo ndi kupita nawo ku madzi. Kumeneko Yehova anamuwuza kuti, “Amene amwe madzi mokhathira ndi manja ngati galu uwayike pawokha, ndipo amene amwe atagwada pansi uwayikenso pawokha.” 6Ndipo anthu 300 anamwa mokhathira, pamene ena onse anagwada pansi pakumwa.

7Yehova anati kwa Gideoni, “Ndi anthu 300 amene anamwa madzi mokhathira ndi manja awo ndidzakupulumutsani ndipo ndidzapereka Amidiyani mʼmanja mwanu. Koma anthu ena onse apite ku nyumba kwawo.” 8Choncho analola anthu ena onse kuti apite ku nyumba zawo kupatula anthu 300 osankhika aja. Iwowa anatenga zakudya ndi malipenga a anthuwo.

Ndipo misasa ya ankhondo Amidiyani inali kumunsi kwa chigwa. 9Usiku umenewo Yehova anati kwa Gideoni, “Dzuka, pita kachite nkhondo ku misasayo, chifukwa ndayipereka mʼmanja mwako. 10Ngati ukuopa, upite ku msasako ndi Pura wantchito wako, 11ndipo ukamvere zimene akunena ndipo pambuyo pake udzalimba mtima ndi kupita kukayithira nkhondo misasayo.” Choncho iye ndi wantchito wake Pura anapita kumbali ina ya msasawo kumene kunali ankhondo. 12Amidiyani, Aamaleki ndi anthu ena onse akummawa anadzaza chigwa chonse ngati dzombe. Ngamira zawo zinali zambiri zosawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.

13Gideoni atafika anangomva munthu wina akuwuza mnzake maloto ake kuti, “Ine ndinalota nditaona dengu la buledi wa barele likugubuduzika kupita ku misasa ya Amidiyani. Litafika linawomba tenti moti inagwa ndi kuphwasukaphwasuka.”

14Ndipo mnzakeyo anamuyankha kuti, “Iyi ndi nkhondo ya Gideoni mwana wa Yowasi, wa ku Israeli. Mulungu wapereka Amidiyani pamodzi ndi ankhondo ake onse mʼdzanja mwake.”

15Gideoni atamva za malotowo ndi kumasulira kwake, anapembedza Mulungu. Kenaka anabwerera ku msasa wa Israeli nawawuza kuti, “Dzukani popeza Yehova wapereka msasa wa Midiyani mʼmanja mwanu.” 16Anawagawa anthu 300 aja magulu atatu, nawapatsa malipenga mʼmanja mwawo ndi mbiya zimene mʼkati mwake munali nsakali zoyaka.

17Anawuza anthuwo kuti, “Muzikayangʼana ine ndi kuchita zimene ndizikachita. Ndikakafika kumalire a msasa, mukachite zomwe ndikachita ine. 18Ndikadzaliza lipenga ndi onse amene ali ndi ine, inunso mukalize malipenga kumbali zonse za misasa yonse ndi kufuwula kuti, ‘Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.’ ”

19Choncho Gideoni pamodzi ndi amuna 100 omwe anali nawo anafika ku malire a msasa pakati pa usiku, alonda atangosinthana kumene. Iwo analiza malipenga awo ndi kuphwanya mbiya zimene zinali mʼmanja mwawo. 20Magulu awiri ena aja anayimbanso malipenga ndi kuswa mbiya zawo. Aliyense ananyamula nsakali ya moto ku dzanja lamanzere ndi lipenga ku dzanja lamanja ndipo anafuwula kuti, “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.” 21Aliyense anayima pa malo pake kuzungulira misasa. Ankhondo a mʼmisasa muja anadzuka nayamba kuthawa akufuwula.

22Anthu 300 aja ataliza malipenga, Yehova anawasokoneza ankhondo a Midiyani aja motero kuti ankamenyana okhaokha. Ankhondowo anathawira ku Beti-Sita cha ku Zerera mpaka ku malire a Abeli-Mehola pafupi ndi Tabati. 23Aisraeli a fuko la Nafutali, fuko la Aseri, ndi fuko lonse la Manase anayitanidwa, ndipo iwo anathamangitsa Amidiyaniwo. 24Gideoni anatumiza amithenga ku dziko lonse la ku mapiri la Efereimu kukanena kuti, “Tsikani mumenyane ndi Amidiyani ndipo mulande madooko awo owolokera mpaka ku Beti-Bara.”

Choncho anthu onse a fuko la Efereimu anasonkhana ndipo analanda madooko awo owolokera mpaka ku Betibaala. 25Iwo anagwiranso atsogoleri awiri a nkhondo a Amidiyani, Orebu ndi Zeebu. Anapha Orebu ku thanthwe la Orebu, koma Zeebu anamuphera ku malo ofinyira mphesa ku Zeebu pothamangitsa Amidiyani. Mitu ya Orebu ndi Zeebu anabwera nayo kwa Gideoni kutsidya kwa Yorodani.