士師記 21 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

士師記 21:1-25

為便雅憫支派娶妻

1以色列人曾在米斯巴起誓不把女兒嫁給便雅憫人。 2他們來到伯特利,坐在上帝面前放聲痛哭,直到黃昏。 3他們說:「以色列的上帝耶和華啊,以色列為何少了一個支派呢?為何發生了這樣的事呢?」 4第二天,眾人清早起來在那裡築了一座祭壇,獻上燔祭和平安祭。 5他們彼此議論說:「我們到米斯巴聚集在耶和華面前的時候,各支派中誰沒有來呢?」原來,他們曾經起誓說:凡不到米斯巴聚集在耶和華面前的人都要被處死。 6以色列人為他們的同胞便雅憫人難過,說:「如今以色列絕了一個支派。 7我們曾經在耶和華面前起誓,決不把女兒嫁給便雅憫人,現在我們應該怎麼辦才能使他們剩下來的人得到妻子呢?」

8他們又查問各支派中誰沒有到米斯巴聚集在耶和華面前,結果發現基列·雅比人缺席, 9因為點兵的時候,沒有一個基列·雅比人在場。 10於是,會眾派出一萬二千精兵,命令他們殺掉基列·雅比人及其婦女和孩子。 11他們對精兵說:「你們所要做的就是消滅所有的男子和已婚婦女。」 12他們在基列·雅比的居民中找到四百名處女,把她們帶回迦南示羅營地。

13全體會眾又派人到臨門岩去跟便雅憫人講和。 14於是,便雅憫人返回了家鄉,以色列人把從基列·雅比居民中留下來的四百個處女給他們做妻子,但還是不夠。 15眾人為便雅憫支派難過,因為耶和華使以色列少了一個支派。

16會眾的長老說:「便雅憫支派的女子都死了,我們應該怎麼辦才能使餘下的人有妻子呢? 17便雅憫的餘民必須成家立後,以免以色列失去一個支派。 18可是我們又不能把女兒嫁給他們,因為我們曾經起誓,『把女兒嫁給便雅憫人的必受咒詛。』」 19有人想起在示羅每年都有耶和華的節期。示羅利波拿以南、伯特利以北至示劍的大路東面。 20於是,他們對便雅憫人說:「你們埋伏在葡萄園裡, 21見到示羅的女子出來跳舞時,就衝出去各自搶一個,帶回便雅憫做妻子。 22倘若她們的父親或弟兄前來抱怨,我們會說,『求你們恩待我們,因為我們從戰場上帶回的女子不夠分給他們做妻子。何況又不是你們把女兒嫁給他們的,所以罪不在你們。』」 23便雅憫人就依計行事,從跳舞的女子中各自搶了一個,帶回自己的家鄉做妻子。他們重建城邑,住在其中。 24於是,以色列人離開那裡,各回自己的支派、宗族和家園。

25那時候,以色列人沒有王,人人各行其是。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 21:1-25

Akazi a Abenjamini

1Aisraeli anali atalumbira ku Mizipa kuti, “Palibe mmodzi wa ife adzapereke mwana wake wamkazi kuti akwatiwe ndi mwamuna wa fuko la Benjamini.”

2Anthu anapita ku Beteli kumene anakakhala pansi pamaso pa Mulungu mpaka madzulo. Iwo anakweza mawu nalira kwambiri. 3Iwo ankanena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli, nʼchifukwa chiyani izi zachitika mʼdziko la Israeli kuti lero fuko limodzi lisowe mu Israeli?”

4Mmawa mwake anthu anadzuka namanga guwa lansembe ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano.

5Kenaka Aisraeli anafunsa kuti, “Kodi ndani pakati pa mafuko a Israeli sanafike ku msonkhano wa Yehova?” Anatero chifukwa anachita malumbiro aakulu okhudza munthu amene alephere kupita ku Mizipa ndi kuti woteroyo ayenera kuphedwa.

6Tsono Aisraeli anamva chisoni chifukwa cha abale awo, Abenjamini. Iwo anati, “Lero fuko limodzi lachotsedwa mu Israeli. 7Kodi tingawapezere bwanji anthu otsalawa akazi woti awakwatire? Paja ife tinalumbira kwa Yehova kuti sitidzapereka ana anthu aakazi kuti awakwatire. 8Kenaka anafunsa kuti, ‘Kodi mu fuko la Israeli ndani amene sanabwere pamaso pa Yehova ku Mizipa?’ ” Tsono panapezeka kuti panalibe ndi mmodzi yemwe wochokera ku Yabesi Giliyadi amene anapita ku msonkhano ku misasa kuja. 9Pamene anthu anawerengana anangoona kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi palibe.

10Choncho msonkhano unatumiza anthu ankhondo 12,000 ndi kuwalamula kuti, “Mukaphe anthu onse okhala ku Yabesi Giliyadi, kuphatikizapo akazi ndi ana.” 11Izi ndi zimene mukachite. “Mukaphe mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense amene anadziwapo mwamuna.” 12Iwo anapeza atsikana 400 pakati pa anthu okhala mu Yabesi Giliyadi amene anali asanadziwepo mwamuna ndipo anabwera nawo ku misasa ku Silo mʼdziko la Kanaani.

13Kenaka msonkhano wonse unatumiza uthenga kwa Abenjamini amene ankakhala ku thanthwe la Rimoni kuwawuza kuti nkhondo yatha. 14Choncho Abenjamini anabwera nthawi imeneyo ndipo Aisraeli anawapatsa akazi a ku Yabesi Giliyadi amene sanaphedwe. Koma sanapezeke owakwanira.

15Aisraeli anamvera chisoni Abenjamini, chifukwa Yehova anachita ngati waligwerula dzino fuko la Israeli. 16Choncho akuluakulu a msonkhano anati, “Kodi tikawapezera kuti akazi anthu otsalirawa kuti awakwatire popeza kuti akazi a fuko la Benjamini anaphedwa?” 17Iwo anati, “Abenjamini amene anapulumukawa ayenera kukhala ndi zidzukulu, kuti mtundu wa Israeli usafafanizike. 18Ife sitingathe kuwapatsa ana anthu aakazi kuti akwatire. Paja tinalumbira kuti, ‘Akhale wotembereredwa aliyense amene adzapereka mwana wake wamkazi kwa mwamuna wa fuko la Benjamini kuti akwatire.’ 19Ndipo anati, ‘Paja ku Silo kuli chikondwerero cha chaka ndi chaka cholemekeza Yehova. Tsono Silo ali kumpoto kwa Beteli, kummawa kwa msewu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu, ndiponso kummwera kwa Lebona.’ ”

20Choncho anawalamulira Abenjamini aja kuti, “Pitani mukabisale mʼminda ya mpesa 21ndipo mukakhale tcheru. Ana aakazi a ku Silo akadzatulukira kudzavina nawo magule, pomwepo inu mutuluke minda ya mpesa ndi kukawagwira aliyense wake ndi kupita nawo ku dziko la Benjamini. 22Ngati abambo awo kapena alongo awo adzabwera kudzadandaula kwa ife, tidzawawuza kuti, ‘Chonde, tikomereni mtima powalola kuti atenga ana anu aakaziwo popeza kuti ife sitinawapezere akazi pomenya nkhondo. Inunso simunachite kuwapatsa. Mukanatero ndiye mukanapalamula.’ ”

23Abenjamini anachitadi zimenezi. Mwa akazi amene ankavina aja anagwirapo ena, malingana ndi chiwerengero chawo, nawatenga kuti akhale akazi awo. Kenaka ananyamuka kubwerera ku dziko la kwawo, nakamanganso mizinda yawo ndi kumakhalamo.

24Pambuyo pake Aisraeli anachoka kumeneko ndi kubwerera kwawo, ku mafuko ndi ku mabanja awo, aliyense ku dera la cholowa chake.

25Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israeli. Aliyense ankangochita zimene zomukomera yekha.