士師記 15 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

士師記 15:1-20

參孫向非利士人報仇

1過了些日子,在割麥的時候,參孫帶著一隻山羊羔去探望他妻子。他說:「我要進內室見我妻子。」他岳父卻不讓他進去, 2並對他說:「我以為你非常恨她,所以我把她改嫁給你的伴郎了。她妹子不是比她更美麗嗎?你可以娶來代替她。」

3參孫說:「這次我要加害非利士人,可不能怪我了。」

4於是,他出去捉了三百隻狐狸,把牠們的尾巴一對一對綁起來,將火把綁在兩條尾巴中間, 5然後點燃火把,把狐狸放進非利士人的麥田裡,將割好的麥捆和未割的麥子、葡萄園和橄欖園都燒毀了。 6非利士人問:「這是誰幹的?」有人回答說:「是亭拿人的女婿參孫幹的,因為他岳父把他的妻子嫁給了他的伴郎。」非利士人就去放火燒死了參孫的妻子和岳父。 7參孫說:「你們既然這樣做,我不向你們報仇誓不甘休。」 8參孫大肆擊殺他們,殺死了很多人。事後,他下到以坦,住在那裡的岩洞裡。

9非利士人進犯猶大,在利希一帶紮營。 10猶大人問他們:「你們為什麼來攻打我們?」非利士人回答說:「我們來捉拿參孫,向他以報還報。」 11於是,有三千猶大人去以坦的岩洞找參孫,對他說:「難道你不知道非利士人是我們的統治者嗎?你為什麼連累我們?」參孫回答說:「我只是以牙還牙。」 12猶大人說:「我們來是要捉拿你,把你交給非利士人。」參孫說:「你們要保證你們不會親手殺我。」 13他們說:「我們不會殺你,只將你綁起來交給非利士人。」於是,他們用兩根新繩子把參孫捆綁起來帶出岩洞。

14非利士人看見參孫來到利希,就呐喊著迎了上去。耶和華的靈降在參孫身上,綁在他手臂上的繩子就像被火燒的麻線一樣脫落下來。 15他看到一塊還沒有乾的驢腮骨,就撿起來用它殺了一千個非利士人。 16參孫說:

「用這驢腮骨,我殺人成堆;

用這驢腮骨,我殺戮千人。」

17說完,他扔掉了手中的驢腮骨。因此,那地方叫拉末·利希15·17 拉末·利希」意思是「腮骨崗」。

18參孫覺得非常口渴,便向耶和華呼求說:「你既然藉著僕人的手大敗敵人,難道你會讓我渴死、落在這些未受割禮的人手中嗎?」 19於是,上帝使利希的一處窪地裂開,湧出水來。參孫喝後恢復了精神。因此,那水泉叫隱哈·歌利15·19 隱哈·歌利」意思是「呼求者的泉」。。那水泉今天還在利希20非利士人統治期間,參孫以色列的士師二十年。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 15:1-20

Samsoni Abwezera Afilisti

1Patapita nthawi, mu nyengo yodula tirigu, Samsoni anatenga kamwana kambuzi ndipo anapita kukacheza kwa mkazi wake. Iye anati, “Ndikufuna kukalowa ku chipinda cha mkazi wanga.” Koma abambo a mkaziyo anamuletsa kutero.

2Abambo a mkaziyo anati, “Ine ndimaganiza kuti umamuda kwambiri nʼchifukwa chake ndinamupereka kwa mnzako. Kodi mngʼono wake uja sindiye wokongola kupambana iye? Ingotengani ameneyo mʼmalo mwake.”

3Samsoni anawawuza kuti, “Pano sindikhala wochimwa ndikawachita choyipa chachikulu Afilistiwa.” 4Choncho Samsoni anapita nakagwira nkhandwe 300 nazimangirira michira ziwiriziwiri ndipo pa fundo iliyonse ya michirayo anamangirira nsakali. 5Anayatsa nsakalizo kenaka ndi kuzitayira nkhandwe zija mʼminda ya tirigu ya Afilisti, ndipo zinatentha milu ya tirigu, ndi wosadula yemwe pamodzi ndi mitengo ya mpesa ndi ya olivi.

6Tsono Afilisti anayamba kufunsana kuti, “Ndani wachita izi?” Ena anati, “Ndi Samsoni mkamwini wa munthu wa ku Timna uja chifukwa Mtimunayo anatenga mkazi wake ndi kumupereka kwa mnzake.”

Choncho Afilisti anapita kukatentha mtsikanayo pamodzi ndi abambo ake. 7Samsoni anawawuza kuti, “Ngati mumachita zangati zimenezi, ndiye ine sindileka mpaka nditakulipsirani.” 8Choncho Samsoni anamenyana nawo koopsa ndipo anapha ambiri a iwo. Kenaka anakalowa mʼphanga la Etamu, nakhala momwemo.

9Pambuyo pake Afilisti anakamanga misasa ya nkhondo mʼdziko la Yuda, ndi kuthira nkhondo mʼdera la Lehi. 10Anthu a fuko la Yuda anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kudzamenyana nafe?”

Iwo anayankha kuti, “Tabwera kudzamanga Samsoni ndi kuti timuchite zofanana ndi zimene anatichita.”

11Ndipo anthu 3,000 a ku Yuda anapita ku phanga la Etamu, ndi kukamufunsa Samsoni kuti, “Kodi iwe sudziwa kuti ife amatilamulira ndi Afilisti? Tsono ndi chiyani chimene watichitachi?”

Iye anayankha kuti, “Ine ndinachita zomwe iwo anandichita.”

12Iwo anati kwa iye, “Ife tabwera kuti tikumange ndi kukupereka kwa Afilisti.”

Ndipo Samsoni anati, “Lonjezani mwa lumbiro kuti simundipha ndinu.”

13Iwo anamuyankha kuti, “Ayi, ife sitikupha. Koma tingokumanga ndi kukupereka mʼmanja mwa Afilisti.” Choncho anamumanga ndi zingwe ziwiri zatsopano namutulutsa mʼphanga muja. 14Samsoni anafika ku Lehi, ndipo Afilisti anamuchingamira akufuwula. Nthawi yomweyo Mzimu wa Yehova unatsika pa iye mwamphamvu ndipo zingwe zimene anamumanga nazo zinasanduka ngati thonje lopsa mʼmoto, zinachita ngati zasungunuka nʼkuchoka mʼmanja mwake. 15Anapeza chibwano cha bulu amene anali atangofa kumene. Anachitola ndi kuphera nacho anthu 1,000.

16Ndipo Samsoni anati,

“Ndi chibwano cha bulu,

milu ndi milu ya anthu.

Ndi chibwano cha bulu,

ndapha anthu 1,000.”

17Atatsiriza kuyankhula, anataya chibwanocho, ndipo malowo anawatcha Ramati-Lehi.

18Pambuyo pake anamva ludzu kwambiri ndipo anayitana Yehova mopempha kuti, “Inu mwapatsa mtumiki wanu chipulumutso chachikulu chotere. Kodi tsopano ndife ndi ludzu ndi kugwidwa ndi anthu osachita mdulidwewa?” 19Pamenepo Mulungu anangʼamba nthaka ku Lehi, ndipo madzi anatuluka mʼdzenjemo. Samsoni anamwa madziwo, ndipo mphamvu zake zinabwerera nakhalanso monga analili. Choncho chitsimecho chinatchedwa Eni-Hakore, ndipo chilipobe ku Lehiko mpaka lero.

20Samsoni anatsogolera Israeli pa nthawi ya Afilisti kwa zaka makumi awiri.