啟示錄 19 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

啟示錄 19:1-21

天上的讚美

1這事以後,我聽見天上好像有一大群人在呼喊:「哈利路亞19·1 哈利路亞」意思是「要讚美上帝」。!救贖、榮耀和權能都歸於我們的上帝! 2因為祂的審判真實公義,祂懲罰了那用淫亂敗壞世界的大淫婦,為那些被她殺害的奴僕伸冤。」 3他們又歡呼說:「哈利路亞!焚燒大淫婦的煙不斷上騰,直到永永遠遠。」 4那二十四位長老和四個活物也俯伏敬拜坐在寶座上的上帝,說:「阿們!哈利路亞!」

5這時從寶座那裡發出聲音,說:「上帝所有的奴僕和一切敬畏祂的人,無論尊卑老少,都要讚美我們的上帝!」 6我聽見有聲音好像一大群人的呼喊聲,又像洪濤,也像雷鳴,說:「哈利路亞!因為我們的主——全能的上帝已經執掌王權了。 7我們應當歡喜快樂,歸榮耀給祂,因為羔羊的婚期到了,祂的新娘已預備妥當, 8獲准穿上光亮潔白的細麻衣。」這細麻衣代表聖徒的義行。

9天使吩咐我說:「你要寫下來,被邀請參加羔羊婚宴的人有福了!」他又說:「這是上帝親口說的,千真萬確。」 10我俯伏在他腳前要拜他,他卻說:「千萬不可!我和你並那些為耶穌做見證的弟兄姊妹同是上帝的奴僕。你要敬拜上帝,因為預言的真諦就是為耶穌做見證。」

白馬騎士

11我看見天開了,有一匹白馬出來,馬上的騎士名叫「誠信真實」,祂憑公義審判、作戰。 12祂的雙目如火焰,頭上戴了許多冠冕,寫著一個只有祂自己才明白的名字。 13祂穿著被鮮血浸透的衣服,祂的名字是「上帝的道」。 14眾天軍穿著潔白的細麻衣,騎著白馬跟隨祂。 15祂口中吐出一把利劍,可以攻擊列國。祂必用鐵杖統治他們,踩踏盛滿全能上帝之烈怒的榨酒池。 16祂的衣服和大腿上都寫著祂的名號:「萬王之王,萬主之主。」

17我又看見一位天使站在太陽裡,對空中飛翔的鳥大聲呼喚: 18「來吧!一起來參加上帝的盛宴,一同享用君王、將軍、勇士、馬匹、騎士、自由人、奴隸和尊卑老少的肉吧!」

19我看見那怪獸、地上的眾王及其軍隊聚集起來,要與白馬騎士和祂的軍隊作戰。 20後來,怪獸被俘虜了,在怪獸面前行奇蹟的假先知也一同被擒了。這假先知曾用奇蹟欺騙那些蓋了獸印、敬拜獸像的人。他和怪獸一同被活活地扔進硫磺火湖裡。 21怪獸的殘兵紛紛被白馬騎士口中的利劍所殺,飛鳥飽餐了他們的肉。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 19:1-21

Babuloni Wagwa, Haleluya!

1Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti,

“Haleluya!

Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,

2pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo.

Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja

amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake.

Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.”

3Ndipo anafuwulanso kuti,

“Haleluya!

Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”

4Akuluakulu 24 aja ndi zamoyo zinayi zija anadzigwetsa pansi kupembedza Mulungu amene anakhala pa mpando waufumu. Ndipo anafuwula kuti,

“Ameni, Haleluya!”

5Kenaka mawu anachoka ku mpando waufumu kuti,

“Lemekezani Mulungu wathu

inu nonse atumiki ake,

inu amene mumamuopa,

nonse angʼono ndi akulu!”

6Kenaka ndinamva chimene chinamveka ngati gulu lalikulu, ngati mkokomo wamadzi othamanga ndipo ngati kugunda kwakukulu kwa bingu, ndipo anati,

“Haleluya!

Pakuti Ambuye Mulungu wathu Wamphamvuzonse akulamulira.

7Tiyeni tisangalale ndi kukondwera

ndi kumutamanda!

Pakuti nthawi ya ukwati wa Mwana Wankhosa yafika,

ndipo Mkwatibwi wakonzekeratu.

8Wapatsidwa nsalu yoyera kwambiri, yowala ndi yosada

kuti avale.”

(Nsalu yoyera kwambiri ikuyimira ntchito zolungama za oyera mtima).

9Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.”

10Pamenepo ndinadzigwetsa pa mapazi ake kumupembedza. Koma anandiwuza kuti, “Usatero ayi, ine ndine mtumiki mnzako ngati iwe yemwe, ndiponso ngati abale ako amene asunga umboni wa Yesu. Pembedza Mulungu. Pakuti umboni wa Yesu ndiye mzimu wa uneneri.”

Wokwera pa Kavalo Woyera

11Ndinaona kumwamba kutatsekuka ndipo patsogolo panga panali kavalo woyera, amene anakwerapo dzina lake linali Wokhulupirika ndiponso Woona. Poweruza ndi kuchita nkhondo, amachita molungama. 12Maso ake anali ngati malawi amoto, ndipo pamutu pake panali zipewa zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lodziwika ndi Iye yekha, osati wina aliyense. 13Iye anavala mkanjo woviyika mʼmagazi, ndipo dzina lake ndi Mawu a Mulungu. 14Magulu ankhondo akumwamba ankamutsatira atakwera pa akavalo oyera, ndipo iwowo atavala nsalu zoyera kwambiri ndi zosada. 15Mʼkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa limene anati akaphe nalo mitundu ya anthu. Iye adzalamulira ndi ndodo yachitsulo. Iye anaponda choponderamo mphesa cha ukali wa Mulungu Wamphamvuzonse. 16Pa chovala ndi pa ntchafu pake panalembedwa dzina ili:

MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE.

17Ndipo ndinaona mngelo atayimirira pa dzuwa amene anafuwula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zowuluka mlengalenga kuti, “Bwerani, sonkhanani pamodzi ku phwando lalikulu la Mulungu. 18Kuti mudye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, ndi wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi okwerapo awo, ndi wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, angʼono ndi aakulu.”

19Kenaka ndinaona chirombo chija ndi mafumu a dziko lapansi ndi magulu ankhondo atasonkhana pamodzi kuti achite nkhondo ndi wokwera pa kavalo ndi ankhondo ake. 20Koma chirombocho chinagwidwa pamodzi ndi mneneri wonyenga uja amene anachita zizindikiro zodabwitsa pamaso pake. Ndi zizindikirozi anasocheretsa amene analembedwa chizindikiro cha chirombocho napembedza fano lake. Onse awiri anaponyedwa amoyo mʼnyanja yamoto yasulufule wotentha. 21Ena onse anaphedwa ndi lupanga lija linatuluka mʼkamwa mwa wokwera pa kavalo uja, ndipo mbalame zonse zinadya mokwanira mnofu wa anthu akufawo.