列王紀下 9 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

列王紀下 9:1-37

耶戶被立為以色列王

1以利沙先知叫來一個先知,吩咐他:「你要束上腰帶,拿著這瓶膏油去基列拉末2到了以後,你去找寧示的孫子、約沙法的兒子耶戶,帶他離開同僚,進入密室, 3把這瓶膏油倒在他頭上,告訴他,『耶和華說,我膏立你為以色列王。』然後,你要馬上開門逃走,不可遲延。」

4於是,那位年輕的先知啟程前往基列拉末5到了那裡,他看見眾將領正坐在一起,便說:「將軍,我有話對你說。」耶戶說:「你想對我們哪一個說話?」他說:「將軍啊,我有話對你說。」 6耶戶便站起來,隨他進入屋裡。他將膏油倒在耶戶頭上,說:「以色列的上帝耶和華說,『我膏立你做我以色列子民的王。 7你要殺你主人亞哈的全家,這樣我就可以為我的僕人——眾先知以及其他僕人報仇,他們被耶洗別殺害。 8亞哈全家必滅亡,我要從以色列剷除他家中所有的男子——不論奴隸還是自由人, 9使他家像尼八的兒子耶羅波安家和亞希雅的兒子巴沙家一樣。 10耶洗別的屍體必在耶斯列的田間被狗吃,無人埋葬。』」說完這話,那位年輕的先知便開門逃跑了。

11耶戶出來回到同僚那裡,一個人問他:「沒事吧?那瘋子為什麼來找你?」耶戶答道:「你們認得他,也知道他會說什麼。」 12他們說:「我們不知道,你告訴我們吧!」耶戶說:「他告訴我,耶和華說膏立我做以色列王。」 13他們連忙將自己的衣服鋪在耶戶腳下的臺階上,吹響號角,高喊:「耶戶做王了!」

以色列王約蘭被殺

14寧示的孫子、約沙法的兒子耶戶背叛了約蘭。當時,約蘭率領全體以色列人在基列拉末防禦亞蘭哈薛15他與哈薛交戰受傷後,回到耶斯列養傷。耶戶對屬下說:「如果你們要我做王,就不要讓任何人逃出城去耶斯列報信。」 16於是,耶戶駕車去了耶斯列,因為約蘭耶斯列養傷,猶大亞哈謝也在那裡探望他。

17耶斯列城樓上的哨兵看見耶戶的人馬朝耶斯列奔來,就報信說:「我見到一隊人馬!」約蘭下令:「派一個騎兵去看看他們是否為平安而來。」 18騎兵出去迎接耶戶,對他說:「王問你是否為平安而來。」耶戶說:「這與你何干?你跟在我後面。」哨兵稟告說:「騎兵到了那裡,卻沒有回來。」 19王又派一個騎兵到耶戶那裡,對他說:「王問你是否為平安而來。」耶戶說:「這與你何干?你跟在我後面。」 20哨兵又稟告說:「他到了那裡,也沒有回來。那人駕車很猛,一定是寧示的孫子耶戶。」

21約蘭下令備車。以色列約蘭猶大亞哈謝各乘自己的戰車去見耶戶。他們和耶戶耶斯列拿伯的田裡相遇。 22約蘭問他:「耶戶,你為平安而來嗎?」耶戶答道:「國中到處都是你母親耶洗別的偶像和邪術,怎能平安呢?」 23約蘭調轉車頭逃跑,向亞哈謝大喊:「亞哈謝,他反了!」 24耶戶張弓搭箭,射中約蘭的後背,箭穿透他的心臟,他倒斃在車上。 25耶戶對將領畢甲說:「你去把他丟在耶斯列拿伯的田裡。還記得嗎?你我一起駕車跟隨他父親亞哈的時候,耶和華曾預言亞哈的事說, 26『我昨天看見拿伯和他兒子們被殺,我必使你在這塊田裡受到報應,這是耶和華說的。』現在你照耶和華的話,把他丟在這塊田裡吧。」

27猶大亞哈謝見狀,就沿著通往伯哈干的道路逃跑。耶戶在後面追,並大喊:「射死他!」他們在以伯蓮附近的姑珥坡射傷了亞哈謝。他逃到米吉多後,傷重身亡。 28他的臣僕用車把他的屍體運回耶路撒冷,安葬在大衛城他的祖墳裡。

29以色列亞哈的兒子約蘭執政第十一年,亞哈謝登基做猶大王。

耶洗別被殺

30耶戶去了耶斯列耶洗別聞訊,便梳頭描眉,向窗外眺望。 31耶戶進城時,耶洗別高聲喊道:「謀殺主人的心利啊,平安嗎?」 32耶戶抬頭望著窗口,喊道:「誰擁護我?誰?」有兩三個太監從窗口往外看他。 33耶戶說:「把她扔下來!」那幾個太監便把耶洗別扔下去,血濺在牆壁上和馬匹身上。耶戶駕車軋過她的身體, 34進入王宮,大吃大喝,然後吩咐部下說:「把那受咒詛的婦人埋了,她畢竟是王的女兒。」 35他們出去埋葬她,卻只找到她的頭骨、手掌和腳, 36便回去稟告耶戶耶戶說:「這正應驗耶和華藉祂僕人提斯比以利亞說的話,『狗必在耶斯列的田間吃耶洗別的肉, 37耶洗別的屍體必像耶斯列田間的糞便,無人能認出那是耶洗別。』」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 9:1-37

Yehu Adzozedwa Ufumu wa ku Israeli

1Mneneri Elisa anayitanitsa mmodzi mwa ana a aneneri, namuwuza kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga botolo la mafuta mʼdzanja lako ndipo upite ku Ramoti Giliyadi. 2Ukakafika kumeneko, ukafunefune Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi. Ukapite kwa iye, ukamuchotse pakati pa anzake ndi kukamulowetsa mʼchipinda chamʼkati. 3Ndipo ukatenge botololi ndi kuthira mafuta pa mutu wake ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ Kenaka ukatsekule chitseko ndi kuthawa ndipo usakachedwe!”

4Choncho mneneri wachinyamatayo anapita ku Ramoti Giliyadi. 5Atafika ku Giliyadiko anapeza atsogoleri a ankhondo ali pa msonkhano. Iye anati, “Mtsogoleri, ine ndili ndi uthenga wanu.”

Ndipo Yehu anafunsa kuti, “Uthengawo ndi wa yani pakati pathu?”

Mneneriyo anayankha kuti, “Ndi wa inuyo, mtsogoleri.”

6Yehu anayimirira nakalowa mʼnyumba. Pamenepo mneneriyo anakhuthulira mafuta pamutu pa Yehu ndipo ananena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndikukudzoza kukhala mfumu ya Israeli, anthu a Yehova. 7Uyenera kuwononga nyumba ya mbuye wako Ahabu ndipo ndidzabwezera imfa ya atumiki anga, aneneri ndiponso imfa ya atumiki ena onse a Yehova amene anaphedwa ndi Yezebeli. 8Banja lonse la Ahabu lidzatheratu. Ndidzachotsa munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu kaya ndi kapolo kapena mfulu. 9Ndidzachititsa kuti banja la Ahabu lifanane ndi banja la Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. 10Kunena za Yezebeli, agalu adzamudya ku dera la Yezireeli ndipo palibe amene adzamuyike mʼmanda.’ ” Kenaka mneneriyo anatsekula chitseko nʼkuthawa.

11Yehu atatuluka kupita kumene kunali atsogoleri anzake, mmodzi mwa iwo anamufunsa kuti, “Kodi zonse zili bwino? Kodi munthu wamisala uja anabwera kudzatani kwa iwe?”

Yehu anayankha kuti, “Iwe ukumudziwa munthu uja ndiponso ukudziwa zomwe amayankhula.”

12Atsogoleri aja anati, “Ukunama! Tiwuze.”

Yehu anati, “Zimene wandiwuza ndi izi: ‘Yehova akuti: Ine ndakudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ ”

13Atsogoleri aja mofulumira anatenga zofunda zawo naziyala pansi pa makwerero kuti Yehu akhalepo. Kenaka analiza lipenga, nafuwula kuti, “Yehu ndiye mfumu!”

Yehu Apha Yoramu ndi Ahaziya

14Choncho Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi, anachitira chiwembu Yoramu. (Nthawi imeneyi nʼkuti Yoramu ndi Aisraeli onse akuteteza Ramoti Giliyadi kwa Hazaeli mfumu ya ku Aramu, 15koma nʼkuti Yoramu atabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene Aaramu anamuvulaza pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya ku Aramu.) Yehu anati, “Ngati mukugwirizana nazo zimenezi, wina aliyense asatuluke mu mzinda muno kupita kukafotokoza nkhaniyi ku Yezireeli.” 16Pamenepo Yehu anakwera galeta lake, napita ku Yezireeli, chifukwa Yoramu anali akupumula kumeneko ndipo Ahaziya, mfumu ya ku Yuda, nʼkuti ali komweko kudzamuona.

17Mlonda amene ankayimirira pa nsanja yolondera mzinda wa Yezireeli ataona gulu lankhondo la Yehu likuyandikira, anafuwula kuti, “Ndikuona gulu lankhondo likubwera.”

Yoramu analamula kuti, “Peza munthu wokwera kavalo, mutume kuti akakumane nawo ndi kuwafunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”

18Choncho munthu wokwera kavalo anapita kukakumana ndi Yehu ndipo anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”

Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”

Mlonda uja anakafotokoza kwa mfumu kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwerera.”

19Choncho mfumu inatumanso munthu wina wachiwiri wokwera kavalo. Atafika kwa anthuwo iye anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”

Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”

20Mlonda uja anakanenanso kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwereranso. Kuyendako kukukhala ngati kwa Yehu mwana wa Nimisi, iye amayenda ngati munthu wamisala.”

21Yoramu analamula kuti, “Konzani galeta langa.” Ndipo atakonza galeta lake, Yoramu mfumu ya Israeli ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda anakwera nʼkutuluka mu mzindamo, aliyense atakwera galeta lake, kukakumana ndi Yehu. Iwo anakumana ndi Yehu pa munda umene unali wa Naboti, wa ku Yezireeli. 22Yoramu ataona Yehu anafunsa kuti, “Yehu, kodi wabwera mwamtendere?”

Yehu anayankha kuti, “Pangakhale bwanji mtendere pamene zopembedza mafano zonse zilipo ndiponso ufiti wa amayi ako Yezebeli uli ponseponse?”

23Yoramu anatembenuka, nathawa akufuwula kwa Ahaziya kuti, “Ahaziya, anthuwa atiwukira!”

24Pamenepo Yehu anakoka uta wake ndipo analasa Yoramu kumsana pakati pa mapewa. Muviwo unakalasa mtima wake ndipo anagwa pansi mʼgaleta lakelo. 25Yehu anawuza Bidikara, mtsogoleri wa galeta lake kuti, “Munyamule ndipo ukamuponye mʼmunda umene unali wa Naboti wa ku Yezireeli, chifukwa kumbukira mmene iwe ndi ine tinkayenda pambuyo pa Ahabu abambo ake, kuti Yehova ananeneratu za iye kuti, 26‘Zoonadi dzulo ndinaona magazi a Naboti ndi magazi a ana ake, akutero Yehova, ndipo Ine ndidzakubwezera ndithu choyipa chimenechi pa munda womwe uno, akutero Yehova.’ Tsono munyamule ndipo ukamuponye mʼmundamo, potsatira zimene Yehova ananena.”

27Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimene zinachitika, anathawira ku Beti Hagani. Yehu anamuthamangitsa, uku akufuwula kuti, “Mupheninso!” Iwo anamuvulaza ali mʼgaleta lakelo pa njira yopita ku Guri pafupi ndi Ibuleamu, koma iye anathawira ku Megido ndipo anakafera kumeneko. 28Antchito ake anamunyamulira mʼgaleta kupita naye ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. 29(Mʼchaka cha khumi ndi chimodzi cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya anakhala mfumu ya ku Yuda).

Kuphedwa kwa Yezebeli

30Kenaka Yehu anapita ku Yezireeli. Yezebeli atamva zimene zinachitika, anapaka zodzikometsera mʼmaso, naluka tsitsi lake, namasuzumira pa zenera. 31Pamene Yehu ankalowa pa chipata iye anafunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere, iwe Zimuri, munthu wopha mbuye wako?”

32Yehu anakweza maso nayangʼana pa zenera, ndipo anafuwula kuti, “Kodi ndani ali mbali yanga? Ndani?” Anthu ofulidwa awiri kapena atatu anayangʼana Yehu pansipo. 33Yehu anawawuza kuti, “Muponyeni pansi!” Motero anamuponya pansi ndipo magazi ake ena anafalikira pa khoma ndi pa akavalo pamene ankamupondaponda.

34Yehu analowa mʼnyumba yaufumu ndipo anadya ndi kumwa. Kenaka iye anati, “Kamutoleni mkazi wotembereredwayo, ndipo kamuyikeni mʼmanda, popeza ndi mwana wa mfumu.” 35Koma atapita kuti akamuyike mʼmanda, sanapeze kanthu kupatula chibade cha mutu wokha, mapazi ake ndi manja ake. 36Choncho iwo anabwerera kwa Yehu ndi kukamufotokozera kuti, “Mawu amene Yehova anayankhula kudzera mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe ndi awa: Pa munda wa ku Yezireeli agalu adzadya mtembo wa Yezebeli. 37Mtembo wa Yezebeli udzakhala ngati zinyalala pa munda wa ku Yezireeli, kotero kuti palibe amene adzathe kunena kuti, ‘Uyu ndi Yezebeli.’ ”