列王紀下 21 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

列王紀下 21:1-26

瑪拿西做猶大王

1瑪拿西十二歲登基,在耶路撒冷執政五十五年。他母親叫謝西芭2他做耶和華視為惡的事,效法耶和華在以色列人面前趕走的外族人的可憎行徑。 3他重建他父親希西迦拆毀的邱壇,效法以色列亞哈巴力築造祭壇,製造亞舍拉神像,並且祭拜和供奉天上的萬象。 4耶和華曾指著祂的殿說:「我的名必在耶路撒冷」,而他卻在耶和華的殿內建造異教的祭壇。 5他在耶和華殿的兩個院子裡建造祭拜天上萬象的祭壇; 6他燒死自己的兒子,獻作祭物;他行邪術,占卜,求問靈媒和巫師,做了許多耶和華視為惡的事,惹耶和華發怒。 7他雕刻亞舍拉神像,放在耶和華的殿中。關於這殿,耶和華曾對大衛和他兒子所羅門說:「我從以色列各支派中選擇了耶路撒冷和這殿,我的名要在這裡永遠受尊崇。 8只要以色列人謹遵我對他們的一切吩咐和我僕人摩西交給他們的律法,我就不再把他們從我賜給他們祖先的土地上趕走。」 9可是以色列人不肯聽從。瑪拿西誘使他們作惡,比耶和華在以色列人面前所毀滅的各族更嚴重。 10於是,耶和華藉著祂的僕人——眾先知宣告: 11瑪拿西王做的這些可憎之事,比以前住在這裡的亞摩利人更嚴重,使猶大人祭拜偶像,陷入罪中。 12所以,以色列的上帝耶和華要在耶路撒冷猶大降下大災難,凡聽見這事的人都必耳鳴。 13我要像懲罰撒瑪利亞亞哈家一樣懲罰耶路撒冷。我要潔淨耶路撒冷,就像人擦淨盤子後倒扣過來。 14我要撇棄我殘存的子民,把他們交給敵人,任其擄掠。 15因為從他們祖先離開埃及那天起直到今天,他們一直做我視為惡的事,惹我發怒。」 16瑪拿西不僅使猶大人犯罪,做耶和華視為惡的事,還濫殺無辜,使耶路撒冷血流遍地。 17瑪拿西其他的事及其一切所作所為都記在猶大的列王史上。 18他與祖先同眠後,葬在他王宮的花園。即烏撒花園,他兒子亞們繼位。

亞們做猶大王

19亞們二十二歲登基,在耶路撒冷執政兩年。他母親叫米舒利密,是約提巴哈魯斯的女兒。 20他效法他父親瑪拿西做耶和華視為惡的事, 21步他父親的後塵,祭拜和供奉同樣的偶像。 22他背棄他祖先的上帝耶和華,沒有遵行耶和華的教導。 23他的臣僕謀反,在王宮裡殺了他。 24民眾殺死那些背叛亞們王的人,立他兒子約西亞為王。 25亞們其他的事及其一切所作所為都記在猶大的列王史上。 26他死後,葬在烏撒花園內他的墳墓裡,他兒子約西亞繼位。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 21:1-26

Manase Mfumu ya Yuda

1Manase anakhala mfumu ali ndi zaka khumi ndi ziwiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 55. Amayi ake anali Hefiziba. 2Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, potsatira mchitidwe wonyansa wa mitundu imene Yehova anayipirikitsa pofika Aisraeli. 3Iyetu anamanganso malo opembedzera mafano amene Hezekiya abambo ake anawawononga. Anamangira Baala maguwa a nsembe ndi mtengo wa fano la Asera monga anachitira Ahabu mfumu ya Israeli ndipo ankapembedza zolengedwa zonse zamlengalenga. 4Anamanga maguwa ansembewa mʼNyumba ya Yehova, mʼmene Yehova ananena kuti, “Mu Yerusalemu ndidzayikamo Dzina langa.” 5Mʼmabwalo onse awiri a Nyumba ya Yehova, Manase anamangamo maguwa opembedzerapo zinthu zamlengalenga. 6Iye anapsereza mwana wake pa moto ngati nsembe, ankachita za matsenga, ankawombeza mawula, ankapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndiponso ankapembedza mizimu. Iyeyo anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova ndipo anakwiyitsa Yehovayo.

7Iye anatenga fano losema la Asera limene analipanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Yehova, Nyumba imene Yehova ananena kwa Davide ndi mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba iyi ndi mu Yerusalemu ndiwo malo amene ndasankha pakati pa mafuko onse a Aisraeli kuyikamo Dzina langa kwamuyaya. 8Sindidzalola kuti Aisraeli achotsedwe mʼdziko lawo limene ndinapatsa makolo awo ngati iwowo adzasamala kuchita zinthu zonse zimene ndinawalamula ndi kusunga malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anawapatsa.” 9Koma anthu sanamvere. Manase anawasocheretsa, kotero kuti anachita zoyipa zambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Yehova anawawononga pamene Aisraeli ankafika.

10Yehova anayankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri kuti, 11“Manase mfumu ya Yuda wachita machimo onyansawa ndipo wachita zoyipa kupambana Aamori amene analipo kale iye asanabadwe ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda ndi mafano ake. 12Choncho Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taonani, ndikubweretsa pa Yerusalemu ndi Yuda mavuto akuti aliyense amene adzawamve adzathedwa nzeru. 13Ndidzalanga Yerusalemu ndi Yuda pogwiritsa ntchito muyeso umene ndinalangira Samariya ndi Ahabu pamodzi ndi nyumba yake. Ndidzayeretsa Yerusalemu monga mmene munthu amachitira popukuta mbale ndipo atayipukuta amayivundikira pansi. 14Ndidzawataya anthu otsala amene ndi cholowa changa ndipo ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo. Adzachotsedwa ndipo adaniwo adzawalanda zinthu zonse 15chifukwa anachita zoyipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuchokera tsiku limene makolo awo anatuluka mu Igupto mpaka lero lino.’ ”

16Kuwonjezera apo, Manase anakhetsa kwambiri magazi a anthu osalakwa mpaka magaziwo kuyenderera mu Yerusalemu kuyambira mbali ina mpaka mbali ina, kuphatikiza pa kuchimwitsa Yuda, kotero kuti anthu anachita zoyipa pamaso pa Yehova.

17Ntchito zina za Manase ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 18Manase anagona ndi makolo ake ndipo anayikidwa mʼmanda mʼmunda wa Uza, ku nyumba yaufumu. Ndipo Amoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Amoni Mfumu ya Yuda

19Amoni anakhala mfumu ali ndi zaka 22 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka ziwiri. Amayi ake anali Mesulemeti mwana wa Haruzi, wochokera ku Yotiba. 20Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira Manase abambo ake. 21Anatsatira makhalidwe onse a abambo ake. Ankapembedza mafano amene abambo akewo ankawapembedza ndipo ankawagwadira. 22Iyeyo anasiya Yehova Mulungu wa makolo ake ndipo sanayende mʼnjira ya Yehova.

23Nduna za Amoni zinamuchita chiwembu ndipo zinamupha mʼnyumba yake. 24Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anachitira chiwembu Mfumu Amoni, nayika Yosiya mwana wake kukhala mfumu mʼmalo mwake.

25Ntchito zina za Amoni ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 26Iye anayikidwa mʼmanda ake mʼmunda wa Uza. Ndipo Yosiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.