列王紀上 17 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

列王紀上 17:1-24

以利亞預言旱災

1有一位先知名叫以利亞,是基列提斯比人。他對亞哈說:「我憑我事奉的以色列的上帝——永活的耶和華起誓,如果我不禱告,這幾年必沒有雨水和甘露。」 2耶和華對以利亞說: 3「你離開這裡,往東去,到約旦河以東的基立溪旁躲起來。 4你可以喝基立溪的水,我已吩咐烏鴉在那裡供應你食物。」 5以利亞遵從耶和華的話,到約旦河東的基立溪旁住下來。 6烏鴉每天早晚為他叼來餅和肉,他喝溪裡的水。

撒勒法的寡婦

7因為天旱無雨,過了些日子,溪水乾了。 8耶和華對他說: 9「你去西頓撒勒法,我已吩咐那裡的一個寡婦供養你。」 10他來到撒勒法的城門口,看見一個寡婦在撿柴,就對她說:「請給我一點水喝。」 11那婦人去拿水的時候,以利亞又說:「請給我拿一點餅。」 12她說:「我憑你的上帝——永活的耶和華起誓,我沒有餅,我罈裡只有一把麵,瓶裡只有一點油。我來撿柴就是要回去做餅,與兒子吃完後,就只能等死了。」

13以利亞說:「不要害怕,你可以照你所說的去做餅,只是你要先做一小塊餅給我,然後再做給你和你兒子。 14因為以色列的上帝耶和華說,『在耶和華降雨之前,你罈裡的麵和瓶裡的油必不會空。』」 15那婦人就依照以利亞的話做了。婦人一家和以利亞就這樣吃了許多天, 16罈裡的麵沒有用完,瓶裡的油也沒有用光,應驗了耶和華藉以利亞說的話。

17後來,婦人的兒子病了,病情越來越重,最後死了。 18婦人對以利亞說:「上帝的僕人啊,我跟你有什麼關係?你到我這裡來是要讓上帝想起我的罪,取我兒子的性命嗎?」 19以利亞對婦人說:「把你兒子交給我。」隨後,他從婦人懷中接過孩子,抱到樓上自己的房間,放在床上。 20他向耶和華呼求道:「我的上帝耶和華啊,我寄居在這寡婦家裡,你為什麼降禍給她,奪去她兒子的性命呢?」 21他三次伏在孩子身上,求告耶和華說:「我的上帝耶和華啊,求你讓這孩子活過來吧。」 22耶和華聽了以利亞的祈求,孩子就活過來了。 23以利亞將孩子從樓上抱下來,交給他母親,說:「看,你兒子活過來了!」 24婦人對以利亞說:「現在我知道你是上帝的僕人,耶和華藉你口所說的都是真的。」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 17:1-24

Makwangwala Adyetsa Eliya

1Ndipo mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, anati kwa Ahabu, “Pali Yehova wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene ndimamutumikira, sipadzakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditanena.”

2Pamenepo Yehova anayankhula ndi Eliya kuti, 3“Choka kuno, upite kummawa, ukabisale mʼmbali mwa mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani. 4Uzikamwa mu mtsinjemo, ndipo ndalamula makwangwala kuti azikakudyetsa kumeneko.”

5Choncho Eliya anachita zomwe Yehova anamuwuza. Anapita ku mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani, nakakhala kumeneko. 6Makwangwala ankabweretsera buledi ndi nyama mmawa ndi madzulo, ndipo ankamwa mu mtsinjemo.

Mayi Wamasiye wa ku Zarefati

7Patapita masiku, mtsinjewo unaphwa chifukwa mvula sinagwe mʼdzikomo. 8Yehova anayankhula naye kuti, 9“Nyamuka tsopano, pita ku Zarefati ku Sidoni ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mkazi wamasiye wa kumeneko kuti azikakudyetsa.” 10Choncho iye ananyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, taonani mkazi wamasiye amatola nkhuni. Anamuyitana ndi kumuwuza kuti, “Patseni madzi pangʼono mʼchikho kuti ndimwe.” 11Mayi wamasiye uja ankapita kukatunga madzi, Eliya anamuyitananso namuwuza kuti, “Chonde munditengerekonso buledi.”

12Iye anayankha kuti “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ine ndilibe chakudya china chilichonse, koma kaufa pangʼono mʼmbiya ndi mafuta pangʼono mʼbotolo. Ine ndikutola tinkhuni tochepa kuti ndipite nato ku nyumba ndi kukaphika chakudya changa ndi cha mwana wanga, kuti tikadye kenaka tife.”

13Eliya anati kwa iye, “Musachite mantha. Pitani mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mundipangire kachakudya pangʼono kuchokera pa ufa umene muli nawo ndi kubwera nako kwa ine, ndipo kenaka mukaphike choti mudye inuyo ndi mwana wanuyo. 14Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ufa umene uli mʼmbiyamo sudzatha ndipo mafuta amene ali mʼbotolomo sadzathanso mpaka tsiku limene Yehova adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”

15Mayi wamasiyeyo anapita nakachita zimene Eliya anamuwuza. Choncho panali chakudya cha Eliya, mayiyo pamodzi ndi banja lake lonse chimene anadya masiku ambiri. 16Pakuti ufa umene unali mʼmbiya sunathe ndiponso mafuta amene anali mʼbotolo sanathe, monga momwe ananenera Yehova kudzera mwa Eliya.

17Tsiku lina mwana wake wa mkazi wamasiye uja, mwini nyumbayo, anadwala. Matenda ananka nakulirakulirabe, ndipo kenaka analeka kupuma. 18Mayiyo anati kwa Eliya, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu munthu wa Mulungu? Kodi munabwera kuno kudzandikumbutsa tchimo langa ndi kudzandiphera mwana wanga?”

19Eliya anayankha kuti, “Patseni mwana wanuyo.” Iye anatenga mwanayo mʼmanja mwa mayiyo napita naye mʼchipinda chapamwamba, kumene Eliyayo amagona, namugoneka pa bedi lake. 20Kenaka Eliya anafuwula kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wanga, kodi mwabweretsanso choyipa chotere pa mkazi wamasiye amene ine ndikukhala naye, pakuchititsa kuti mwana wake afe?” 21Pamenepo Eliya anakumbatira mwanayo katatu ndi kufuwula kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wanga, mubwezereni mwanayu moyo wake!”

22Yehova anamva kufuwula kwa Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unabwerera mwa iye ndipo anatsitsimuka. 23Eliya ananyamula mwanayo natsika naye kuchoka mʼchipinda chapamwamba chija nalowa naye mʼnyumba. Anamupereka kwa amayi ake ndipo anati, “Taonani, mwana wanu ali ndi moyo!”

24Pamenepo mayiyo anati kwa Eliya, “Tsopano ndadziwa kuti ndinu munthu wa Mulungu ndipo mawu a Yehova amene mumayankhula ndi owona.”