列王紀上 14 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

列王紀上 14:1-31

亞希雅對耶羅波安的預言

1那時,耶羅波安的兒子亞比雅病了, 2耶羅波安就吩咐妻子:「你喬裝改扮使人認不出你是我妻子,然後去示羅找那位預言我做王的先知亞希雅3你要帶十個餅、一些薄餅和一瓶蜂蜜去,他將告訴你孩子的病情會怎樣。」

4耶羅波安的妻子就照他的話做,前往示羅,來到亞希雅家。那時亞希雅因年紀老邁,眼睛已失明。 5耶和華預先告訴亞希雅說:「耶羅波安的妻子會喬裝成別的婦女,前來問你有關她兒子的病情,你要如此如此回答她。」

6她剛進門,亞希雅聽見她的腳步聲就說:「耶羅波安的妻子啊,你進來吧,為什麼喬裝改扮呢?我奉命告訴你一個噩耗。 7你回去告訴耶羅波安,『以色列的上帝耶和華說,我從百姓中擢升你,立你做我以色列子民的王。 8我把國從大衛家奪走賜給你,你卻沒有像我僕人大衛那樣遵守我的誡命,全心聽從我,做我視為正的事, 9反而比前人行惡更甚,為自己設立其他神明,鑄造神像,惹我發怒,把我拋在腦後。 10所以,我要降禍給耶羅波安家,從以色列剷除耶羅波安家所有的男子,不論是奴隸還是自由人。我要像清除糞便一樣,把耶羅波安家焚燒淨盡。 11耶羅波安家人中,死在城中的必被狗吃,死在田野的必被鳥吃。這是耶和華說的。』

12「現在你回家去吧,你一進城,孩子就會死。 13以色列會為他哀悼,把他埋葬。耶羅波安家人中只有他將得到安葬,因為以色列的上帝耶和華在他身上看見了良善。 14耶和華必為自己立一位君王統治以色列,他必剷除耶羅波安家。現在就是時候了。 15耶和華將擊打以色列人,使他們像水中的蘆葦一樣顫抖不已。耶和華將把以色列人從祂賜給他們祖先的佳美之地連根拔起,拋散到幼發拉底河的彼岸,這都是因為他們製造亞舍拉神像,惹耶和華發怒。 16因為耶羅波安犯罪作孽,使以色列人陷入罪中,耶和華必拋棄以色列。」

17耶羅波安的妻子動身回到得撒,剛邁過家門檻,孩子就死了。 18以色列人埋葬了他,為他哀悼,正應驗了耶和華藉祂僕人亞希雅先知說的話。

19耶羅波安其他的事,不論文治武功,都記在以色列的列王史上。 20他做王二十二年,然後與祖先同眠。他兒子拿答繼位。

羅波安做猶大王

21所羅門的兒子羅波安猶大王。他四十一歲登基,在耶路撒冷,就是耶和華從以色列眾支派中選擇來立祂名的城執政十七年。羅波安的母親是亞捫拿瑪22猶大人做耶和華視為惡的事,他們的罪行比他們祖先所做的更惹耶和華發怒。 23他們在各高崗上、樹蔭下為自己建造邱壇,豎立神柱和亞舍拉神像, 24國中甚至男廟妓充斥。猶大人仿效耶和華在以色列人面前趕走的外族人,行各種可憎之事。

25羅波安王執政第五年,埃及示撒上來攻陷耶路撒冷26搶走了耶和華的殿和王宮裡所有的寶物,包括所羅門製造的金盾牌。 27羅波安王就造了銅盾牌代替那些金盾牌,交給看守宮門的護衛長看管。 28每次王進耶和華的殿,護衛軍就帶上盾牌,用完後放回護衛房。

29羅波安其他的事及其一切所作所為都記在猶大的列王史上。 30羅波安常常與耶羅波安爭戰。 31羅波安與祖先同眠後,葬在大衛城的祖墳裡。他母親是亞捫拿瑪。他兒子亞比央繼位。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 14:1-31

Ahiya Anenera za Kugwa kwa Yeroboamu

1Pa nthawi imeneyo Abiya mwana wa Yeroboamu anayamba kudwala, 2ndipo Yeroboamu anati kwa mkazi wake, “Nyamuka ndipo udzibise kuti usadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yeroboamu, ndipo upite ku Silo. Kumeneko kuli mneneri Ahiya amene anandiwuza kuti ndidzakhala mfumu ya anthu awa. 3Utenge buledi khumi, makeke ndiponso botolo la uchi ndipo upite kwa mneneriyo. Iye adzakuwuza zimene zidzamuchitikire mwanayu.” 4Choncho mkazi wa Yeroboamu anadzibisa ndipo anapita ku nyumba ya Ahiya ku Silo.

Tsono Ahiya sankatha kupenya bwino. Ankangoona kuti mbuu chifukwa cha ukalamba. 5Koma Yehova nʼkuti atamuwuza Ahiya kuti, “Taona, mkazi wa Yeroboamu akubwera kudzafunsa iwe za mwana wake pakuti akudwala, ndiye udzamuyankhe zakutizakuti mkaziyo. Iye akafika, adzadzibisa.”

6Tsono Ahiya atamva mgugu wa mapazi ake pa khomo, anati, “Lowa, iwe mkazi wa Yeroboamu. Bwanji ukudzibisa? Ine ndatumidwa kuti ndikuwuze nkhani yoyipa. 7Pita, kamuwuze Yeroboamu kuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakukweza pakati pa anthu ndipo ndinakuyika kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli. 8Ndinachotsa ufumu ku nyumba ya Davide ndi kuwupereka kwa iwe, koma iwe sunafanane ndi mtumiki wanga Davide, amene ankasunga malamulo anga ndi kunditsata Ine ndi mtima wake wonse, kuchita zolungama zokhazokha pamaso panga. 9Ndipo iwe wachita zoyipa kupambana onse amene analipo kale. Wadzipangira milungu ina, mafano a zitsulo. Iweyo wandikwiyitsa ndipo wandiwukira.

10“ ‘Choncho taona, ndidzabweretsa masautso pa nyumba ya Yeroboamu. Ndipo ndidzawononga munthu wamwamuna aliyense wa pa banja lako, kapolo pamodzi ndi mfulu yemwe mʼdziko la Israeli. Ndidzatentha nyumba ya Yeroboamu monga mmene munthu amatenthera ndowe mpaka yonse kutheratu. 11Agalu adzadya aliyense wa banja la Yeroboamu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame zamlengalenga zidzadya iwo amene adzafere ku thengo, pakuti Yehova watero!’

12“Ndipo iwe nyamuka, bwerera ku nyumba kwako. Phazi lako likadzangoponda mu mzindamo, mwanayo adzamwalira. 13Aisraeli onse adzalira maliro ake ndi kumuyika mʼmanda. Ndi yekhayo wa banja la Yeroboamu amene adzayikidwe mʼmanda, pakuti ndi mwa iye yekha mmene Yehova Mulungu wa Israeli wapezamo kanthu kabwino.

14“Koma Yehova adzadzisankhira yekha mfumu yolamulira Israeli imene idzawononga banja la Yeroboamu. Tsiku lake ndi lero! Ndati chiyani? Inde, ndi lero lomwe lino. 15Ndipo Yehova adzakantha Israeli, kotero kuti adzakhala ngati bango logwedera pa madzi. Iye adzazula Israeli mʼdziko labwino limene analipereka kwa makolo ake ndi kuwamwazira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, chifukwa anakwiyitsa Yehova pamene anapanga mafano a Asera. 16Ndipo Iye sadzasamalanso Israeli chifukwa cha machimo amene anachita Yeroboamu ndi kuchimwitsa nawo Israeli.”

17Tsono mkazi wa Yeroboamu anayimirira nachoka kupita ku Tiriza. Atangoponda pa khonde la nyumba yake, mwana uja anamwalira. 18Aisraeli anamuyika mʼmanda, ndipo onse analira maliro ake, monga momwe Yehova ananenera kudzera mwa mtumiki wake, mneneri Ahiya.

19Ntchito zina pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu, nkhondo zake ndi mmene ankalamulirira zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli. 20Iye analamulira zaka 22 ndipo anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Nadabu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Rehobowamu Mfumu ya Yuda

21Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya ku Yuda. Iye analowa ufumu ali ndi zaka 41, ndipo analamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anawusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti ayikemo Dzina lake. Amayi ake anali Naama, wa ku Amoni.

22Anthu a ku Yuda anachita zoyipa pamaso pa Yehova kupambana mmene anachitira makolo awo ndipo Yehova anawakwiyira. 23Iwonso anadzipangira malo opembedzerapo mafano pa chitunda chilichonse ndi kuyimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya Asera pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. 24Mʼdzikomo munalinso amuna ochita zachiwerewere mwa chipembedzo. Anthu ankachita zonyansa zonse za anthu a mitundu ina imene Yehova anayipirikitsa asanafike Aisraeli.

25Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisaki, mfumu ya Igupto, anadzathira nkhondo Yerusalemu. 26Ananyamula chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso chuma cha ku nyumba ya mfumu. Anatenga chilichonse, ngakhalenso zishango zonse zagolide zimene Solomoni anapanga. 27Ndipo Mfumu Rehobowamu anapanga zishango zamkuwa mʼmalo mwake, nazipereka mʼmanja mwa olamulira alonda a pa khomo pa nyumba ya mfumu. 28Nthawi zonse mfumu ikamapita ku Nyumba ya Yehova, alonda ankanyamula zishangozo, kenaka ankazisunga mʼchipinda cha alonda.

29Tsono ntchito zina za Rehobowamu ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 30Panali nkhondo zosalekeza pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu. 31Ndipo Rehobowamu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Amayi ake anali Naama wa ku Amoni. Ndipo Abiya analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.