出埃及記 34 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

出埃及記 34:1-35

新的約版

1耶和華對摩西說:「你要鑿出兩塊石版,跟你之前摔碎的兩塊一樣,我要把前兩塊石版上的字刻在上面。 2你要預備好,明天清早你要上西奈山頂來見我。 3誰也不可與你同來,整座山上都不可有人,就是牛羊也不得在山前吃草。」 4於是,摩西鑿出兩塊石版,跟先前的兩塊一樣。他清早起來,照著耶和華的吩咐把石版帶到西奈山上。 5耶和華在雲中降臨和摩西一同站在那裡,宣告祂的名——耶和華。 6耶和華在摩西面前經過,並且宣告說:「我是耶和華,我是耶和華,是有憐憫和恩典的上帝,不輕易發怒,充滿慈愛,無比信實, 7向千萬人彰顯慈愛,赦免罪惡和過犯,但決不免除罪責,必向子孫追討父輩的罪債,直到三四代。」 8摩西急忙俯伏在地上敬拜, 9說:「主啊,如果我在你面前蒙了恩,求你與我們同行。雖然百姓頑固不化,求你赦免我們的過犯和罪惡,接納我們做你的子民。」

10耶和華說:「我要與你立約,我要在你的同胞面前行奇事,是天下萬國從未有過的奇事,你周圍的外族人必看見我為你做的偉大而可畏的事。 11你要遵行我今天的吩咐。我必從你面前驅逐亞摩利人、迦南人、人、比利洗人、希未人和耶布斯人。 12你要謹慎,到了目的地後,不可與當地的居民立約,免得因此而陷入網羅。 13相反,要拆掉他們的祭壇,打碎他們的神柱,砍掉他們的亞舍拉神像。 14不可拜別的神明,因為耶和華是痛恨不貞的上帝,祂名為『痛恨不貞』。

15「不可與當地的居民立約,免得他們與自己的神明苟合時邀請你,你就吃他們的祭物, 16給兒子娶他們的女兒為妻,以致她們與自己的神明苟合時誘使你的兒子犯同樣的罪。

17「不可為自己鑄造神像。

18「要守除酵節,照我的吩咐在亞筆月所定的時間吃七天的無酵餅,因為你是在亞筆月離開埃及的。

19「凡是頭胎生的兒子都屬於我,包括牲畜中一切頭胎生的公牛和公羊。 20頭胎生的驢要用羊贖回,如果不用羊贖回,就要打斷牠的脖子。凡頭胎生的男嬰,都要贖回他的性命。誰也不可空手來朝見我。

21「一週工作六天,第七天要休息,就是耕種和收割時也要休息。

22「在收割初熟麥子的時候,要守七七收割節,年底要守收藏節。 23所有的男子都要一年三次來朝見主耶和華——以色列的上帝。 24我要從你面前趕走外族人,擴張你的領土。你一年三次來朝見你的上帝耶和華時,必沒有人貪戀你的土地。

25「不可把祭牲的血和有酵的餅一起獻給我。逾越節的祭物也不可留到第二天早晨。

26「要把田中最好的初熟之物送到你們的上帝耶和華的殿中。

「不可用母山羊的奶煮牠的小羊羔。」

27耶和華又對摩西說:「你要把我說的這些話記錄下來,因為我要按這些話跟你和以色列人立約。」 28摩西在耶和華那裡待了四十晝夜,沒吃也沒喝。耶和華把約的內容,就是十條誡命,寫在石版上。

29摩西手裡拿著兩塊約版下西奈山,他不知道自己因為曾與耶和華說話而臉上發光。 30亞倫和所有的以色列百姓看見摩西臉上發光,都不敢走近他。 31摩西召他們過來,亞倫和會眾的首領便上前來。摩西與他們說話。 32之後,所有的以色列人都來到他面前,他就把耶和華在西奈山上的吩咐都告訴他們。 33說完之後,他就用帕子遮住自己的臉。 34每當進到會幕跟耶和華說話時,他就揭開帕子,出來後便把耶和華的吩咐告訴以色列百姓。 35百姓會看到他臉上發光,於是他再用帕子遮住臉,直到下次與耶和華說話的時候才揭開。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 34:1-35

Miyala ina Yatsopano

1Yehova anati kwa Mose, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo Ine ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. 2Ukonzeke mmamawa, ndipo ubwere ku Phiri la Sinai. Udzaonekera pamaso panga pamwamba pa phiri. 3Palibe amene abwere nawe kapena kuoneka pena paliponse pafupi ndi phiri. Ndipo ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmbali mwa phirilo.”

4Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo anapita ku Phiri la Sinai mmawa atanyamula miyala iwiri mʼmanja mwake monga momwe Yehova anamulamulira. 5Ndipo Yehova anatsika mu mtambo ndi kuyima pamodzi ndi Mose ndi kulengeza dzina lake lakuti Yehova. 6Ndipo Iye anadutsa kutsogolo kwa Mose akulengeza kuti, “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosapsa mtima msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, 7waonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu miyandamiyanda, wokhululukira zoyipa, kuwukira, ndiponso tchimo, komatu salekerera ochimwa kuti asalangidwe. Iye amalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha machimo a makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi.”

8Pamenepo Mose anawerama pansi napembedza. 9Iye anati, “Chonde Ambuye, ngati ndapeza chisomo pamaso panu, lolani Ambuye kuti mupite nafe pamodzi. Ngakhale kuti anthuwa ndi nkhutukumve, khululukirani zoyipa ndi machimo athu, ndipo mutenge ife kukhala anthu anu.”

10Choncho Yehova anati: “Ine ndikuchita nanu pangano. Ndidzachita zodabwitsa pamaso pa anthu onse zimene sizinachitikenso ndi mtundu wina uliwonse wa anthu pa dziko lonse lapansi. Anthu amene mudzakhala pakati pawo adzaona kuopsa kwa ntchito imene Ine Yehova ndidzakuchitireni. 11Mverani zimene ndikukulamulirani lero. Ine ndidzathamangitsa pamaso panu Aamori, Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi. 12Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa mukadzatero iwo adzakhala ngati msampha pakati panu. 13Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, ndipo mukadule mitengo yawo ya Asera. 14Musapembedze mulungu wina, pakuti Yehova amene dzina lake ndi Nsanje, ndi Mulungu wa nsanje.

15“Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa iwo akamakachita zadama ndi milungu yawo ndi kupereka nsembe, adzakuyitanani ndipo inu mudzadya nsembe zawo. 16Ndipo inu mukasankha ena mwa ana awo aakazi kukhala akazi a ana anu, akaziwo akakachita zadama ndi milungu yawo, akatsogolera ana anu aamuna kuchita chimodzimodzi.

17“Musadzipangire milungu yosungunula.

18“Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga momwe ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi pa nthawi yoyikika mwezi wa Abibu, pakuti mwezi umenewu inu munatuluka mʼdziko la Igupto.

19“Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi ziweto zoyamba kubadwa zazimuna kuchokera ku ngʼombe kapena nkhosa. 20Muziwombola mwana woyamba kubadwa wa bulu popereka mwana wankhosa. Mukapanda kumuwombola mupheni. Muziwombola ana anu onse aamuna.

“Palibe ndi mmodzi yemwe adzaonekere pamaso panga wopanda kanthu mʼdzanja lake.

21“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri, musagwire ntchito ina iliyonse, Ngakhale nthawi yolima ndi yokolola muyenera kupuma.

22“Muzichita Chikondwerero cha Masabata, chifukwa ndi chikondwerero cha tirigu woyambirira kucha, ndiponso ndi chikondwerero cha kututa zokolola pakutha pa chaka. 23Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu wa Israeli, katatu pa chaka. 24Ine ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufikako ndi kukulitsa malire anu. Palibe ndi mmodzi yemwe adzafune kulanda dziko lanu ngati inu muzidzapita katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, chaka chilichonse.

25“Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti, ndipo musasunge nsembe ya pa Chikondwerero cha Paska mpaka mmawa.

26“Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu.

“Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.”

27Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba mawu awa pakuti potsatira mawuwa, ine ndipangana pangano ndi iwe ndi Israeli.” 28Mose anakhala kumeneko pamodzi ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku, wosadya kanthu kapena kumwa madzi. Ndipo iye analemba pa miyala ija mawu a pangano, malamulo khumi.

Nkhope ya Mose Inyezimira

29Mose anatsika kuchokera mʼPhiri la Sinai pamodzi ndi miyala iwiri ija ya pangano mʼmanja mwake. Iye sanazindikire kuti nkhope yake imanyezimira pakuti anayankhula ndi Yehova. 30Aaroni ndi Aisraeli ataona kuti nkhope ya Mose imanyezimira anaopa kumuyandikira. 31Koma Mose anawayitana. Kotero Aaroni ndi atsogoleri onse a gululo anabwera kwa iye, ndipo anawayankhula. 32Kenaka Aisraeli onse anamuyandikira, ndipo anawapatsa malamulo onse omwe Yehova anamupatsa pa Phiri la Sinai.

33Mose atamaliza kuyankhula nawo anaphimba nkhope yake. 34Koma nthawi zonse popita pamaso pa Yehova kukayankhula naye amachotsa chophimbacho mpaka atatuluka. Ndipo akatuluka kudzawuza Aisraeli zimene walamulidwa, 35iwo amaona nkhope yake ikunyezimira. Choncho Mose amaphimba nkhope yake ngakhale pamene amapita kukayankhula ndi Yehova.