傳道書 12 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

傳道書 12:1-14

1年輕時要記住你的創造主,不要等到衰老的歲月來臨時才哀歎:「我的日子毫無樂趣。」 2那時,太陽、月亮、星星都暗淡無光,雨後烏雲再現; 3守衛家園的手腳顫抖,強壯的身軀變得彎腰駝背;牙齒稀少,無法咀嚼;視力衰退,看不清楚; 4耳朵發背,聽不到推磨聲;小鳥一叫,人就起來;歌聲沙啞,不再美妙; 5懼怕高處,走路戰戰兢兢;頭髮白如銀杏,精力枯竭,慾望蕩然無存;人都走向永遠的歸宿,弔喪的人往來於街上; 6銀鏈斷裂,金碗摔壞,泉旁的瓶子破碎,井口的輪子朽爛。 7那時塵土必歸於塵土,靈也要歸回賜靈的上帝。 8傳道者說:「虛空的虛空,一切都是虛空。」 9傳道者不但有智慧,還把知識傳授給眾人。他經過細心推敲和研究之後,編寫了許多警世的箴言。 10傳道者費盡心思尋找金玉良言,所寫的都是正直誠實的道理。 11智者的言語好像趕牛的刺棍,他們收集的箴言像釘穩的釘子一樣牢靠,都是一位牧者所賜的。 12我親愛的兒子,還有一件事,你要聽我的忠告:著書多,沒有窮盡;讀書多,身體疲勞。

13以上所說的,總而言之,就是要敬畏上帝,遵守祂的誡命,這是人的本分。 14因為人一切的行為,無論善惡,包括一切隱秘事,上帝都必審問。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 12:1-14

1Uzikumbukira mlengi wako

masiku a unyamata wako,

masiku oyipa asanafike,

nthawi isanafike pamene udzanena kuti,

“Izi sizikundikondweretsa.”

2Nthawi ya ukalamba wako, dzuwa ndi kuwala,

mwezi ndi nyenyezi zidzada.

Mitambo idzabweranso mvula itagwa.

3Nthawi imene manja ako adzanjenjemera,

miyendo yako idzafowoka,

pamene mano ako adzalephera kutafuna chifukwa ndi owerengeka,

ndipo maso ako adzayamba kuchita chidima.

4Makutu ako adzatsekeka,

ndipo sudzamva phokoso lakunja;

sudzamvanso kusinja kwa pa mtondo

kapena kulira kwa mbalame mmawa.

5Imeneyi ndiyo nthawi imene anthu amaopa kupita kumalo okwera,

amaopa kuyenda mʼmisewu;

Mutu umatuwa kuti mbuu,

amayenda modzikoka ngati ziwala

ndipo chilakolako chimatheratu.

Nthawi imeneyo munthu amapita ku nyumba yake yamuyaya

ndipo anthu olira maliro amayendayenda mʼmisewu.

6Kumbukira Iye chingwe cha siliva chisanaduke,

kapena mbale yagolide isanasweke;

mtsuko usanasweke ku kasupe,

kapena mkombero usanathyoke ku chitsime.

7Iyi ndi nthawi imene thupi lidzabwerera ku dothi, kumene linachokera,

mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene anawupereka.

8“Zopanda phindu! Zopandapake!” akutero Mlaliki.

“Zonse ndi zopandapake!”

Mawu Otsiriza

9Mlaliki sanali wozindikira zinthu kokha ayi, komanso ankaphunzitsa anthu. Iye ankasinkhasinkha ndi kufufuzafufuza ndi kulemba mwadongosolo miyambi yambiri. 10Mlaliki anafufuzafufuza kuti apeze mawu oyenera, ndipo zimene analemba zinali zolondola ndiponso zoona.

11Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga, zokamba zawo zimene anasonkhanitsa zili ngati misomali yokhomera, yoperekedwa ndi mʼbusa mmodzi. 12Samalira mwana wanga, za kuwonjezera chilichonse pa zimenezi.

Kulemba mabuku ambiri sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi.

13Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa:

uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake,

pakuti umenewu ndiwo udindo

wa anthu onse.

14Pakuti Mulungu adzaweruza zochita zonse,

kuphatikizanso zinthu zonse zobisika,

kaya zabwino kapena zoyipa.