使徒行傳 3 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

使徒行傳 3:1-26

彼得醫治瘸腿的乞丐

1一天,在下午三點禱告的時間,彼得約翰去聖殿。 2有一個生來瘸腿的人天天被人抬到聖殿美門的外面,向進殿的人乞討。 3他看見彼得約翰要進殿,就求他們施捨。 4二人定睛看他,彼得說:「看著我們!」 5那人就緊盯著他們,期盼能有所收穫。

6彼得說:「金子、銀子我都沒有,但是我把我有的給你。我奉拿撒勒人耶穌基督的名,命令你起來行走!」

7彼得拉著他的右手扶他起來,那人的腳和踝骨立刻變得強健有力。 8他跳了起來,站穩後開始行走,跟著彼得約翰進入聖殿,走著跳著讚美上帝。 9大家看見他一邊走一邊讚美上帝, 10認出他就是那個在美門外面的乞丐,都為發生在他身上的事而感到驚奇、詫異。 11那乞丐緊緊拉著彼得約翰的手走到所羅門廊,眾人都跑過來,嘖嘖稱奇。

彼得傳揚基督

12彼得看見這情形,就對大家說:「以色列人啊,何必驚奇呢?為什麼一直盯著我們呢?你們以為我們是憑自己的能力和虔誠叫這人行走嗎? 13亞伯拉罕以撒雅各的上帝,就是我們祖先的上帝,已經使祂的僕人耶穌得了榮耀。你們把耶穌交給彼拉多,儘管彼拉多想釋放祂,你們卻在彼拉多面前棄絕祂! 14你們棄絕了那聖潔公義者,竟然要求彼拉多釋放一個兇手。 15你們殺了生命之主,上帝卻使祂從死裡復活了。我們都是這事的見證人。 16你們認識的這個乞丐因為相信耶穌的名,得到了醫治。你們都看見了,他能痊癒是因為他信耶穌。

17「弟兄們,我知道你們的所作所為是出於無知,你們的官長也是一樣。 18但是上帝早已藉眾先知預言基督要受害,這事果然應驗了。 19所以你們要悔改,歸向上帝,祂將除去你們一切的罪惡, 20賜給你們煥然一新的日子,也將差遣祂預先為你們選立的基督耶穌降臨。 21基督必須留在天上,直到萬物更新的時候,這是上帝自古以來藉聖先知的口說的。 22摩西曾經說,『主——你們的上帝將要在你們中間興起一位像我一樣的先知。你們要留心聽祂的話, 23凡不聽的,必將他從民中剷除。』

24「從撒母耳到後來的所有先知都宣告過這些日子。 25你們是先知的子孫,也承受了上帝和你們祖先所立的約。上帝曾對亞伯拉罕說,『天下萬族必因你的後裔而蒙福。』 26上帝興起祂的僕人,首先差遣祂到你們中間賜福給你們,使你們脫離罪惡。」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 3:1-26

Petro Achiritsa Wolumala Miyendo

1Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera nthawi ya 3 koloko masana. 2Ndipo munthu wolumala chibadwire ankanyamulidwa tsiku ndi tsiku kukayikidwa pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola kuti azikapempha amene amalowa ku bwalo la Nyumbayo. 3Ataona Petro ndi Yohane ali pafupi kulowa anawapempha ndalama. 4Iwo anamuyangʼanitsitsa iye. Kenaka Petro anati, “Tiyangʼane!” 5Munthuyo anawayangʼanitsitsa kuyembekezera kuti alandira kanthu kuchokera kwa iwo.

6Petro anati kwa iye, “Ine ndilibe siliva kapena golide, koma chimene ndili nacho ndikupatsa. Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda.” 7Ndipo anamugwira dzanja lamanja, namuthandiza kuti ayimirire ndipo nthawi yomweyo mapazi ake ndi akakolo ake analimba. 8Iye analumpha ndi kuyamba kuyenda. Kenaka analowa nawo pamodzi mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, akuyenda ndi kulumpha ndiponso kuyamika Mulungu. 9Anthu onse atamuona akuyenda ndiponso kuyamika Mulungu, 10anamuzindikira kuti ndi yemwe uja ankakhala pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola, ndipo anazizwa ndi kudabwa ndi zimene zinamuchitikira.

Petro Ayankhula kwa Anthu

11Wopempha uja akuyenda pamodzi ndi Petro ndi Yohane, anthu onse anadabwa ndipo anawathamangira iwo kumalo wotchedwa Khonde la Solomoni. 12Petro ataona zimenezi anawawuza kuti, “Inu Aisraeli, chifukwa chiyani mukudabwa ndi zimene zachitikazi? Bwanji mukuyangʼana ife ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu yathu kapena chifukwa cha kupembedza kwathu? 13Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, wamulemekeza mtumiki wake Yesu. Amene inu munamukana pamaso pa Pilato ndi kumupereka Iye kuti aphedwe, ngakhale kuti Pilato anafuna kuti amumasule. 14Koma inu munamukana Woyera ndi Wolungamayo ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wakupha anthu. 15Inu munapha mwini moyo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi. 16Mwachikhulupiriro mʼdzina la Yesu, munthu uyu amene mukumuona ndi kumudziwa analimbikitsidwa. Mʼdzina la Yesu ndi chikhulupiriro chimene chili mwa iye chamuchiritsa kwathunthu, monga nonse mukuona.

17“Tsopano abale ine ndikudziwa kuti inu munachita zimenezi mosadziwa, monga momwenso anachitira atsogoleri anu. 18Koma umu ndi mmene Mulungu anakwaniritsira zimene zinanenedwa kale ndi aneneri onse, kuti Khristu adzamva zowawa. 19Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye, 20ndi kuti Iye atumize Yesu Khristu amene anasankhidwa chifukwa cha inu. 21Iye ayenera kukhalabe kumwamba mpaka nthawi ya kukonzanso zinthu zonse monga Mulungu analonjeza kale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima. 22Pakuti Mose anati, ‘Ambuye Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri monga ine kuchokera pakati pa anthu anu; mumvere zonse zimene iye akuwuzeni. 23Aliyense amene sadzamvera mawu a mneneriyo, adzayenera kuchotsedwa pakati pa abale ake.’

24“Ndipo aneneri onse ambiri amene anayankhula kuyambira Samueli, ananeneratu za masiku ano. 25Inu ndinu ana a aneneri ndiponso ana apangano limene Mulungu anachita ndi makolo anu. Iye anati kwa Abrahamu, ‘Anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako.’ 26Pamene Mulungu anaukitsa mtumiki wake, anamutuma Iye poyamba kwa inu kuti akudalitseni pobweza aliyense wa inu ku zoyipa zake.”