以西結書 32 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以西結書 32:1-32

為法老唱哀歌

1第十二年十二月一日,耶和華對我說: 2「人子啊,你要為埃及王法老唱哀歌,對他說,

『你自認為是列邦中的雄獅,

其實你像激蕩江河、

用腳把江河攪渾的海怪。

3主耶和華說,

我要差遣多國組成的大軍,

用我的網把你拉上來,

4拋在地上,丟在田野,

給天上的飛鳥吃,

讓地上的走獸飽餐。

5我要把你的肉丟在山間,

把你的屍首填滿山谷,

6用你的血澆灌大地,

漫過群山,溢滿溝壑。

7當我消滅你的時候,

我要用雲遮蔽天空,

使日月無光,星辰昏暗。

8我要遮蔽天上所有的光,

使黑暗籠罩你的四境。

這是主耶和華說的。

9「『我把你滅亡的消息帶到你不認識的列邦時,必使許多人惶恐不安。 10我在他們面前揮刀攻擊你的時候,各國的人都必因你而驚駭,他們的君王必膽戰心驚。在你傾覆那天,他們都必時刻為自己的性命戰戰兢兢。』

11「主耶和華這樣說,『巴比倫王的刀必來攻擊你。 12我要使你的人民喪身在各國中最殘暴的勇士刀下。

『他們必摧毀埃及的驕傲,

消滅她的人民。

13我要殺盡她河邊的牲畜,

使人足獸蹄不再攪渾河水。

14我要使埃及的河流清澈見底,

像油一樣緩緩流淌。

這是主耶和華說的。

15我要使埃及的土地荒涼,

毀滅其中的居民,

那時他們就知道我是耶和華。

16「『這是列國為埃及唱的哀歌,各國的婦女要為埃及和她的人民唱這哀歌。這是主耶和華說的。』」

17第十二年十二月十五日,耶和華對我說: 18「人子啊,為埃及的百姓哀哭吧!我要把她與各強國的人民一同送入陰間。

19埃及啊,你比誰更美呢?

你下去跟未受割禮的人躺在一起吧!

20埃及人要倒斃在喪身刀下的人當中。刀已出鞘,她和她的國民要被拖走。 21英勇的統領要在陰間談論埃及王和他的盟友說,『這些喪身刀下、未受割禮的人下來長眠了。』

22亞述和她的大軍都在那裡,她周圍是她大軍的墳墓。他們都是喪身刀下的人。 23他們的墳墓在陰間的最深處,她的大軍躺臥在她墳墓的周圍。他們生前曾使人恐懼,如今卻喪身刀下。 24以攔在那裡,她的百姓在她墳墓的周圍。他們都未受割禮,喪身刀下,下到了陰間。他們生前曾使人恐懼,如今卻和下墳墓的人一同抱愧蒙羞。 25以攔躺臥在被殺的人當中,周圍是她百姓的墳墓。他們都未受割禮、喪身刀下。他們生前曾使人恐懼,如今卻和喪身刀下的人在一起,與下墳墓的人一同抱愧蒙羞。

26米設土巴都在那裡,周圍是她們百姓的墳墓。他們都未受割禮,生前曾使人恐懼,如今卻喪身刀下。 27他們沒有古代32·27 古代」有古卷作「未受割禮的」。勇士的榮耀葬禮,那些勇士帶著兵器下到陰間,頭枕著刀,屍骨上蓋著盾,生前曾使人恐懼。

28「法老啊,你要被毀滅,跟那些未受割禮、喪身刀下的人躺在一起。

29以東也在那裡,她的王侯儘管力量強大,卻和喪身刀下的人在一起,與那些未受割禮、下墳墓的人躺在一起。

30「北方的諸王和所有的西頓人也在那裡,雖然他們力量強大,令人恐懼,卻羞辱地與被殺的人下到了陰間。他們未受割禮,與喪身刀下的人躺在一起,與下墳墓的人一同蒙羞。

31「法老看見這些人,便得到了安慰,因為並非只有他的軍隊被殺。這是主耶和華說的。 32我使法老生前給人帶來恐懼,但他和他的百姓最後還是要躺臥在未受割禮、喪身刀下的人當中。這是主耶和華說的。」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 32:1-32

Nyimbo ya Maliro a Farao

1Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiwiri, chaka chakhumi ndi chiwiri, Yehova anandiyankhula kuti: 2“Iwe mwana wa munthu imba nyimbo ya maliro a Farao mfumu ya Igupto ndipo uyiwuze kuti,

“Iwe umadziyesa ngati mkango pakati pa mitundu ya anthu.

Koma iwe uli ngati ngʼona mʼnyanja.

Umakhuvula mʼmitsinje yako,

kuvundula madzi ndi mapazi ako

ndi kudetsa madzi mʼmitsinje.

3“Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Pogwiritsa ntchito gulu la anthu a mitundu yambiri,

ndidzakuponyera khoka langa

ndi kukugwira mu ukonde wanga.

4Ndidzakuponya ku mtunda

ndi kukutayira pansi.

Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe,

ndipo zirombo zonse za dziko lapansi zidzakudya.

5Ndidzayanika mnofu wako pa mapiri

ndipo zigwa zidzadzaza ndi zotsalira zako.

6Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako,

mpaka kumapiri komwe,

ndipo mitsinje idzadzaza ndi mnofu wako.

7Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba miyamba

ndikudetsa nyenyezi zake.

Ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo,

ndipo mwezi sudzawala.

8Zowala zonse zamumlengalenga

ndidzazizimitsa;

ndidzachititsa mdima pa dziko lako,

akutero Ambuye Yehova.

9Ndidzasautsa mitima ya anthu a mitundu yambiri

pamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,

ku mayiko amene iwe sunawadziwe.

10Ine ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yambiri adabwe nawe,

ndipo mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha aakulu chifukwa cha iwe

pamene ndidzaonetsa lupanga langa pamaso pawo.

Pa nthawi ya kugwa kwako,

aliyense wa iwo adzanjenjemera

moyo wake wonse.

11“ ‘Pakuti ndikunena Ine Ambuye Yehova kuti,

“ ‘Lupanga la mfumu ya ku Babuloni

lidzabwera kudzalimbana nawe.

12Ndidzachititsa gulu lako lankhondo kuti ligwe

ndi lupanga la anthu amphamvu,

anthu ankhanza kwambiri pakati pa mitundu yonse ya anthu.

Adzathetsa kunyada kwa Igupto,

ndipo gulu lake lonse la nkhondo lidzagonjetsedwa.

13Ndidzawononga ziweto zake zonse

zokhala mʼmbali mwa madzi ambiri.

Ku madziko sikudzaonekanso phazi la munthu

kapena kudetsedwa ndi phazi la ziweto.

14Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi ake

ndipo mitsinje yake idzayenda mokometsera ngati mafuta,

akutero Ambuye Yehova.

15Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja;

ndikadzawononga dziko lonse

ndi kukantha onse okhala kumeneko,

adzadziwa kuti ndine Yehova.’

16“Mawu angawa adzakhala nyimbo ya maliro. Ana a akazi amitundu ya anthu adzayimba, kuyimbira Igupto ndi gulu lake lonse la nkhondo, akutero Ambuye Yehova.”

17Pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiwiri, Yehova anayankhula kuti: 18“Iwe mwana wa munthu, lirira gulu lankhondo la Igupto ndipo uwalowetse pamodzi ndi anthu ena amphamvu a mayiko ena ku dziko la anthu akufa. 19Ufunse kuti, ‘Ndani amene akukuposa kukongola? Tsikirani ku manda ndi kukhala pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe.’ 20Aigupto adzagwa pakati pa amene akuphedwa ndi lupanga. Lupanga ndi losololedwa kale. Iye adzaphedwa pamodzi ndi gulu lake lankhondo. 21Mʼkati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana za Igupto nʼkumati, ‘Afika kuno anthu osachita mdulidwe aja! Ndi awa agona apawa, ophedwa pa nkhondo.’

22“Asiriya ali komweko ndipo ankhondo ake onse ali mʼmanda omuzungulira. Onsewo anaphedwa pa nkhondo. 23Manda awo ali kumalo ozama a dzenje, ndipo ankhondo ake azungulira manda ake. Onse amene anaopseza dziko la anthu amoyo aphedwa, agwa ndi lupanga.

24“Elamu ali komweko ndipo ankhondo ake ali mʼmanda omuzungulira. Onsewa anaphedwa pa nkhondo, natsikira ku manda ali osachita mdulidwe. Iwowa kale ankaopseza anthu pa dziko lapansi. Tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. 25Amukonzera pogona pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse la nkhondo litazungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe ophedwa ndi lupanga. Paja anthuwa ankaopsa mʼdziko la anthu a moyo. Koma tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Iwo ayikidwa pakati pa anthu ophedwa.

26“Mesaki ndi Tubala ali komweko, pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo litazungulira manda awo. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe, ophedwa ndi lupanga. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. 27Iwo sanayikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene anatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zawo zomwe za nkhondo. Malupanga awo anawayika ku mitu yawo, ndipo zishango zawo anaphimba mafupa awo. Kale anthu amphamvu amenewa ankaopsa dziko la anthu amoyo.

28“Iwenso Farao, udzaphwanyidwa ndi kuyikidwa pakati pa anthu osachita mdulidwe, amene anaphedwa ndi lupanga.

29“Edomu ali kumeneko pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, koma anayikidwa. Ayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje.

30“Akalonga onse akumpoto pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni ali kumeneko. Anatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi ngakhale anali owopsa ndi mphamvu zawo. Iwo akugona osachita mdulidwe pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga ndipo akuchita manyazi pamodzi ndi iwo amene anatsikira kale ku manda.

31“Farao ndi gulu lake lankhondo akadzawaona iwowa adzathunza mtima pokumbukira kuchuluka kwa gulu lake lankhondo limene linaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 32Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. Koma Faraoyo pamodzi ndi ankhondo ake onse adzayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi amene anaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”