以西結書 24 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以西結書 24:1-27

鏽鍋的比喻

1第九年十月十日,耶和華對我說: 2「人子啊,今天是巴比倫王圍攻耶路撒冷的日子,你要記下這日子。 3你要向叛逆的以色列人說比喻,告訴他們,主耶和華這樣說,

『把鍋放在火上,

裡面倒進水,

4把羊腿、羊肩等上好的肉塊放進鍋裡,

讓鍋裡盛滿精選的骨頭。

5要從羊群中選一頭上好的羊,

把柴堆在鍋下,

燒開鍋煮裡面的骨頭。』」

6主耶和華說:「這像鏽鍋一樣充滿血腥的城有禍了!要把肉從這鏽跡斑斑的鍋中一塊塊地取出來。 7這城沾滿血腥,任憑受害者的血流在光禿禿的磐石上,而不是流在地上用土掩蓋。 8我任憑這城把受害者的血灑在磐石上,不加掩蓋,好激起我的烈怒,使她受報應。 9所以主耶和華說,『血腥的城啊,你有禍了!我要預備大堆木柴, 10添在火上,燃起旺火,把肉煮爛,加入香料,燒焦骨頭。 11然後,把倒空的鍋放在炭火上燒熱,把銅燒紅,好熔化它的雜質,除淨鏽垢, 12卻徒勞無功,因為鏽垢太厚,就是用火也不能清除。 13耶路撒冷啊,淫蕩使你污穢不堪,我要潔淨你,你卻不願被潔淨。所以,除非我向你傾盡一切憤怒,否則你的污穢將不能清除。 14我耶和華言出必行,決不寬容,也不留情,我必照你的所作所為來審判你。』這是主耶和華說的。」

15耶和華對我說: 16「人子啊,我要突然奪去你心愛的人,你不可悲傷,也不可流淚哭泣。 17你要默然哀歎,不可為死人辦喪事,仍要纏著頭巾,穿著鞋,不可蒙著臉,也不可吃喪家吃的飯。」 18早晨我把這事告訴百姓,晚上我的妻子便死了。次日早晨,我便遵照耶和華的吩咐行。

19百姓問我:「你可以告訴我們,你這樣做跟我們有什麼關係嗎?」 20我告訴他們:「耶和華對我說, 21『你告訴以色列人,我要使我的聖所,就是你們引以為傲、眼中所愛、心裡所慕的受到褻瀆。你們留下的兒女必死於刀下。 22那時,你們將像我的僕人一樣不蒙臉,不吃喪家吃的飯。 23你們仍將裹著頭巾,穿著鞋,不哭泣,也不悲傷。你們必因自己的罪惡而默然歎息,逐漸滅亡。 24以西結做的事都是你們的預兆,你們也將做他做的。當這事發生時,你們就知道我是主耶和華了。』

25「人子啊,有一天我要奪去他們所喜悅、所誇耀、眼中所愛、心裡所慕的堡壘,也要奪去他們的兒女。 26那日,倖存的人必來告訴你這個消息。 27那時,你必開口向那人說話,不再沉默。你必成為他們的預兆,他們就知道我是耶和華。」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 24:1-27

Mʼphika Wophikira

1Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi chaka chachisanu ndi chinayi, Yehova anandiyankhula kuti: 2“Iwe mwana wa munthu lemba dzina la tsiku lalero, lero lomwe lino, chifukwa mfumu ya Babuloni yazungulira Yerusalemu lero lino. 3Uwaphere mwambi anthu owukirawa ndi kuwawuza kuti: ‘Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Ikani mʼphika pa moto,

ndipo mu mʼphikamo muthiremo madzi.

4Mu mʼphikamo muyikemo nthuli za nyama,

nthuli zonse zabwino kwambiri za mwendo wathako ndi mwendo wamwamba.

Mudzadzemo mafupa abwino kwambiri.

5Pa gulu la nkhosa musankhepo nkhosa yabwino kwambiri.

Muyike nkhuni pansi pa mʼphikawo.

Madzi awire.

Kenaka muphike nyamayo pamodzi ndi mafupa omwe.’

6“ ‘Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova akuti,

“ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi,

tsoka kwa mʼphika wadzimbiri;

dzimbiri lake losachoka!

Mutulutsemo nthuli imodzimodzi

osasankhulapo.

7“ ‘Paja magazi amene anakhetsa akanali pakati pake mu mzindamo.

Iye awakhuthulira pa thanthwe losalala.

Sanawakhutulire pa dothi

kuopa kuti fumbi lingawafotsere.

8Ndinasiya magaziwo pa mwala wosalala

kuti asafotseredwe ndi fumbi

chifukwa ndinafuna kuonetsa mkwiyo wanga ndi kulipsira.

9“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:

“ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi!

Inenso, ndidzawunjika mulu waukulu wa nkhuni.

10Choncho wonjeza nkhuni

ndipo muyatse moto.

Phikani nyamayo bwinobwino,

muthiremo zokometsera,

mutsanule msuzi, ndipo mupsereze mafupawo.

11Tsono muyike pa makala mʼphika wopanda kanthuwo

mpaka utenthe kuchita kuti psuu

kuti zonyansa zake zisungunuke

ndi kuti dzimbiri lake lichoke.

12Koma mʼphikawo walephereka kuyeretsedwa.

Dzimbiri lake linalowerera silingatheke kuchoka

ngakhale ndi moto womwe.

13“ ‘Tsono dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako. Pakuti ine ndinayesa kukutsuka koma iwe sunayere, ndipo sudzayeranso mpaka ukali wanga utakwaniratu pa iwe.

14“ ‘Ine Yehova ndayankhula. Zimenezi zikubwera ndipo ndidzazichitadi. Sindidzabwerera mʼmbuyo. Sindidzakulekerera kapena kukuchitira chifundo. Ndidzakulanga molingana ndi makhalidwe ndi machitidwe ako, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Imfa ya Mkazi wa Ezekieli

15Yehova anandiyankhula kuti: 16“Iwe mwana wa munthu, Ine ndikulanda mwadzidzidzi mkazi amene amakukomera mʼmaso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi. 17Ubuwule koma mwakachetechete. Usamulire wakufayo. Uvale nduwira yako ndithu, nsapato zakonso usavule. Usaphimbe nkhope kapena kudya chakudya cha anamfedwa.”

18Choncho ndinayankhula ndi anthu mmawa, ndipo madzulo mkazi wanga anamwalira. Mmawa mwake ndinachita monga momwe anandilamulira.

19Ndipo anthu anandifunsa kuti, “Kodi sutifotokozera tanthauzo la zimene ukuchitazi?”

20Ndinawayankha kuti, “Yehova anandipatsa uthenga wakuti, 21‘Awuze Aisraeli kuti: Ine Ambuye Yehova ndikuti: ndidzayipitsa Nyumba yanga yopatulika, nyumba imene mwakhala mukuyinyadira. Mumakondwa kwambiri poyiona, ndipo mumayikonda ndi mtima onse. Ana aamuna ndi aakazi amene munawasiya mʼmbuyo adzaphedwa ndi lupanga. 22Ndipo mudzachita monga ndachitira inemu. Inu simudzaphimba nkhope zanu kapena kudya chakudya cha anamfedwa. 23Mudzavala nduwira zanu kumutu ndi nsapato zanu ku mapazi anu. Simudzabuma maliro kapena kukhetsa misozi koma mudzavutika kwambiri chifukwa cha machimo anu ndipo mudzabuwula pakati panu. 24Ine Ezekieli ndidzakhala chitsanzo chanu. Mudzachita monga momwe ndachitira. Izi zikadzachitika, akutero Yehova, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Wamphamvuzonse.’

25“Ndipo Yehova anandiyankhula nati: Iwe mwana wa munthu, tsiku lina ndidzawachotsera anthuwa linga lawo limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkawakomera mʼmaso mwawo, limenenso anayikapo mtima wawo kwambiri. Ndidzawachotsera ana awo aamuna ndi aakazi. 26Pa tsiku limenelo wothawa nkhondo adzabwera kudzakuwuzani zimenezo. 27Pa tsiku limenelo pakamwa pako padzatsekuka. Udzatha kuyankhula naye ndipo sudzakhalanso chete. Motero udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”