以西結書 23 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以西結書 23:1-49

兩個淫婦的比喻

1耶和華對我說: 2「人子啊,有一對同胞姊妹, 3她們在埃及做娼妓,年輕時就淫亂,任人撫摸她們的胸,玩弄她們的乳。 4姐姐名叫阿荷拉,妹妹名叫阿荷利巴。後來她們都歸屬了我,並且生兒育女。阿荷拉撒瑪利亞阿荷利巴耶路撒冷

5阿荷拉歸屬我後仍然淫亂,貪戀她的情人——亞述人。 6他們都是身穿紫衣的省長和總督,都是英俊的年輕騎士。 7她便與這些亞述的精英放縱情慾,拜他們的偶像,玷污自己。 8她沒有放棄在埃及的淫蕩行為,她年輕的時候就任人玩弄、發洩情慾。 9因此,我把她交在她所戀慕的亞述人手裡。 10他們扒光她的衣服,奪去她的兒女,用刀殺了她。她受了報應,成了婦女口中的笑柄。

11「她妹妹阿荷利巴看見這一切,不但沒有引以為戒,反而更加放蕩淫亂。 12她貪戀亞述的省長和總督,那些衣著華麗、英俊的年輕騎士。 13我看見她玷污了自己,與姐姐的行徑如出一轍。 14她還變本加厲地放蕩淫亂,看見牆上用朱砂畫著迦勒底人的像, 15腰間束帶,頭巾飄揚,都像是來自迦勒底巴比倫人的將領, 16便戀上了他們,差遣使者到他們那裡。 17巴比倫人便來上她的床,放縱情慾玷污了她。之後,她便厭棄他們。 18她繼續公開地淫亂,在眾人面前赤身露體,我厭棄她,像厭棄她姐姐一樣。 19她卻更加淫亂,懷念自己年輕時在埃及為娼的日子, 20怎樣與那些體壯精足、如驢似馬的情人縱淫, 21渴望重溫早年的淫行,任埃及人摸胸弄乳。

22「因此,主耶和華對阿荷利巴這樣說,『我要使那些被你離棄的情人從四面八方來攻擊你。 23他們是巴比倫人,還有從比割書亞哥亞來的迦勒底人以及亞述人,都是騎馬的省長和總督及年輕英俊的有名將領。 24他們率領大隊人馬,帶著兵器、戰車和軍需車來攻擊你。他們頂盔貫甲,手拿盾牌從四面八方進攻你。我要讓他們懲罰你,他們會按自己的律例來審判你。 25我要藉著他們向你傾倒我的義憤,他們要在憤怒中對付你,割去你的鼻子和耳朵,擄去你的兒女,城中剩下的人都要死於刀下,被火吞噬。 26他們要剝下你的衣服,奪去你的珠寶。 27我要藉此制止你從埃及染上的淫亂和放蕩,使你不再嚮往埃及28我要把你交在你所厭惡的人手中, 29他們必滿懷仇恨地對付你,奪去你努力得來的一切,留下你赤身露體,使你淫蕩的醜惡公佈於眾。 30因為你與各國苟合,被他們的偶像玷污,這些事必臨到你身上。 31你既然步你姐姐的後塵,我要讓你喝她喝的那杯。』

32「主耶和華說,

『你必喝你姐姐那又大又深的杯,

成為人們恥笑和辱罵的對象。

33你姐姐撒瑪利亞的杯盛滿了恐懼和淒涼。

你喝了後必酩酊大醉,

滿心憂愁。

34你必一滴不剩把它喝光,

然後把杯摔成碎片,

抓破自己的胸脯。

這是主耶和華說的。』

35「主耶和華說,『你既忘記我,把我拋在腦後,就要受自己放蕩淫亂的報應。』」

36耶和華又對我說:「人子啊,你要審判阿荷拉阿荷利巴,指出她們的醜行。 37她們淫蕩,手上沾滿血腥,與偶像淫亂,把為我所生的兒女燒死獻給偶像。 38同時,她們還在同一天玷污我的聖所,褻瀆我的安息日, 39她們焚燒自己的兒女獻祭給偶像,並在當天進入我的聖所,褻瀆聖所。這就是她們在我聖所裡的惡行。

40「她們甚至派使者請來遠方的人,並且沐浴洗身,描眉畫眼,佩戴首飾, 41坐在華麗的床上,面前的桌子上擺設著我的香料和膏油。 42她們屋裡傳出眾人的安樂聲,從曠野來的酒徒和粗漢把鐲子戴在這對姊妹的手腕上,把華冠戴在她們的頭上。 43我說,『她們縱慾無度、年老色衰,這些人還與她們淫亂。 44他們與這對淫婦阿荷拉阿荷利巴淫亂,好像與娼妓淫亂一樣。 45她們是雙手沾滿血腥的淫婦,必有義人按她們應得的報應審判她們。』

46「主耶和華說,『我要使許多人起來攻擊、搶掠她們,叫她們膽戰心驚。 47這些人要用石頭打死她們,用刀殺戮她們和她們的兒女,用火燒毀她們的房屋。 48這樣,我便制止了這地方的淫亂,所有的婦女都引以為戒,不敢效法她們。 49她們淫亂,必得報應;她們拜偶像,必受懲罰。這樣,你們就知道我是主耶和華。』」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 23:1-49

Za Yerusalemu ndi Samariya

1Yehova anandiyankhula nati: 2“Iwe mwana wa munthu, panali atsikana awiri ana a mayi mmodzi. 3Iwo ankachita za chiwerewere ku Igupto. Za chiwerewerezo anayamba ali achichepere. Kumeneko anthu ankangowasisita pa chifuwa ndi kuwagwiragwira mawere awo aja. 4Wamkulu dzina lake anali Ohola, ndipo mngʼono wakeyo anali Oholiba. Ine ndinawakwatira ndipo anabereka ana aamuna ndi ana aakazi. Ohola ndiye Samariya, ndipo Yerusalemu ndiye Oholiba.

5“Ohola anachita zachiwerewere ngakhale anali mkazi wanga; ndipo iye anakangamira abwenzi ake a ku Asiriya. 6Amenewo anali asilikali ovala zibakuwa zamlangali, abwanamkubwa ndiponso atsogoleri a nkhondo. Onsewo anali anyamata osiririka ndipo ankakwera pa akavalo. 7Ohola anachita zachiwerewere ndi onsewa, anthu otchuka a ku Asiriya. Iye anadziyipitsa ndi mafano a munthu aliyense amene anagona naye. 8Iye sanaleke za chiwerewere zimene anaziphunzira ku Igupto. Paja akanali mtsikana anyamata ankagona naye. Iwo ankamusisita mawere akanali anthete nachita naye zachiwerewere.

9“Nʼchifukwa chake Ine ndinamupereka kwa achikondi ake, Asiriya, amene iye ankawalakalaka. 10Iwowa anamuvula, namulanda ana ake aamuna ndi aakazi ndipo anamupha ndi lupanga. Ndipo atalangidwa choncho, iye anasanduka chinthu chonyozeka pakati pa akazi.

11“Mphwake Oholiba anaona zimenezi natengerako. Koma iye anachita zachiwerewere kuposa mkulu wake. 12Iyenso anakangamira Asiriya, abwanamkubwa, olamulira asilikali, ankhondo ovala zovala zonse za nkhondo ndi okwera pa akavalo. Onsewa anali anyamata osiririka. 13Ndinaona kuti iyenso anadziyipitsa; ndipo onse awiriwo anatsata njira imodzi.

14“Koma Oholiba uja anachita chigololo kopitirira mkulu wake. Iye anaona zithunzi za amuna pa khoma, zithunzi za Ababuloni zolembedwa ndi inki yofiira, 15atamanga malamba mʼchiwuno mwawo ndi kuvala nduwira pa mitu yawo. Onse amaoneka ngati atsogoleri a magaleta a Ababuloni, mbadwa za ku Kaldeya. 16Oholiba atangowaona, anawalakalaka ndipo anatuma amithenga ku Kaldeya kukawayitana. 17Ndipo Ababuloni anabwera nʼkudzagona naye. Choncho mwa chilakolako chawo anamuyipitsa. Koma atamuyipitsa choncho, iye ananyansidwa nawo. 18Iye atachita chiwerewere chake poyera ndi kuonetsa umaliseche wake, Ine ndinamuchokera monyansidwa monga mmene ndinachitira ndi mʼbale wake. 19Koma anachitabe zachiwerewere osalekeza. Ankakumbukira masiku a ubwana wake pamene ankachita za chiwerewere mʼdziko la Igupto. 20Kumeneko iye ankalakalaka zibwenzi zake, amene ziwalo zawo zinali ngati za abulu ndipo kutentha kwawo kunali ngati kwa akavalo. 21Motero, iwe Oholiba unafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Igupto pamene unali mtsikana. Nthawi imene ija ankakusisita pa chifuwa ndi kugwiragwira mawere ako osagwa aja.

22“Tsono iwe Oholiba, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakudzutsira zibwenzi zako zimene unkanyansidwa nazo zija kuti zilimbane nawe. Ndidzaziyitana kuti zibwere kuchokera mbali zonse. 23Ndidzayitana anthu a ku Babuloni ndi Akaldeya onse, anthu a ku Pekodi, Sowa ndi Kowa pamodzi ndi Asiriya onse. Onsewa ndi amuna osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri a ankhondo, oyenda pa magaleta, anthu a maudindo akuluakulu. Onsewa ndi okwera akavalo. 24Iwo adzabwera kudzalimbana nawe ndi zida za nkhondo, magaleta ndi ngolo, pamodzi ndi anthu ambiri. Adzakuzinga mbali zonse atavala zishango zankhondo ndi zipewa zankhondo. Ndidzakupereka kwa iwo kuti akulange ndipo adzakulanga monga momwe adzafunire. 25Ndidzaonetsa mkwiyo wanga pa iwe ndipo iwo adzakulanga iwe mwankhanza. Adzadula mphuno zanu ndi makutu anu, ndipo amene adzatsalira mwa iwe adzaphedwa ndi lupanga. Iwo adzakulanda ana ako aamuna ndi aakazi ndipo amene adzatsalira adzaphedwa ndi moto. 26Adzakuvulaninso zovala zanu ndikukulandani zodzikongoletsera zanu zamtengowapatali. 27Motero ndidzathetsa zonyansa zako ndi zachigololo zomwe unaziyamba ku Igupto. Choncho sudzalakalaka za ku Igupto kapena kuzikumbukiranso.

28“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikukupereka mʼmanja mwa amene amadana nawe, kwa iwo amene unawafulatira moyipidwa nawo. 29Adzachita nawe mwachidani. Adzakulanda zonse zimene unagwirira ntchito. Adzakusiya wamaliseche ndiponso wausiwa. Kuyipa kwa makhalidwe ako achiwerewere kudzakhala pammbalambanda. Zonyansa zako ndi chiwerewere chako, 30zabweretsa izi pa iwe chifukwa unachita zonyansa ndi anthu a mitundu ndi kudziyipitsa ndi mafano awo. 31Unatsata zochita za mkulu wako; choncho Ine ndidzayika chikho cha chilango chake mʼdzanja lako.

32“Ine Ambuye Yehova ndikuti:

“Udzamwera chikho cha mkulu wako,

chikho chachikulu ndi chakuya;

anthu adzakuseka ndi kukunyoza,

pakuti chikhocho ndi chodzaza kwambiri.

33Udzaledzera ndipo mtima wako udzadzaza ndi chisoni.

Chimenechi ndi chikho chachiwonongeko ndi chipasupasu,

chikho cha mkulu wako Samariya.

34Udzamwa chikhocho mpaka kugugudiza.

Tsono udzaphwanyaphwanya chikhocho

ndipo udzangʼamba mawere ako ndi zigoba zake.

Ine ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.

35“Chifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza wandiyiwala Ine ndi kundifulatira, chomwecho uyenera kulangidwa chifukwa cha zonyansa zako ndi chiwerewere chako.”

36Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Tsono uwayimbe mlandu chifukwa cha machitidwe awo onyansa. 37Iwo achita chigololo ndipo anapha anthu. Anachita chigololo popembedza mafano awo. Ngakhale ana amene anandiberekera Ine anawapereka kwa mafanowo ngati chakudya chawo. 38Anachitanso izi: Iwo anayipitsa malo anga opatulika ndi kudetsa masabata anga. 39Atapereka ana awo kwa mafano, tsiku lomwelo anakalowanso mʼNyumba yanga yopatulika ndi kuyipitsamo. Izi ndi zimene anachita mʼNyumba mwanga.

40“Iwo anatuma amithenga kukayitana amuna a ku mayiko akutali. Anthuwo atabwera, abale awiri aja anasambasamba, kudzola utoto wodzikometsera kumaso, kenaka ndi kuvala zovala zamakaka. 41Anakhala pa bedi lokongola ndipo patsogolo pawo panali tebulo pamene munayikapo lubani ndi mafuta. Zonse zowapatsa Ine.

42“Mfuwu wa chigulu cha anthu unamveka. Anthu oledzera ochokera ku chipululu anabwera pamodzi ndi anthu wamba ndipo anaveka akaziwo zibangiri kumanja ndi zipewa zaufumu zokongola ku mutu. 43Ndipo ine ndinati za mkazi wotheratu ndi chigololoyo, ‘Tsono asiyeni kuti achite naye monga wachiwerewere, pakuti ichi ndi chimene iye ali basi.’ 44Tsono anapita kwa iwo monga mmene anthu amapitira kwa mkazi wadama. Momwemo anapita kwa Ohola ndi kwa Oholiba kukachita nawo zadama. 45Koma anthu olungama adzawazenga anthuwa mlandu wa chigololo ndi wa kupha anthu. Ndi iwodi anthu achigololo ndiponso mʼmanja mwawo muli magazi.

46“Ambuye Yehova akuti: Itanitsani chigulu cha anthu kuti chidzawalange ndi kulanda chuma chawo. 47Anthuwo adzawaponye miyala akazi awiriwo ndi kuwatema ndi malupanga awo. Ana awo aamuna ndi aakazi adzawaphe ndi kutentha nyumba zawo.

48“Motero Ine ndidzathetsa zachigololo mʼdzikomo, ndipo akazi onse adzatengapo phunziro kuti asadzachite zachigololo monga za iwowo. 49Ndidzawalanga chifukwa cha ntchito zawo za dama ndipo adzazunzika chifukwa cha tchimo lawo lopembedza mafano. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.”