以西結書 17 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以西結書 17:1-24

鷹和葡萄樹的比喻

1耶和華對我說: 2「人子啊,你要向以色列人出謎語,講比喻, 3告訴他們,主耶和華說,『有一隻大鷹翅膀寬大,羽毛豐滿,色彩繽紛。這隻鷹飛到黎巴嫩的香柏樹上,折去樹梢, 4叼到一個商賈雲集的城市,栽在那裡。 5牠又把以色列的樹苗像柳樹一樣栽在水源豐沛的沃土裡。 6樹苗很快發了芽,成了向四面蔓延的矮小葡萄樹,根深葉茂,枝子向著鷹伸展開去。

7「『又有一隻大鷹飛來,翅膀寬大,羽毛豐滿。這葡萄樹把根和枝子轉向這隻鷹,渴望得到牠的澆灌。 8但這樹已栽在水源豐沛的沃土裡,可以長得枝繁葉茂,成為結實纍纍的好葡萄樹。』

9「你要告訴他們,主耶和華這樣說,『這樹能長得枝繁葉茂嗎?難道那鷹不把它連根拔起,摘掉它的果子,使樹和嫩葉全部枯萎嗎?不必費多大力氣,也不需要多少人就可以把它連根拔起。 10這樹雖然被栽種了,又豈能長得茂盛呢?東風一吹,它豈不完全枯萎在園圃中了嗎?』」

11耶和華對我說: 12「你要對這些悖逆的人說,『你們不明白這比喻的意思嗎?』要告訴他們,巴比倫王攻取了耶路撒冷,把其中的君王和大臣擄到巴比倫13並從猶大王室中選出一人與他立約,要他效忠。巴比倫王擄去猶大國的重臣, 14使猶大國臣服於他,無法圖強,只能遵守盟約,以求生存。 15後來,猶大王背叛了巴比倫王,派使者到埃及請求支援軍隊馬匹。他能成功嗎?他這樣做怎能逃脫懲罰呢?他這樣背約怎能逃脫懲罰呢?

16「我憑我的永恆起誓,巴比倫王立他做王,他卻棄約背誓,他必死在巴比倫17敵人築起圍攻的土壘和高臺大肆殺戮的時候,法老雖然兵強馬壯,人多勢眾,仍無法幫他抗敵。 18他起誓降服,卻棄約背誓,所以絕不能逃避後果。 19因此,主耶和華說,『我憑我的永恆起誓,他既藐視與我所立的誓言,背棄與我所定的約,我必懲罰他。 20我要撒開網羅抓住他,把他帶到巴比倫,審判他對我不忠的罪。 21他所有的精兵都要喪身刀下,餘下的也要四散逃竄。這樣,你們就知道這是我耶和華說的。

22「主耶和華說,『我要從高大的香柏樹梢折下一根嫩枝,種植在以色列巍峨的高山上。 23它會生枝結果,成為一棵美麗的香柏樹,各類飛鳥都要棲息在它的樹枝上。 24田野所有的樹都會知道我耶和華使高樹倒下、矮樹長高、青樹枯萎、枯樹發榮。我耶和華言出必行。』」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 17:1-24

Fanizo la Ziwombankhanga Ziwiri ndi Mtengo Wamphesa

1Yehova anayankhula nane kuti, 2“Iwe mwana wa munthu, aphere mwambi anthu a Israeli ndi kuwawuza fanizo. 3Uwawuze kuti Ambuye Yehova akuti, chiwombankhanga chachikulu, cha mapiko amphamvu, nthenga zitalizitali zamathothomathotho chinabwera ku Lebanoni. Chinagwira nthambi ya pamwamba pa mtengo wa mkungudza. 4Chinabudula msonga yeniyeni ya nthambiyo nʼkupita nayo ku dziko lamalonda ndipo anakayika mu mzinda wa anthu amalonda.

5“ ‘Kenaka chinatenga mbewu ina ya mʼdziko ndi kukayidzala ku malo a chonde kumene kunali madzi ambiri. Anayidzala ngati mmene amadzalira mtengo wa msondozi. 6Ndipo inaphuka nisanduka mtengo wa mpesa wotambalala chamʼmunsi. Nthambi zake zinaloza mmwamba kumene kunali chiwombankhangacho, koma mizu yake inalowa pansi. Kotero unakhala mtengo wamphesa ndipo unasanduka wa nthambi ndiponso wa masamba ambiri.

7“ ‘Koma panali chiwombankhanga chinanso chachikulu, cha mapiko amphamvu ndi cha nthenga zambiri. Tsopano mtengo wamphesa uja unakhotetsera mizu yake kwa chiwombankhangacho kuchokera pa malo amene unadzalidwa ndipo unatambalitsa nthambi zake kwa chiwombankhangacho kufuna kuthiridwa madzi. 8Koma mtengowo unadzalidwa kale pa nthaka yabwino mʼmbali mwa madzi kuti ukhale ndi nthambi zambiri, ubereke zipatso ndi kukhala wokongola.’

9“Ukawawuze Aisraeli kuti, ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Kodi udzakula bwino? Kodi chiwombankhanga chija sichidzawuzula mizu ndi kubudula nthambi zake kuti ufote? Masamba ake onse anthete adzafota. Sipadzafunika dzanja lamphamvu kapena anthu ambiri kuti awuzule. 10Ngakhale utawokedwa pena, kodi udzaphuka? Kodi sudzafoteratu mphepo ya kummawa ikadzawomba, kufotera pa malo pamene anawuwokerapo?’ ”

11Kenaka Yehova anandiyankhula nati: 12“Tawafunsa anthu owukirawa kuti, ‘kodi mukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?’ Uwafotokozere kuti, ‘Mfumu ya Babuloni inapita ku Yerusalemu ndikukatengako mfumu ndi anthu ake otchuka ndi kubwera nawo ku Babuloni. 13Ndipo anatenga mmodzi wa banja laufumu ndi kuchita naye mgwirizano, ndipo anamulumbiritsa kuti akhale womvera. Inatenganso akulu onse a mʼdzikomo 14kuti ufumu wa dzikolo utsitsidwe, usadzaphukenso, koma kuti ukhalepobe posunga pangano limene unachita. 15Koma mfumu inawukira mfumu ya ku Babuloni potumiza nthumwi ku dziko la Igupto kukatenga akavalo ndi gulu lalikulu la nkhondo. Kodi mfumu yotereyi ingapambane? Kodi wochita zinthu zoterezi angapulumuke? Kodi angaphwanye mgwirizano ndi kupulumuka?

16“ ‘Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, mfumuyo idzafera ku Babuloni, mʼdziko la mfumu imene inayika pa mpando waufumu. Inapeputsa lumbiro lake nʼkuphwanya pangano limene inachita ndi mfumu inayo. 17Farao ndi gulu lake lankhondo lamphamvu sadzatha kumuthandiza pa nkhondo, pamene mfumu ya Babuloni idzapanga mitumbira ya nkhondo ndi nsanja za nkhondo kuti iwononge miyoyo yambiri. 18Mfumu ya ku Yuda inanyoza lumbiro lake pophwanya pangano. Inalonjeza komabe sinatsatire malonjezo ake. Choncho sidzapulumuka.

19“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndithu pali Ine wamoyo, Ine ndidzalanga mfumu imeneyi chifukwa inanyoza lumbiro langa, ndi kuphwanya pangano langa. 20Ndidzayitchera ukonde ndipo idzakodwa mu msampha wanga. Ndidzapita nayo ku Babuloni ndi kuyilanga kumeneko chifukwa inali yosakhulupirika kwa Ine. 21Asilikali ake onse amene akuthawa adzaphedwa ndi lupanga, ndipo opulumuka adzabalalitsidwa ku mbali zonse. Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova ndayankhula.

22“ ‘Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndidzatenga nthambi pamwamba penipeni pa mkungudza ndi kuyidzala; ndidzathyola nthambi yanthete kuchokera pa nthambi zapamwamba penipeni ndi kuyidzala pamwamba pa phiri lalitali. 23Ndidzayidzaladi pa phiri lalitali la Israeli. Idzaphuka nthambi ndi kubereka zipatso. Choncho idzasanduka mkungudza wamphamvu. Mbalame za mtundu uliwonse zidzamanga zisa zawo mʼmenemo; zidzapeza malo okhala mu mthunzi wa nthambi zake. 24Mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine ndine Yehova amene ndimafupikitsa mitengo yayitali ndi kutalikitsa mitengo yayifupi. Ndimawumitsa mitengo yabiriwiri ndi kubiriwitsa mitengo yowuma.

“ ‘Ine Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichita.’ ”