马太福音 15 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

马太福音 15:1-39

传统与诫命

1有几个法利赛人和律法教师从耶路撒冷来质问耶稣: 2“为什么你的门徒吃饭前不行洗手礼,破坏祖先的传统呢?”

3耶稣回答说:“为什么你们拘守传统而违背上帝的诫命呢? 4上帝说,‘要孝敬父母’,又说,‘咒骂父母的,必被处死。’ 5你们却说,‘人如果把供养父母的钱奉献给上帝, 6他就不必供养父母。’你们这是用传统来废掉上帝的诫命。 7你们这些伪君子,以赛亚指着你们说的预言一点不错,

8“‘这些人嘴上尊崇我,

心却远离我,

9他们的教导无非是人的规条,

他们敬拜我也是枉然。’”

10耶稣召集了众人,对他们说:“你们要听,也要明白。 11入口的东西不会使人污秽,从口中出来的才会使人污秽。”

12门徒上前对祂说:“你知道吗?法利赛人听见你的话很反感。”

13耶稣回答说:“凡不是我天父栽种的都要被连根拔起来。 14随便他们吧!他们是瞎眼的向导。瞎子给瞎子领路,二人都会掉进坑里。”

15彼得对耶稣说:“请给我们解释一下这个比喻。”

16耶稣说:“你们还不明白吗? 17岂不知入口的东西都是进到肚子里,然后排泄到厕所里吗? 18可是,从口中出来的乃是发自内心,会使人污秽。 19因为从心里出来的有恶念、谋杀、通奸、淫乱、偷盗、假见证和毁谤, 20这些东西才使人污秽。不洗手吃饭并不会使人污秽。”

迦南妇人的信心

21耶稣从那里退到泰尔西顿境内。 22那地方有个迦南的妇人前来大声恳求耶稣:“主啊!大卫的后裔啊!可怜我吧!我的女儿被鬼附身,受尽折磨!” 23耶稣却一言不发。门徒上前求祂说:“请让她走吧!她老是在后面喊叫。”

24耶稣说:“我奉差遣只是来寻找以色列家迷失的羊。”

25那妇人上前跪下,说:“主啊!求你帮帮我吧!”

26耶稣答道:“把儿女的食物丢给狗吃,不合适。”

27妇人说:“主啊,不错,可是狗也吃主人饭桌上掉下来的碎渣呀!”

28耶稣说:“妇人,你的信心真大!我答应你的要求。”就在那一刻,她女儿就好了。

耶稣使四千人吃饱

29耶稣离开那里,来到加利利湖边,上了山,在那里坐下。 30大群的人把瘸子、瞎子、残疾的、哑巴及许多别的病人带来,放在祂脚前,祂就治好了他们。 31大家看见哑巴说话,残疾的复原,瘸子走路,瞎子看见,都很惊奇,就赞美以色列的上帝。

32耶稣把门徒召集过来,对他们说:“我怜悯这些人,他们跟我在一起已经三天,没有任何吃的。我不愿让他们饿着肚子回去,以免他们在路上体力不支。”

33门徒说:“在这荒野,我们到哪里找足够的食物给这么多人吃呢?”

34耶稣问:“你们有多少饼?”

门徒答道:“七个,还有几条小鱼。”

35耶稣便吩咐大家坐在地上。 36祂拿着那七个饼和几条鱼祝谢后,掰开,递给门徒,门徒再分给大家。 37大家都吃了,并且吃饱了,剩下的零碎装满了七个筐子。 38当时吃饭的,除了妇女和小孩,共有四千男人。 39随后,耶稣叫众人散去,自己坐船去了马加丹地区。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 15:1-39

Miyambo ya Makolo

1Pamenepo Afarisi ena ndi aphunzitsi amalamulo anabwera kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu ndipo anamufunsa kuti, 2“Chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya mwambo wa akuluakulu? Iwo sasamba mʼmanja pakudya!”

3Yesu anayankha kuti, “Nanga chifukwa chiyani inu mumaphwanya lamulo la Mulungu chifukwa cha mwambo wa makolo anu? 4Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ 5Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’ 6iye sakulemekeza nayo abambo ake ndipo ndi khalidwe lotere inu mumapeputsa nalo Mawu a Mulungu chifukwa cha mwambo wanu. 7Inu anthu achiphamaso, Yesaya ananenera za inu kuti,

8“ ‘Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo,

koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.

9Amandilambira Ine kwachabe

ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’ ”

10Yesu anayitana gulu la anthu nati, “Mverani ndipo zindikirani. 11Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu sichimuchititsa kukhala woyipa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake, icho ndi chimene chimamuchititsa kukhala woyipa.”

12Pamenepo ophunzira anabwera kwa Iye ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti Afarisi anakhumudwa pamene anamva mawu aja?”

13Iye anayankha kuti, “Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe. 14Alekeni, ndi atsogoleri osaona. Ngati munthu wosaona atsogolera wosaona mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”

15Petro anati, “Timasulireni fanizoli.”

16Yesu anawafunsa kuti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa? 17Kodi inu simudziwa kuti chilichonse cholowa mʼkamwa chimapita mʼmimba ndipo kenaka chimatuluka kunja kwa thupi? 18Koma zinthu zimene zituluka mʼkamwa zimachokera mu mtima ndipo zimenezi zimamuchititsa munthu kukhala woyipa. 19Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe. 20Izi ndi zimene zimachititsa munthu kukhala woyipa; koma kudya ndi mʼmanja mosasamba sikumuchititsa munthu kukhala woyipa.”

Mayi wa ku Kanaani

21Yesu atachoka kumalo amenewo anapita kudera la ku Turo ndi ku Sidoni. 22Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.”

23Yesu sanayankhe kanthu. Ndipo ophunzira ake anabwera namupempha Iye kuti, “Muwuzeni achoke chifukwa akulira mofuwula pambuyo pathu.”

24Iye anayankha kuti, “Ine ndinatumidwa kwa nkhosa zotayika za Israeli zokha.”

25Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, “Ambuye ndithandizeni!”

26Iye anayankha kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu.”

27Mayiyo anati, “Inde Ambuye. Komatu ngakhale agalu amadya nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pa tebulo la mbuye wawo.”

28Pomwepo Yesu anayankha kuti, “Mayi iwe uli ndi chikhulupiriro chachikulu! Pempho lako lamveka.” Ndipo mwana wake wamkazi anachira nthawi yomweyo.

Yesu Adyetsa Anthu 4,000

29Yesu anachoka kumeneko napita mʼmbali mwa nyanja ya Galileya. Ndipo anakwera ku phiri nakhala pansi. 30Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye ndi anthu olumala, osaona, ofa ziwalo, osayankhula ndi ena ambiri nawagoneka pa mapazi ake ndipo Iye anawachiritsa. 31Anthu ataona osayankhula akuyankhula, ofa ziwalo akuchira, olumala miyendo akuyenda ndi osaona akuona anadabwa kwambiri. Ndipo analemekeza Mulungu wa Israeli.

32Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala kale ndi Ine masiku atatu ndipo alibe chakudya. Ine sindifuna kuti apite kwawo ndi njala chifukwa angakomoke pa njira.”

33Ophunzira anayankha kuti, “Ndikuti kumene tingakapeze buledi mʼtchire muno okwanira kudyetsa gulu lotere?”

34Yesu anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?”

Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri ndi tinsomba pangʼono.”

35Iye anawuza gululo kuti likhale pansi. 36Kenaka anatenga malofu asanu ndi awiri aja ndi tinsombato ndipo atayamika anagawa napatsa ophunzira ake ndipo iwo anagawira anthuwo. 37Onse anadya ndipo anakhuta. Pomaliza ophunzira anatolera zotsalira nadzaza madengu asanu ndi awiri. 38Chiwerengero cha anthu amene anadya chinali 4,000 kupatula amayi ndi ana. 39Yesu atatha kuwuza gululo kuti lipite kwawo, analowa mʼbwato ndipo anapita kudera la Magadala.