马可福音 5 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

马可福音 5:1-43

治好被鬼附身的人

1他们来到湖对岸的格拉森地区。 2耶稣刚下船,就遇见一个被污鬼附身的人从坟场迎面而来。 3那人以坟场为家,从来没有人能把他捆住,就算用铁链也锁不住他。 4尽管有人多次用铁链和脚镣锁住他,但他挣断了铁链,砸碎了脚镣。没有人能制服他。 5他昼夜在坟场和山野间大喊大叫,又用石头砍自己。

6他远远看见耶稣,就跑过去跪下来拜祂,喊着说: 7“至高上帝的儿子耶稣啊,我和你有什么关系?看在上帝的份上,求你不要折磨我!” 8原来,耶稣已经对他身上的鬼说:“污鬼,从这人身上出来!”

9耶稣问:“你叫什么名字?”

他说:“我的名字叫‘群’,因为我们是一大群。”

10接着污鬼再三哀求耶稣,不要把它们逐出那个地区。 11当时有一大群猪在附近山坡上觅食。 12污鬼就哀求耶稣说:“让我们到猪群里去,附在它们身上吧!”

13耶稣允许了,污鬼就离开那人,进入猪群。那群猪就一路奔下陡坡,冲进湖里淹死了,约有两千头。

14放猪的人都吓跑了。他们把这消息传遍了城里乡间,于是人人都跑来看个究竟。 15他们到了耶稣那里,看见那一度被群鬼附身的人神智清醒、衣着整齐地坐在那里,都很害怕。 16目睹这件事的人向他们讲述整个经过。 17他们请耶稣离开他们的地方。

18耶稣上了船准备离开的时候,那被鬼附过的人恳求耶稣让他随行。 19耶稣没有答应,只对他说:“回去见你的家人,将主为你所做的事和祂怜悯你的经过告诉他们吧!”

20这人就回到低加坡里一带宣扬耶稣为他所行的奇事,大家都很惊奇。

耶稣医治有信心的人

21耶稣再坐船回到对岸,立刻有一大群人在岸边围着祂。 22人群中有一位会堂的主管名叫雅鲁,他一见到耶稣便俯伏在祂脚前, 23恳求说:“我小女儿快要死了,求你去把手按在她身上,医治她,救她一命。”

24耶稣和他同去,一大群人跟着祂,拥挤着祂。

25有一个妇人患血漏病已经十二年, 26经过许多医生的诊治,受尽痛苦,耗尽钱财,病情仍没有好转,反而更加严重。 27她听见耶稣的事,就夹在人群中挤到耶稣背后摸祂的衣服, 28心想:“只要摸到祂的衣服,我就痊愈了!”

29她的血漏立刻停止了,她感到自己痊愈了。 30耶稣马上知道有能力从自己身上发出,便在人群中转过身来问:“谁摸了我的衣服?”

31门徒对祂说:“你看,这么多人在你周围挤来挤去,你怎么问谁摸你呢?”

32耶稣环视四周,要找出摸祂的人。 33那妇人害怕得发抖,她知道在自己身上发生了什么事,于是上前俯伏在耶稣面前,将实情说了出来。

34耶稣说:“女儿,你的信心救了你。安心地回去吧!你的病好了。”

35耶稣还在说话的时候,有人从雅鲁家中赶来,对雅鲁说:“你的女儿已经死了,何必麻烦老师呢?”

36耶稣听了,便对雅鲁说:“不要怕,只要信。” 37于是,祂带着彼得雅各雅各的弟弟约翰雅鲁家,不准其他人跟着。 38他们到了那里,只见在场的人嚎啕大哭,场面混乱。 39耶稣进去问道:“你们为什么大哭大嚷呢?这孩子并没有死,只是睡着了。”

40这些人听了,都讥笑祂。耶稣让他们全部出去,然后带着孩子的父母和三个门徒进了房间。 41祂拉着孩子的手说:“大利大,古米!”意思是:“小女孩,我吩咐你起来!”

42小女孩应声而起,并且可以走动,那时她十二岁。在场的人都惊奇不已。 43耶稣郑重叮嘱他们不要把这事张扬出去,又吩咐他们给女孩东西吃。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 5:1-43

Yesu Achiritsa Wogwidwa ndi Ziwanda

1Ndipo anawoloka nyanja napita ku dera la Gerasa. 2Yesu atatuluka mʼbwato, munthu amene anali ndi mzimu woyipa anachoka ku manda ndi kukumana naye. 3Munthuyu amakhala ku manda, ndipo panalibe amene akanatha kumumanganso ngakhale ndi unyolo. 4Pakuti nthawi zambiri akamumanga manja ndi miyendo amadula maunyolo ndi kudula zitsulo zimene zinali mʼmapazi ake. Panalibe amene anali ndi mphamvu yoti ndi kumugonjetsa. 5Usana ndi usiku ankakhala ku manda ndi kumapiri, akulira ndi kudzicheka ndi miyala.

6Ataona Yesu ali patali, anathamanga nagwa pa mawondo ake pamaso pake. 7Iye anafuwula kwambiri nati, “Mukufuna muchite nane chiyani, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Lumbirani kwa Mulungu kuti simundizunza!” 8Pakuti Yesu anati kwa iye, “Tuluka mwa munthuyu, iwe mzimu woyipa!”

9Ndipo Yesu anamufunsa iye, “Dzina lako ndani?”

Iye anayankha kuti, “Dzina langa ndine Legiyo, pakuti tilipo ambiri.” 10Ndipo anamupempha Yesu mobwerezabwereza kuti asazitulutse mʼderalo.

11Gulu lalikulu la nkhumba limadya mʼmbali mwa phiri limene linali pafupi. 12Ziwandazo zinapempha Yesu kuti, “Titumizeni pakati pa nkhumbazo; ndipo mutilole tilowe mwa izo.” 13Iye anazipatsa chilolezo, ndipo mizimu yoyipayo inatuluka ndi kukalowa mu nkhumbazo. Gulu la nkhumba, zokwana pafupifupi 2,000 zinathamanga kutsetserekera ku nyanja ndipo zinamira.

14Omwe amaweta nkhumbazo anathawa ndi kukawuza anthu za izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi, ndipo anthu anapita kukaona zomwe zinachitika. 15Atafika kwa Yesu, anaona munthu amene anagwidwa ndi ziwanda zambiri uja atakhala pansi pomwepo, atavala, ndipo ali bwinobwino. Iwo anachita mantha. 16Amene anaona zimenezi anawuza anthu zomwe zinachitika kwa munthu wogwidwa ndi ziwandayo ndipo anawawuzanso za nkhumbazo. 17Ndipo anthu anayamba kumupempha Yesu kuti achoke mʼdera lawo.

18Yesu akulowa mʼbwato, munthu amene anagwidwa ndi ziwanda uja anamupempha kuti apite nawo. 19Yesu sanamulole, koma anati, “Pita kwanu ku banja lako ndipo ukawawuze zimene Ambuye wakuchitira, ndi chifundo chimene wakuchitira.” 20Pomwepo munthuyo anapita nayamba kuwuza anthu a ku Dekapoli zinthu zimene Yesu anamuchitira. Ndipo anthu onse anadabwa.

Mtsikana Womwalira ndi Mayi Wodwala

21Yesu atawolokeranso pa bwato kupita mbali ina ya nyanja, gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira. Ali mʼmbali mwa nyanja, 22mmodzi wa akulu a mʼsunagoge, dzina lake Yairo anafika pamenepo. Ataona Yesu, anagwa pa mapazi ake, 23ndi kumudandaulira kwambiri nati, “Mwana wanga wamkazi wamngʼono ali pafupi kufa. Chonde tiyeni kuti mukamusanjike manja kuti akachiritsidwe nakhala ndi moyo.” 24Ndipo Yesu anapita naye.

Gulu lalikulu la anthu linamutsata ndi kumamupanikiza Iye. 25Pomwepo panali mayi amene amadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri. 26Iye anavutika kwambiri pamene asingʼanga ambiri ankamusamalira ndipo anagwiritsa ntchito zonse anali nazo, koma mʼmalo mochira, nthenda yake inkakulakulabe. 27Atamva za Yesu, anabwera kumbuyo kwake mʼgulu la anthu ndipo anakhudza mkanjo wake, 28chifukwa anaganiza kuti, “Ngati nditangokhudza mkanjo wake, ndidzachiritsidwa.” 29Nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka ndipo anamva mʼthupi mwake kuti wamasulidwa ku vuto lake.

30Pomwepo Yesu anazindikira kuti mphamvu inachoka mʼthupi mwake. Anatembenuka mʼgulu la anthu ndipo anafunsa kuti, “Ndani wakhudza zovala zanga?”

31Ophunzira ake anayankha kuti, “Mukuona kuti anthu akukupanikizani, ndipo Inu mukufunsa kuti, ‘Ndani wandikhudza?’ ”

32Koma Yesu anapitirizabe kuyangʼana kuti aone amene anachita zimenezi. 33Kenaka mayi uja pozindikira chimene chinamuchitikira, anabwera ndi kugwa pa mapazi ake, ndipo akunjenjemera ndi mantha, anamuwuza zoona zokhazokha. 34Anati kwa iye, “Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere ndipo khala womasulidwa ku mavuto ako.”

35Pamene Yesu ankayankhulabe, amuna ena anafika kuchokera ku nyumba ya Yairo, mkulu wa sunagoge. Iwo anati, “Mwana wanu wamkazi wamwalira, muvutitsiranjinso aphunzitsiwa?”

36Posasamala zomwe ananena, Yesu anamuwuza mkulu wa sunagoge uja kuti, “Usachite mantha; ingokhulupirira.”

37Iye sanalole munthu wina aliyense kuti amutsatire koma Petro, Yakobo ndi Yohane mʼbale wa Yakobo. 38Atafika ku nyumba ya mkulu wa sunagoge, Yesu anaona chipiringu cha anthu akulira ndi kufuwula kwambiri. 39Analowa nati kwa iwo, “Mukuchita phokoso ndi kulira chifukwa chiyani? Mwanayu sanamwalire koma ali mtulo.” 40Koma anamuseka Iye.

Atawatulutsa onse panja, Iye anatenga abambo ndi amayi ake a mwanayo ndi ophunzira omwe anali naye, ndipo analowa mʼmene munali mwanayo. 41Anagwira dzanja lake nanena kwa iye, “Talita Kumi!” (Kutanthauza kuti, “Mtsikana, ndikunena ndi iwe, imirira!”) 42Nthawi yomweyo anayimirira nayenda mozungulira (anali wa zaka khumi ndi ziwiri). Pa ichi onse anadabwa kwambiri. 43Anawalamulira kwambiri kuti asawuze wina aliyense za ichi, ndipo anawawuza kuti amupatse kanthu koti adye.