阿摩司书 8 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

阿摩司书 8:1-14

审判之日将临

1主耶和华让我看见了异象,我看到一篮夏天的果子。 2耶和华问我:“阿摩司,你看见什么?”我说:“我看见一篮夏天的果子。”祂说:“我以色列子民的结局8:2 结局”希伯来文中与“夏天的果子”发音相近。到了,我不会再饶恕他们。 3到那日,殿里的歌声要变成哀号;尸横遍地,一片死寂。这是主耶和华说的。”

4践踏贫民、灭绝穷人的人啊,

你们要听!

5你们盼望朔日8:5 朔日”即每月初一。和安息日快点过去,

你们好售卖谷物。

你们用小升斗卖粮,

用加重的砝码收银子,

用假秤骗人。

6你们用银子买贫民,

以一双鞋买穷人为奴,

售卖掺了糠秕的麦子。

7耶和华凭以色列的荣耀起誓:

“我决不会忘记你们的所作所为。

8这片土地要因此而震动,

那里的人都要悲哀。

大地要像尼罗河一样涨起,如埃及的河流翻腾退落。”

9主耶和华说:

“到那日,我要使太阳中午落下,

使白昼变为黑暗。

10我要使你们的节期变为丧礼,

叫你们的欢歌变为哀歌。

我要使你们都腰束麻布,剃光头发;

我要使你们伤心欲绝,如丧独生子;

我要使那日成为痛苦的日子。”

11主耶和华说:

“日子将到,我要使饥荒降在地上。

人饥饿非因无饼,干渴非因无水,

而是因为听不到耶和华的话。

12人们从南到北,从东到西8:12 从南到北,从东到西”希伯来文是“从这海到那海,从北到东”。海指西面的地中海和南面的死海。

在境内四处流荡,

要寻找耶和华的话却找不到。

13“到那日,

“美丽少女和青春少男都要因干渴而昏倒;

14那些凭撒玛利亚别示巴的神明起誓的,

都要跌倒,永不再起来。”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Amosi 8:1-14

Dengu la Zipatso Zakupsa

1Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: dengu la zipatso zakupsa. 2Iye anandifunsa kuti, “Amosi nʼchiyani ukuona?”

Ine ndinayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.”

Ndipo Yehova anati kwa ine, “Nthawi yachimaliziro yawakwanira anthu anga Aisraeli; sindidzawakhululukiranso.

3“Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akulengeza kuti, “Nyimbo za mʼNyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira kofuwula. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzayiponya ponseponse! Kudzangoti zii!”

4Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa

ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu.

5Mumanena kuti,

“Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti

kuti tigulitse zinthu?

Ndipo tsiku la Sabata litha liti

kuti tigulitse tirigu,

kuti tichepetse miyeso,

kukweza mitengo

kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo,

6tigule osauka ndi ndalama zasiliva

ndi osowa powapatsa nsapato,

tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?”

7Yehova amene Yakobo amamunyadira, walumbira kuti: Ine sindidzayiwala chilichonse chimene anachita.

8“Kodi dziko silidzagwedezeka chifukwa cha zimenezi,

ndi onse okhala mʼmenemo kulira mwachisoni?

Dziko lonse lidzavunduka ngati mtsinje wa Nailo;

lidzagwedezeka kenaka nʼkukhala bata

ngati mtsinje wa ku Igupto.

9“Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akunena kuti,

“Ndidzadetsa dzuwa masana

ndi kugwetsa mdima pa dziko lapansi dzuwa likuswa mtengo.

10Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni

ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro.

Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu

ndi kumeta mipala mitu yanu.

Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo,

ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake.

11“Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti,

“Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse;

osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi,

koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.

12Anthu azidzangoyendayenda kuchoka ku nyanja ina kupita ku nyanja ina.

Azidzangoyendayenda kuchoka kumpoto kupita kummawa,

kufunafuna mawu a Yehova,

koma sadzawapeza.

13“Tsiku limenelo

“anamwali okongola ndi anyamata amphamvu

adzakomoka ndi ludzu.

14Onse amene amalumbira pa tchimo la Samariya,

kapena kumanena kuti, ‘Iwe Dani, pali mulungu wako wamoyo,’

kapena, ‘Pali mulungu wamoyo wa ku Beeriseba.’

Iwowo adzagwa

ndipo sadzadzukanso.”